Levitiko 19 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 19:1-37

Malamulo Osiyanasiyana

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Khalani oyera mtima chifukwa Ine, Yehova Mulungu wanu, ndine Woyera.

3“ ‘Aliyense mwa inu azilemekeza abambo ake ndi amayi ake. Ndipo muzisunga masabata anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

4“ ‘Musatembenukire ku mafano kapena kudzipangira nokha milungu ya zitsulo zosungunula. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

5“ ‘Pamene mukupereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, muyipereke mwanjira yoti ilandiridwe. 6Nsembe izidyedwa tsiku lomwe mwayiperekalo kapena mmawa mwake. Chilichonse chotsala mpaka tsiku lachitatu chiyenera kutenthedwa. 7Ngati mudya choperekacho tsiku lachitatu, ndiye kuti mwachita chonyansa ndipo chakudyacho sichidzalandiridwa. 8Munthu aliyense amene adya chakudyacho adzasenza machimo ake chifukwa wayipitsa chinthu chimene ndi choyera kwa Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.

9“ ‘Pamene mukolola zinthu mʼmunda mwanu musakolole mpaka mʼmphepete mwa munda, ndipo musatole khunkha lake. 10Musakolole mphesa zonse mʼmunda wanu wa mpesa kapena kutola mphesa zakugwa mʼmundamo. Zimenezi muzisiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wako.

11“ ‘Musabe.

“ ‘Musamanamizane.

“ ‘Musachitirane zinthu mwachinyengo.

12“ ‘Musalumbire mʼdzina langa monyenga popeza kutero ndi kuyipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.

13“ ‘Musapsinje mnzanu kapena kumulanda zinthu zake.

“ ‘Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka mmawa.

14“ ‘Musatemberere wosamva kapena kuyikira munthu wosaona chinthu choti apunthwe nacho patsogolo pake, koma muziopa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.

15“ ‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musachite tsankho pakati pa osauka ndi olemera, koma muweruze mlandu wa mnzanu mwachilungamo.

16“ ‘Musamapite uku ndi uku kunena bodza pakati pa anthu anu.

“ ‘Musachite kanthu kalikonse kamene kangadzetse imfa kwa mnzanu. Ine ndine Yehova.

17“ ‘Musamude mʼbale wanu mu mtima mwanu. Koma mudzudzuleni mnzanu moona mtima kuti musakhale wolakwa.

18“ ‘Musamubwezere mnzanu choyipa kapena kumusungira kanthu kunkhosi, koma konda mnansi wako monga iwe mwini. Ine ndine Yehova.

19“ ‘Muzisunga malangizo anga.

“ ‘Tsono musamalole kuti ngʼombe zanu zikwerane ndi chiweto cha mtundu wina.

“ ‘Ndiponso musamadzale mbewu za mitundu iwiri mʼmunda umodzi.

“ ‘Musavale chovala chopangidwa ndi nsalu za mitundu iwiri.

20“ ‘Ngati munthu agonana ndi kapolo wamkazi amene wafunsidwa mbeta ndi munthu wina, koma sanawomboledwe kapenanso kulandira ufulu wake, alangidwe. Koma onsewa asaphedwe, chifukwa mkaziyo anali asanalandire ufulu wake. 21Koma mwamunayo abwere ndi nsembe yopepesera kupalamula kwa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Nsembe yake ikhale nkhosa yayimuna 22ndipo wansembe achite nayo mwambo wopepesera chifukwa cha kupalamula kumene anachita pamaso pa Yehova. Akatero tchimo lake lidzakhululukidwa.

23“ ‘Mukadzalowa mʼdzikomo ndi kudzala mtengo wa mtundu uliwonse wa zipatso, zipatso zakezo mudzaziyese ngati zodetsedwa. Ndiye kuti kwa zaka zitatu zidzakhale zoletsedwa kwa inu. Musadzazidye nthawi imeneyi. 24Chaka chachinayi, zipatso zake zonse zidzakhala zopatulika, ndipo zidzakhala chopereka cha matamando kwa Yehova. 25Koma chaka chachisanu, mudzatha kudya zipatso zake kuti mitengoyo idzakubalireni zochuluka. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

26“ ‘Musadye nyama ya magazi.

“ ‘Musamawombeze kapena kuchita zamatsenga.

27“ ‘Musamamete mduliro kapena kumeta mʼmphepete mwa ndevu zanu.

28“ ‘Musadzichekecheke pathupi panu chifukwa cha munthu wakufa kapena kudzitema mphini pa thupi lanu. Ine ndine Yehova.

29“ ‘Musamuyipitse mwana wanu wamkazi pomusandutsa mkazi wachiwerewere. Mukatero dziko lidzasanduka la anthu achiwerewere ndi lodzaza ndi zoyipa.

30“ ‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga opatulika. Ine ndine Yehova.

31“ ‘Musamapite kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa owombeza. Musamawafunefune kuti angakuyipitseni. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

32“ ‘Muzikhala mwa ulemu pamaso pa munthu wachikulire, ndipo muzichitira ulemu munthu wokalamba. Kumeneko ndiye kuopa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.

33“ ‘Pamene mlendo akhala nanu mʼdziko mwanu, musamuzunze. 34Mlendo amene akhala nanu akhale ngati mmodzi mwa mbadwa zanu. Mumukonde monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Paja inu munali alendo mʼdziko la Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

35“ ‘Musamachite za chinyengo poweruza mlandu, kapena poyeza utali, kulemera ngakhalenso kuchuluka kwa zinthu. 36Miyeso ya sikelo, miyeso yoyezera kulemera kwa zinthu, miyeso yotchedwa efa ndi miyeso yotchedwa hini zikhale zolungama. Ine ndine Yehova, Mulungu wanu amene ndinakutulutsani ku dziko la Igupto.

37“ ‘Choncho muzisunga malangizo ndi malamulo angawa ndi kuwatsatira. Ine ndine Yehova.’ ”

Het Boek

Leviticus 19:1-37

Wees heilig, want Ik ben heilig

1De Here droeg Mozes op ook de volgende woorden aan de Israëlieten over te brengen. 2‘U moet heilig zijn, want Ik, de Here, uw God, ben heilig. 3U moet uw vader en moeder eren en mijn sabbatswet gehoorzamen, want Ik ben de Here, uw God. 4Maak geen afgodsbeelden en aanbid ze niet, want Ik ben de Here, uw God. 5Wanneer u de Here een vredeoffer brengt, doe het zoals is voorgeschreven, zodat het wordt aanvaard. 6Eet het dezelfde dag dat u het offert of uiterlijk de volgende dag, wat overblijft tot de derde dag moet worden verbrand. 7Want als iets ervan op de derde dag wordt gegeten, zal Mij dat met afkeer vervullen en Ik zal het niet aanvaarden. 8Als u het op de derde dag eet, zult u schuldig zijn, want u schendt daarmee de heiligheid van de Here en u zult worden verstoten uit het volk van de Here.

9Wanneer u de oogst binnenhaalt, moet u de randen van het veld niet helemaal afmaaien en wat op de grond is gevallen, moet u naderhand niet bijeenrapen. 10Hetzelfde geldt voor de wijnoogst, haal niet alle druiven van de planten en laat wat op de grond is gevallen, gewoon liggen. Laat het liggen voor de armen en voor hongerige reizigers, want Ik ben de Here, uw God.

11U mag niet stelen, liegen of elkaar bedriegen. 12Zweer geen valse eed, want daarmee ontheiligt u de naam van uw God, want Ik ben de Here. 13U mag niet roven of iemand iets afpersen en u moet de arbeiders die u hebt gehuurd, op tijd betalen. Als u een van hen nog loon schuldig bent, laat er dan niet nog een nacht overheen gaan voordat u hem uitbetaalt. 14U mag niet vloeken tegen een dove. U mag een blinde niets in de weg leggen. Heb ontzag voor uw God, Ik ben de Here! 15Rechters moeten bij hun uitspraken altijd rechtvaardig blijven en zich niet laten leiden door het feit of iemand rijk of arm is, zij moeten altijd strikt rechtvaardig zijn. 16Roddel niet. Doe niets dat het leven van uw naaste in gevaar brengt, want Ik ben de Here. 17U mag uw broeder niet haten. Vermaan ieder die zondigt, want als u er niets van zegt, bent u even schuldig als hij. 18Wees niet haatdragend of wraakzuchtig, maar heb uw naaste net zo lief als uzelf, want Ik ben de Here. 19Gehoorzaam mijn wetten: laat van uw vee niet verschillende soorten met elkaar paren, zaai uw land niet in met twee verschillende soorten zaad, draag geen kleren van twee soorten stof.

20Als een man een slavin verleidt die aan een andere man als vrouw is gegeven, hoewel zij niet is vrijgekocht, moeten zij beiden door de rechter worden gestraft. Maar zij zullen niet worden gedood, want zij was nog niet vrij. 21De betrokken man zal een ram als zijn schuldoffer voor de Here brengen bij de ingang van de tabernakel. 22De priester zal met de ram verzoening doen voor de begane zonde en het zal de zondaar worden vergeven.

23Wanneer u het land binnenkomt en allerlei vruchtbomen plant, zult u de eerste drie oogsten niet binnenhalen, want die zijn onrein. 24In het vierde jaar zal de hele oogst tot lof van de Here zijn geheiligd. 25In het vijfde jaar mag u de oogst eten en gebruiken, zo krijgt u een grotere opbrengst.

26Ik ben de Here, uw God! U mag geen vlees eten waarin nog bloed zit, u mag zich niet bezighouden met waarzeggerij en toverij. 27U mag, als teken van rouw om een dode, uw hoofdhaar niet rond laten afknippen, uw baardhaar niet aan de zijden afscheren, 28niet in uw lichaam snijden en geen tatoeëringen op uw huid aanbrengen—Ik ben de Here. 29Ontheilig uw dochter niet door haar te laten prostitueren, anders zal het land worden vervuld met schanddaden. 30Handhaaf mijn sabbatswetten en eerbiedig mijn tabernakel, want Ik ben de Here. 31Geef u niet af met geesten of mensen die de geesten van doden kunnen raadplegen, want Ik ben de Here, uw God. 32Eer en respecteer de ouderen, in ontzag voor God, Ik ben de Here. 33Vreemdelingen in uw land mag u niet onderdrukken of uitbuiten. 34Zij moeten worden behandeld als iedere andere burger, houd van hen als van uzelf. Vergeet niet dat ook u zelf als vreemdelingen in Egypte hebt gewoond. Ik ben de Here, uw God. 35-36 Wees onpartijdig in de rechtspraak. Gebruik de juiste maten voor lengte, gewicht en inhoud en geef altijd de volledige hoeveelheden. Want Ik ben de Here, uw God, die u uit Egypte heeft bevrijd. 37Al mijn regels en verordeningen moet u nauwgezet naleven, Ik ben de Here.’