Levitiko 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 4:1-35

Nsembe Yopepesera Tchimo

1Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 2“Awuze Aisraeli kuti, ‘Munthu akachimwa mosadziwa ndi kuchita chilichonse chimene Yehova walamula kuti asachite, azichita izi:

3“ ‘Ngati wansembe wodzozedwa achimwa, ndi kuchimwitsa anthu onse, iyeyu ayenera kupereka mwana wangʼombe wamphongo wopanda chilema chifukwa cha tchimo limene wachitalo. Imeneyi ndi nsembe ya Yehova yopepesera tchimo lake. 4Wansembeyo abwere nayo ngʼombeyo pa khomo la tenti ya msonkhano pamaso pa Yehova. Asanjike dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo ndipo ayiphe pamaso pa Yehova. 5Kenaka wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano. 6Iye aviyike chala chake mʼmagazi, ndipo awawaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani yotchinga malo wopatulika. 7Kenaka wansembe apake magaziwo pa nyanga za guwa lofukizira lubani limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. 8Pambuyo pake achotse mafuta onse a ngʼombe yayimuna yopepesera machimoyo: mafuta okuta zamʼkati kapena mafuta onse amʼkatimo. 9Achotsenso ndi kubwera ndi impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta onse ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi ndi impsyo 10monga momwe amachotsera mafuta a ngʼombe yoperekedwa kuti ikhale chopereka chachiyanjano. Tsono wansembe atenthe zimenezi pa guwa lansembe zopsereza. 11Koma chikopa cha ngʼombe yayimunayo ndi mnofu wake wonse, pamodzi ndi mutu ndi miyendo, zamʼkati ndi matumbo, 12kapena kuti ngʼombe yonse yotsalayo apite nayo kunja kwa msasa ku malo woyeretsedwa, kumene amatayako phulusa ndi kuyitentha pa nkhuni, pa phulusapo.

13“ ‘Ngati gulu lonse la Aisraeli lichimwa mosadziwa, nachita chomwe ndi choletsedwa ndi Yehova, ngakhale kuti gulu lonselo silikudziwa kuti lachimwa, anthuwo ndi olakwa ndithu. 14Akazindikira tchimo limene achita, gulu lonse lipereke mwana wangʼombe wamphongo kuti akhale chopereka chopepesera tchimo ndipo abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. 15Akuluakulu a anthuwo asanjike manja awo pa mutu pa ngʼombe pamaso pa Yehova, ndipo ayiphe pomwepo pamaso pa Yehova. 16Tsono wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano. 17Aviyike chala chake mʼmagaziwo ndi kuwawaza pamaso pa Yehova kasanu ndi kawiri patsogolo pa nsalu yotchinga. 18Pambuyo pake iye apake magaziwo pa nyanga za guwa limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. 19Kenaka achotse mafuta onse a ngʼombeyo ndi kuwatentha pa guwa, 20ndipo achite ndi ngʼombe yayimunayi monga anachitira ndi ngʼombe yayimuna yopepesera machimo. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera anthu, ndipo machimo awo adzakhululukidwa. 21Kenaka atulutse ngʼombeyo kunja kwa msasa ndi kuyitentha monga anatenthera ngʼombe yoyamba ija. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo a gulu lonse.

22“ ‘Ngati mtsogoleri achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova Mulungu wake, ndiye kuti wapalamula. 23Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, iye abwere ndi mbuzi yayimuna yopanda chilema kuti ikhale chopereka chake. 24Asanjike dzanja lake pa mutu wa mbuziyo ndi kuyiphera pamalo pamene amaphera zopereka zopsereza pamaso pa Yehova. Ichi ndi chopereka chopepesera tchimo. 25Pambuyo pake wansembe atengeko magazi a chopereka chopepesera tchimocho ndi chala chake, ndipo awapake pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Athire magazi otsalawo pa tsinde la guwalo. 26Wansembeyo atenthe mafuta onse pa guwapo monga amatenthera chopereka chachiyanjano. Pochita zimenezi, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo, ndipo adzakhululukidwa.

27“ ‘Ngati munthu wamba achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova, ndiye kuti wapalamula. 28Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, abweretse mbuzi yayikazi yopanda chilema kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo. 29Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo ayiphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza. 30Ndipo wansembe atenge magazi ndi chala chake ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza ndi kuthira magazi wotsalawo pa tsinde la guwalo. 31Kenaka iye achotse mafuta onse monga momwe anachotsera mafuta a chopereka chachiyanjano, ndipo awatenthe pa guwa kuti akhale fungo lokomera Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo ndipo adzakhululukidwa.

32“ ‘Ngati munthu apereka mwana wankhosa ngati chopereka chopepesera tchimo lake, abwere ndi mwana wankhosa wamkazi wopanda chilema. 33Asanjike dzanja lake pa mutu wa mwana wankhosayo ndipo amuphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza. 34Kenaka wansembe atengeko ndi chala chake magazi a mwana wankhosa uja ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Magazi otsalawo athire pa tsinde la guwalo. 35Iye achotse mafuta onse, monga amachotsera mafuta a mwana wankhosa wa chopereka chachiyanjano, ndipo wansembe awatenthe pa guwa pamodzi ndi zopereka zina zopsereza za Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo limene munthuyo anachita ndipo adzakhululukidwa.