Levitiko 16 – CCL & KLB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 16:1-34

Tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo

1Atafa ana awiri a Aaroni amene anaphedwa atapita pamaso pa Yehova mosayenera, Yehova anayankhula ndi Mose. 2Yehova anawuza Mose kuti, “Uza mchimwene wako Aaroni kuti asamalowe ku Malo Wopatulika, kuseri kwa katani, pamaso pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano nthawi iliyonse imene akufuna kuopa kuti angadzafe, pakuti Ine ndimaoneka mu mtambo umene uli pamwamba pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano.

3“Aaroni azilowa Malo Wopatulika Kwambiri motere: azitenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. 4Azivala mwinjiro wopatulika wa nsalu yosalala, azivalanso kabudula wa mʼkati wa nsalu yosalala, azimanga lamba wa nsalu yosalala, ndipo avalenso nduwira ya nsalu yosalala kumutu. Zimenezi ndi nsalu zopatulika ndipo atasamba thupi lonse azivala zimenezi. 5Kuchokera pa gulu la Aisraeli, Aaroni azitenga mbuzi zazimuna ziwiri kuti zikhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza.

6“Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale yopepesera machimo a iye mwini kuti achite mwambo wopepesera machimo ake pamodzi ndi a banja lake. 7Kenaka atenge mbuzi ziwiri zija ndipo aziyimike pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. 8Aaroni ndiye achite maere pa mbuzi ziwirizo kuti imodzi ikhale ya Yehova, ndipo inayo ikhale ya Azazele. 9Aaroni abwere ndi mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Yehova, ndipo apereke kuti ikhale nsembe yopereka chifukwa cha tchimo. 10Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi yosenza machimo, apereke ya moyo pamaso pa Yehova, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo poyitumiza ku chipululu kuti ikhale ya Azazele.

11“Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ake. Ndiye achite mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake pamodzi ndi banja lake. Pambuyo pake aphe ngʼombe yopepesera machimo ake aja. 12Kenaka iye atenge chofukizira chodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Yehova. Atengenso lubani wonunkhira ndi woperapera wokwanira manja awiri, ndipo alowe naye kuseri kwa katani. 13Athire lubani pa moto pamaso pa Yehova kuti utsi wa lubaniyo uphimbe chivundikiro chimene chili pamwamba pa Bokosi la Chipangano, kuti Aaroniyo asafe. 14Ndipo atenge magazi ena a ngʼombeyo, awawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha kummawa; kenaka awaze magaziwo ndi chala chake kasanu ndi kawiri patsogolo pa chivundikirocho.

15“Kenaka Aaroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu, ndipo magazi ake alowe nawo kuseri kwa katani ndi kuchita chimodzimodzi monga anachitira ndi magazi a ngʼombe aja: Aaroni awaze magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho. 16Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika chifukwa cha kudetsedwa ndi kuwukira kwa Aisraeli pa machimo ena aliwonse amene achita. Achite chimodzimodzi ndi tenti ya msonkhano imenenso ili yodetsedwa chifukwa cha machimo awo. 17Mu tenti ya msonkhano musakhale munthu ndi mmodzi yemwe nthawi imene Aaroni akupita kukachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika mpaka atatulukako. Musakhale munthu mu tenti ya msonkhano mpaka atachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake, banja lake ndi gulu lonse la Aisraeli.

18“Kenaka, Aaroniyo akatuluka apite ku guwa limene lili pamaso pa Yehova ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ngʼombe yayimuna ndiponso magazi a mbuzi ndi kuwapaka pa nyanga zonse za guwa lansembe. 19Magazi ena awawaze pa guwalo ndi chala chake kasanu ndi kawiri kuliyeretsa ndi kulipatula kuchotsa zodetsa za Aisraeli.

20“Aaroni akatsiriza mwambo wopepesera Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa, azibwera ndi mbuzi yamoyo kudzayipereka nsembe. 21Aaroni asanjike manja ake pa mutu wa mbuziyo ndipo awulule pa mbuziyo zoyipa zonse ndi zowukira zonse za Aisraeli, kutanthauza machimo awo onse. Machimowo awayike pa mutu wa mbuziyo. Kenaka munthu amene anasankhidwa athamangitsire mbuziyo ku chipululu. 22Mbuziyo isenze machimo awo onse ndi kupita nawo kutali ndipo munthuyo aleke mbuziyo kuti ipite ku chipululuko.

23“Pambuyo pake Aaroni alowe mu tenti ya msonkhano ndi kuvula zovala zosalala zija zimene anavala polowa ku Malo Wopatulika ndi kuzisiya komweko. 24Asambe thupi lonse ku Malo Wopatulika ndi kuvala zovala zake za nthawi zonse. Kenaka atuluke ndi kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake ndi a anthu. 25Mafuta a nyama yopepesera machimo awatenthe pa guwa lansembe.

26“Tsono munthu amene anaperekeza mbuzi yosenza machimo ija achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe ku msasa. 27Ngʼombe ndi mbuzi zoperekera nsembe yopepesera machimo zimene magazi ake anabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera Malo Wopatulika, azitulutsire kunja kwa msasa. Koma zikopa zake, nyama yake ndi matumbo ake azitenthe. 28Munthu amene azitenthe achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe mu msasa.

29“Ili likhale lamulo lanu lamuyaya: Mwezi wachisanu ndi chiwiri, pa tsiku la khumi la mwezi, mugonje pamaso pa Yehova. Musamagwire ntchito iliyonse, kaya ndinu mbadwa kapena mlendo amene akukhala pakati panu, 30chifukwa tsiku limeneli kudzachitika mwambo wopepesera machimo anu, kukuyeretsani kuti mukhale oyeretsedwa ku machimo anu pamaso pa Yehova. 31Limeneli ndi tsiku lanu la Sabata lopumula, ndipo muzigonja pamaso pa Yehova. Limeneli ndi lamulo lanu la muyaya. 32Wansembe amene wadzozedwa ndi kupatulidwa kuti akhale wansembe kulowa mʼmalo mwa abambo ake ndiye azichita mwambo wopepesera machimo atavala zovala zake zosalala ndi zopatulika. 33Adzachite mwambo wopepesera machimo Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Adzachitenso mwambo wopepesera anzake ndi gulu lonse la anthu.

34“Ili likhale lamulo lanu lamuyaya. Mwambo wopepesera machimo uzichitika kamodzi pa chaka chifukwa cha machimo a anthu onse.”

Ndipo Mose anachita monga momwe Yehova analamulira.

Korean Living Bible

레위기 16:1-34

속죄일

1아론의 두 아들이 여호와 앞에서 죽은 일이 있은 후에 여호와께서 모세 에게 말씀하셨다.

2“너는 네 형 아론에게 경고하여 성소의 휘장 뒤 법궤와 그 법궤의 뚜껑인 속죄소가 있는 지성소에 함부로 들어오지 못하도록 하라. 그렇지 않으면 죽음을 당할 것이다. 이것은 내가 그 속죄소 위 구름 가운데서 나타나기 때문이다.

3“아론이 지성소에 들어오려고 할 때 먼저 갖추어야 할 조건은 이렇다: 그는 속죄제물로 수송아지 한 마리와 번제물로 숫양 한 마리를 가져와야 하며

4지성소에 들어오기 전에 먼저 목욕을 하고 고운 모시로 만든 겉옷과 속옷과 띠와 관을 착용해야 한다.

5그리고 이스라엘 백성이 속죄제물로 숫염소 두 마리와 번제물로 숫양 한 마리를 가져오면

6아론은 먼저 자기를 위해 속죄제물로 수송아지를 드려 자기와 자기 가족의 죄를 속한 다음

7그 숫염소 두 마리는 성막 입구나 여호와 앞에 두고

8거기서 제비 뽑아 나 여호와에게 제물로 바칠 염소와 16:8 또는 ‘아사셀 양’광야로 보낼 염소를 결정해야 한다.

9그런 다음 그는 나 여호와에게 바칠 제물로 제비 뽑힌 염소는 속죄제로 드리고

10남아 있는 다른 염소는 나 여호와 앞에 산 채로 두었다가 그것으로 속죄한 다음에 희생의 염소로 광야에 내보내도록 하라.

11“아론은 수송아지를 속죄제로 드려 자기와 자기 가족의 죄를 속한 다음

12향로를 가져다가 나 여호와의 단에서 피운 숯불을 가득 채우고 또 두 움큼의 고운 가루향을 가지고 지성소로 들어가

13나 여호와 앞에서 분향하여 그 향의 연기가 법궤 위의 속죄소를 덮어 가리도록 해야 한다. 그러면 그가 죽지 않을 것이다.

14또 그는 수송아지 피를 조금 가져다가 손가락으로 찍어 속죄소 동편에 뿌린 다음 그 피를 속죄소 앞에 일곱 번 뿌려야 한다.

15“그러고서 아론은 성소 밖으로 나가서 백성의 죄를 속할 속죄제 염소를 잡아 그 피를 가지고 지성소로 다시 들어와서 수송아지 피를 뿌릴 때와 같이 속죄소 위와 앞에 그것을 뿌려야 한다.

16이런 방법으로 그는 이스라엘 백성의 부정과 죄로 더럽혀진 지성소를 정결하게 하고 또 그들의 부정으로 둘러싸인 야영지 가운데 있는 성막을 위해서도 그렇게 해야 한다.

17아론이 지성소에 들어가서 자기와 자기 가족과 이스라엘 백성을 위해 속죄제를 드리고 나올 때까지는 한 사람도 성막 안에 있어서는 안 된다.

18-19아론은 지성소를 정결하게 한 다음에 번제단 앞으로 나와서 수송아지 피와 염소의 피를 가지고 단 네 뿔에 바르고 또 손가락으로 그 피를 찍어 단 위에 일곱 번 뿌려서 이스라엘 백성의 죄와 부정으로 더럽혀진 그 단을 정결하게 하여 거룩하게 해야 한다.”

속죄의 염소

20“아론은 지성소와 성막 전체와 단을 정결하게 한 다음에 산 염소를 끌어다가

21그 머리에 두 손을 얹어 이스라엘 백성의 모든 죄를 고백하고 그 죄를 염소의 머리에 지운 다음 지정된 사람에게 맡겨 그 염소를 광야로 보내야 한다.

22그 염소가 이스라엘 백성의 모든 죄를 지고 사람이 살지 않는 광야에 이르거든 그 염소를 놓아 주어라.

23“그런 후에 아론은 성막으로 다시 들어가서 지성소에 들어갈 때 입었던 고운 모시 옷을 벗어 거기에 두고

24거룩한 곳에서 목욕을 한 다음 자기 옷으로 갈아 입고 나와서 자기와 백성을 위해 각각 번제를 드려 자기 죄와 백성의 죄를 속하고

25속죄제물로 잡은 짐승의 기름은 단에서 불로 태워야 한다.

26“그리고 16:26 또는 ‘염소를 아사셀에게 보낸 자’희생의 염소를 끌고 가서 광야로 보낸 자는 옷을 빨고 목욕을 한 후에 야영지로 들어오게 하라.

27또 죄를 속하기 위해 속죄제물로 드려진 수송아지와 염소의 피는 지성소에서 죄를 속하는 데 사용되었으므로 그 나머지 부분인 가죽과 고기와 내장을 야영지 밖으로 내어다가 불사를 것이며

28그것을 불사른 자도 옷을 빨고 목욕을 한 다음에 야영지 안으로 들어와야 한다.”

속죄일에 관한 규정

29“그리고 너희가 대대로 지켜야 할 규정은 이렇다: 7월 10일에는 아무 일도 하지 말고 16:29 또는 ‘스스로 괴롭게 하고’자기를 살피면서 경건한 마음으로 보내야 한다. 이것은 이스라엘 사람뿐만 아니라 그들 가운데 사는 외국인들도 지켜야 할 규정이다.

30이 날은 속죄 의식을 베풀어 나 여호와 앞에서 너희 모든 죄를 씻어 너희를 정결하게 하는 날이며

31또 너희가 쉬어야 할 거룩한 안식일이다. 그러므로 너희는 자기를 살피면서 경건하게 이 날을 보내야 한다. 너희는 이 규정을 대대로 지켜라.

32자기 아버지를 계승하여 기름 부음을 받고 위임된 대제사장은 거룩한 고운 모시 옷을 입고

33지성소와 전체 성막과 단과 제사장들과 백성을 위해 속죄 의식을 베풀어야 한다.

34이것은 너희가 영원히 지켜야 할 규정이다. 속죄 의식은 이스라엘 백성의 모든 죄를 위해 일 년에 한 번씩 베풀어야 한다.” 그래서 아론은 여호와께서 모세에게 명령하신 그대로 하였다.