Levitiko 3 – CCL & OL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 3:1-17

Nsembe Yachiyanjano

1“ ‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, ndipo choperekacho nʼkukhala ngʼombe yayimuna kapena yayikazi, ikhale yopanda chilema. 2Munthuyo asanjike dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo, ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ansembe, ana a Aaroni, awaze magazi mbali zonse za guwalo. 3Pa nsembe yachiyanjanopo, ayenera kupatula zamʼkati mwa nyamayo ndi mafuta onse amene amakuta zamʼkati kupereka nsembe ya chakudya kwa Yehova. 4Apatulenso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake omwe ndiponso mafuta okuta chiwindi amene achotsedwa pamodzi ndi impsyo zija. 5Ndipo ana a Aaroni atenthe zimenezi pa guwa, pamwamba pa chopereka chopsereza chimene chili pa nkhuni zoyakazo. Imeneyi ndi nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Yehova.

6“ ‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, choperekacho chikhale nkhosa yayimuna kapena yayikazi yopanda chilema. 7Ngati apereka nsembe ya mwana wankhosa, abwere naye pamaso pa Yehova. 8Asanjike dzanja lake pamutu pa nkhosayo ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ana a Aaroni awaze magaziwo mbali zonse za guwalo. 9Pa nsembe yachiyanjanopo ayenera kuchotsa ndi kubweretsa: mafuta a nkhosayo, mchira wake wonse wonona atawudulira mʼtsinde pafupi ndi fupa la msana, zamʼkati zonse ndi mafuta onse amene akuta ziwalo zamʼkatimo, 10impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta amene akuta impsyozo, msonga ya chiwindi imene idzachotsedwere limodzi ndi impsyozo. 11Wansembe awotche zonsezi pa guwa. Ichi ndi chakudya chotentha pa moto choperekedwa kwa Yehova.

12“ ‘Ngati munthuyo apereka mbuzi ngati nsembe, abwere nayo kwa Yehova. 13Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ana a Aaroni awaze magazi ake mbali zonse za guwa. 14Tsono pa nsembe yoti iwotchedwe kukhala nsembe chakudya ya Yehova, achotse ndi kubweretsa: mafuta onse amene amaphimba zamʼkati kapena mafuta onse a mʼkatimo, 15impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta onse omwe akuta impsyozo ndi msonga ya chiwindi imene adzachotsera pamodzi ndi impsyo zija. 16Wansembe awotche zonsezi pa guwa. Ichi ndi chakudya cha Yehova, chowotcha pa moto ndiponso cha fungo lokomera Yehova. Mafuta onse ndi a Yehova.

17“ ‘Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse kuti musadzadye mafuta kapena magazi kulikonse kumene mudzakhale.’ ”

O Livro

Levítico 3:1-17

Sacrifício de gratidão

1Se o vosso sacrifício for oferta de paz ao Senhor, podem oferecer tanto um boi como uma vaca, mas deverá ser sem defeito algum, para poder ser oferecido ao Senhor. 2O homem que o trouxer porá a mão sobre a cabeça do animal e matá-lo-á à porta da tenda do encontro. Os filhos de Aarão, os sacerdotes, derramarão o sangue sobre os lados do altar 3e queimarão perante o Senhor a gordura que cobre os órgãos internos, 4os dois rins com a gordura que os cobre e que está perto dos lombos, e a vesícula biliar, que ele removerá junto com os rins. 5Os descendentes de Aarão queimarão tudo isso em cima do holocausto que está sobre a lenha acesa no altar. É um holocausto, oferta queimada, com que o Senhor se agrada.

6Se a vossa oferta de paz ao Senhor for antes gado miúdo, não deverá ter defeito algum, e tanto pode ser um macho como uma fêmea. 7Se for um cordeiro, apresentá-lo-á ao Senhor; 8o homem que o trouxer por-lhe-á a mão na cabeça e matá-lo-á à entrada da tenda do encontro. Os sacerdotes derramarão parte do sangue dele à volta do altar, 9-11e oferecerão sobre o altar a gordura, a cauda, cortada rente ao espinhaço, a gordura que cobre as partes internas, os dois rins com a sua gordura e a vesícula biliar, como oferta queimada ao Senhor.

12Se for um cabrito a oferecer ao Senhor, 13por-lhe-á a mão na cabeça e matá-lo-á à entrada da tenda do encontro. Os sacerdotes aspergirão o seu sangue sobre os lados do altar, 14e neste oferecerão, como oferta queimada para o Senhor, a gordura que cobre os órgãos internos, 15os dois rins com a gordura que os cobre e que está perto dos lombos, e a vesícula biliar, que ele removerá junto com os rins. 16O sacerdote queimá-los-á no altar como alimento, como oferta preparada no fogo. É uma oferta queimada com que o Senhor se agrada. Toda a gordura é do Senhor.

17Aliás, isto é uma lei válida para sempre, para todos os vossos descendentes, onde quer que vivam: não comerão nem gordura nem sangue.”