Levitiko 13 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 13:1-59

Malamulo a Nthenda za pa Khungu Zopatsirana

1Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 2“Munthu akakhala ndi chithupsa, kapena mʼbuko, kapena chikanga pa thupi lake chimene chitha kusanduka nthenda ya khate, abwere naye munthuyo kwa Aaroni wansembe kapena kwa mmodzi mwa ana ake amene ndi ansembe. 3Tsono wansembe ayangʼanitsitse nthendayo pa khungupo, ndipo ngati ubweya wa pamalo pamene pali nthendapo wasanduka woyera, komanso kuti nthendayo yazama mʼkati kupitirira khungu, ndiye kuti nthendayo ndi khate. Wansembe akamuonetsetsa alengeze kuti ndi wodetsedwa. 4Ngati chikanga cha pa khungulo chikuoneka choyera, ndipo kuya kwake sikukuonekera kuti kwapitirira khungu ndi ubweya wake pamalopo sunasanduke woyera, wansembe amuyike wodwalayo padera kwa masiku asanu ndi awiri. 5Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso bwino wodwalayo. Ndipo ngati waona kuti nthendayo sinasinthe ndipo sinafalikire pa khungu, amuyikenso wodwalayo padera kwa masiku ena asanu ndi awiri. 6Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembeyo amuonenso bwino munthuyo, ndipo ngati nthendayo yazima ndi kusafalikira pa khungu, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi woyera. Umenewo unali mʼbuko chabe. Choncho munthuyo achape zovala zake ndipo adzakhala woyera. 7Koma ngati mʼbukowo ufalikira pakhungu atakadzionetsa kale kwa wansembe ndipo wansembeyo nʼkulengeza kuti munthuyo ndi woyeretsedwa, ndiye kuti apitenso kukadzionetsa kwa wansembeyo. 8Wansembe amuonetsetsenso munthuyo, ndipo ngati mʼbukowo wafalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa ndi kuti nthendayo ndi khate.

9“Ngati munthu aliyense ali ndi nthenda ya pakhungu yoyipitsa thupi, wodwalayo abwere naye kwa wansembe. 10Wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati ali ndi chithupsa chamaonekedwe woyera pa khungupo chimene chasandutsa ubweya wa pamalopo kukhala woyera, ndipo ngati pali zilonda pa chotupacho, 11limenelo ndi khate lachikhalire la pa khungu, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Asamutsekere munthu woteroyo pakuti ndi wodetsedwa kale.

12“Ndipo ngati, mʼkuona kwa wansembe, khate lija lafalikira pa khungu lonse moti lamugwira thupi lonse kuyambira kumutu mpaka kumapazi, 13wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati khatero lagwira thupi lake lonse, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Popeza kuti thupi lonse lasanduka loyera, munthuyo ndi woyeretsedwa. 14Koma pa tsiku limene zilonda zidzaoneka pa iye, munthuyo adzakhala wodetsedwa. 15Wansembe aonetsetse zilondazo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zilondazo ndi zodetsedwa ndipo ili ndi khate. 16Koma zilondazo zikasinthika ndi kusanduka zoyera, munthuyo ayenera kupita kwa wansembe. 17Wansembe amuonetsetse ndipo ngati zilondazo zasanduka zoyera, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woyera ndipo adzakhala woyera ndithu.

18“Ngati pa khungu la munthu wodwalayo pali chithupsa chimene chinapola kale, 19ndipo pamalo pamene panali chithupsacho pakatuluka chotupa choyera kapena banga loyera mofiirira, munthuyo ayenera kukadzionetsa kwa wansembe. 20Wansembe aonetsetse bwino ndipo ngati chikuoneka kuti chazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka woyera, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate imene yatuluka mʼchithupsacho. 21Koma ngati wansembe waonetsetsa napeza kuti palibe ubweya woyera ndipo chithupsacho sichinazame, koma chazimirira, wansembeyo amuyike padera wodwalayo kwa masiku asanu ndi awiri. 22Ngati nthendayo ikufalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limeneli ndi khate. 23Koma bangalo likakhala malo amodzi, wosafalikira, chimenecho ndi chipsera cha chithupsacho, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera.

24“Munthu akakhala ndi bala lamoto pa khungu lake, ndipo chilonda cha balalo chikasanduka banga loyera mofiirira kapena loyera, 25wansembe aonetsetse bangalo, ndipo ngati ubweya wa pa bangapo usanduka woyera, ndipo balalo lioneka kuti ndi lozama, limenelo ndi khate lomwe latuluka pa balalo. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate la pa khungu. 26Koma ngati wansembe waonetsetsa balalo ndipo palibe ubweya woyera, ndipo ngati balalo silinazame ndi kuti lazirala, wansembe amuyike padera wodwalayo kwa masiku asanu ndi awiri. 27Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso wodwalayo, ndipo ngati bangalo lafalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate. 28Koma ngati bangalo likhala pa malo amodzi wosafalikira pa khungu, ndipo lazimirira, limenelo ndi thuza la bala lamoto, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Chimenecho ndi chipsera chamoto.

29“Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi nthenda kumutu kapena ku chibwano, 30wansembe aonetsetse balalo ndipo likaoneka kuti lazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka wachikasu ndi wonyololoka, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zimenezo ndi mfundu zonyerenyetsa, khate lakumutu kapena ku chibwano. 31Koma wansembe akaonetsetsa mfundu zonyerenyetsazo, ndipo zikaoneka kuti sizinazame ndi kuti palibe ubweya wakuda, wansembe amuyike padera munthuyo kwa masiku asanu ndi awiri. 32Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aonetsetsenso mfundu zonyerenyetsazo, ndipo ngati sizinafalikire ndipo palibe ubweya wachikasu pamalopo ndiponso sizinazame, 33wodwalayo ametedwe, koma pamene pali mfunduyo pasametedwe. Wansembe amuyike padera munthuyo kwa masiku enanso asanu ndi awiri. 34Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aonetsetsenso mfundu zonyerenyetsazo ndipo ngati sizinafalikire pa khungu ndi kuti sizinazame, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Tsono achape zovala zake, ndipo adzakhala woyera. 35Koma mfundu zonyerenyetsazo zikafalikira pa khungu, wansembe atalengeza kuti ndi woyera, 36wansembe amuonetsetsenso wodwalayo ndipo ngati mfunduzo zafalikira pa khungu, iye asalabadirenso zoyangʼana ngati ubweya uli wachikasu. Munthuyo ndi wodetsedwa. 37Koma ngati wansembe waonetsetsa kuti mfunduzo sizinasinthe ndipo ubweya wakuda wamera pa mfundupo, ndiye kuti wodwalayo wachira. Tsono wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa.

38“Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi mawanga woyera pa khungu, 39wansembe aonetsetse mawangawo, ndipo ngati ali otuwa, ndiye kuti ndi mibuko chabe yotuluka pa khungu. Munthuyo ndi woyera.

40“Tsitsi la munthu likayoyoka kumutu ndiye kuti ndi dazi limenelo koma munthuyo ndi woyeretsedwa. 41Ngati tsitsi lake layoyoka chapamphumi ndiye kuti ndi dazi la pa chipumi limenelo koma munthuyo ndi woyera. 42Koma ngati pa dazi la pamutu kapena la pa chipumi pakhala chithupsa choyera mofiirira, ndiye kuti ndi khate limenelo lochokera mu dazi la pamutu lija kapena pa chipumi lija. 43Tsono wansembe amuonetsetse wodwalayo ndipo ngati chithupsa cha pa dazi lapankhongo kapena pa dazi lapachipumicho ndi choyera mofiirira monga nthenda ya khate imaonekera, 44ndiye kuti munthuyo ali ndi khate, motero ndi wodetsedwa. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa chifukwa cha chithupsa cha pamutu pakepo.

45“Munthu wa khate lotere avale sanza, tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wapamwamba ndipo azifuwula kuti, ‘Ndine wodetsedwa, ndine wodetsedwa!’ 46Munthu wodwalayo adzakhala wodetsedwa kwa nthawi yonse imene ali ndi nthendayo. Iye ayenera kumakhala payekha kunja kwa msasa.

Malamulo a Nguwi ya pa Zovala

47“Nsalu iliyonse ikakhala ndi nguwi, 48kaya ndi chovala chopangidwa ndi nsalu yathonje kapena yaubweya, yoluka ndi thonje kapena ubweya, yachikopa kapena yopangidwa ndi chikopa, 49ndipo ngati pamalo pamene pachita nguwiyo pali ndi maonekedwe obiriwira kapena ofiirira imeneyo ndi nguwi yoyipitsa chovala ndipo chovalacho chikaonetsedwe kwa wansembe. 50Wansembeyo ayionetsetse nguwiyo ndipo chovalacho achiyike padera kwa masiku asanu ndi awiri. 51Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ayionetsetsenso nguwiyo ndipo ngati nguwiyo yafalikira pa chovalacho, chathonje kapena chaubweya, kapena pa chikopacho, kaya ndi cha ntchito ya mtundu wanji, imeneyo ndi nguwi yoopsa ndipo chovalacho ndi chodetsedwa. 52Wansembe atenthe chovala chathonje kapena chaubweya chija, ngakhalenso chinthu chachikopa chija popeza nguwiyo yachidetsa. Nguwiyo ndi yoopsa choncho chinthucho achitenthe.

53“Koma ngati wansembe akayangʼanitsitsa nguwiyo apeza kuti sinafalikire pa chovalacho kapena pa chinthu chilichonse chachikopa, 54iye alamulire kuti chinthu choyipitsidwacho achichape. Akatero achiyike padera kwa masiku enanso asanu ndi awiri. 55Chovalacho chitachapidwa, wansembe achionenso ndipo ngati nguwiyo sinasinthe maonekedwe ake, ngakhale kuti sinafalikire, chovalacho ndi chodetsedwa ndithu. Muchitenthe, ngakhale kuti nguwiyo ili kumbuyo kapena kumaso kwa chinthucho. 56Koma ngati wansembe aonetsetsa nʼkupeza kuti nguwi ija yathimbirira pa chovala chija kapena pa chinthu chachikopa chija atachichapa, ndiye angʼambeko chinthucho pa banga la nguwiyo. 57Koma ngati nguwiyo iwonekanso pa chovala chathonje kapena chaubweya ndiye kuti nguwiyo ikufalikira. Chilichonse chimene chili ndi nguwi chiyenera kutenthedwa. 58Chovala chathonje kapena chaubweya, ngakhale chinthu china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, mukachichapa nguwi yake nʼkuchoka muchichapenso kawiri ndipo chidzakhala choyeretsedwa.”

59Amenewa ndiwo malamulo a nguwi yokhala pa chovala chaubweya kapena pa chovala chathonje, kapenanso pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa kuti muzitha kulekanitsa choyeretsedwa ndi chodetsedwa.

Het Boek

Leviticus 13:1-59

Wetten betreffende melaatsheid

1Opnieuw sprak de Here tegen Mozes en Aäron: 2‘Als iemand een zwelling, een uitslag of een lichte plek op zijn huid ziet, kan dat een begin van melaatsheid zijn. Hij moet naar de priester worden gebracht, naar Aäron of een van zijn nakomelingen. 3De priester zal de huidaandoening nader onderzoeken. Als het haar op de plek wit geworden is en het blijkt dat de plek dieper zit dan de huid, is het melaatsheid. Als de priester dat constateert, zal hij hem melaats en onrein verklaren. 4Maar als de plek niet dieper blijkt te zitten dan de huid en het haar erop is niet wit geworden, zal de priester hem zeven dagen in afzondering houden. 5Daarna zal de priester hem opnieuw onderzoeken. Als dan blijkt dat de plek hetzelfde is gebleven en zich niet over de huid heeft uitgebreid, zal de priester hem nog eens zeven dagen in afzondering houden. 6Op de zevende dag zal de priester hem opnieuw onderzoeken. Als dan blijkt dat de plek is weggetrokken en zich niet over de huid heeft uitgebreid, zal de priester hem rein en genezen verklaren, het gaat dan om gewone huiduitslag. Hij zal zijn kleren wassen en rein zijn. 7Maar als de uitslag zich wel over de huid heeft uitgebreid na het derde onderzoek, moet hij zich nog een keer door de priester laten onderzoeken. 8Als de priester bij dat onderzoek constateert dat de uitslag zich over de huid heeft uitgebreid, zal hij hem onrein verklaren, dan is het melaatsheid.

9-11Als iemand de verschijnselen van melaatsheid vertoont, moet hij bij de priester worden gebracht. Als de priester hem onderzoekt en er is een witte zwelling op de huid aanwezig die het haar wit heeft gemaakt of als er wild vlees in de zwelling groeit, is het een duidelijk geval van melaatsheid. De priester zal hem dan niet in afzondering ter observatie houden, want hij is al onrein.

12-13 Maar als de priester ziet dat de melaatsheid is doorgebroken en de hele huid van top tot teen bedekt, zal hij hem rein verklaren, want dan is hij genezen. 14-15 Maar als er wild vlees groeit, moet hij melaats en onrein worden verklaard. Het wilde vlees is het kenmerk van de ziekte. 16-17 Mocht het wilde vlees verdwijnen en de huid wit worden, dan moet hij weer naar de priester gaan. Die zal hem onderzoeken en als blijkt dat hij wit is geworden, zal hij hem rein verklaren. Dan is hij genezen.

18-19 Als iemand een zweer op zijn lichaam heeft gehad die weer is genezen, maar die een witte zwelling of een roodachtig witte plek heeft achtergelaten, moet hij voor onderzoek naar de priester gaan. 20Als de priester bij zijn onderzoek constateert dat het haar op de huid wit is geworden en de zwelling onderhuids zit, zal de priester hem onrein en melaats verklaren. De melaatsheid is dan op de plaats van de zweer uitgebroken. 21Als de priester echter constateert dat het haar op de huid niet wit is en de zwelling niet meer onder de huid zit, maar weggetrokken is, zal hij hem zeven dagen in afzondering houden. 22Als de plek zich na zeven dagen verder over de huid heeft uitgebreid, zal de priester hem melaats en onrein verklaren. 23Maar als de lichte plek op dezelfde plaats is gebleven en zich niet heeft uitgebreid, is dat het litteken van de zweer en zal de priester hem rein en genezen verklaren. 24-25 Als iemand een brandwond heeft opgelopen en het vlees van de wond is roodachtig wit of helemaal wit, moet de priester de wond onderzoeken. Als het haar wit is geworden en het zit onderhuids, is het melaatsheid die in de brandwond is uitgebroken en de priester zal hem melaats en onrein verklaren. 26Maar als de priester de plek onderzoekt en deze is oppervlakkig en er blijkt geen wit haar op te zitten, zal de priester hem zeven dagen in afzondering houden. 27Op de zevende dag zal de priester hem opnieuw onderzoeken. Als de plek zich verder over de huid heeft uitgebreid, zal de priester hem melaats en onrein verklaren. 28Als de lichte plek echter hetzelfde is gebleven en zich niet over de huid heeft verspreid maar is afgenomen, is het de zwelling van de brandwond. De priester zal hem genezen verklaren, want het is het litteken van de brandwond.

29-30 Als een man of een vrouw een zere plek op het hoofd of op de kin heeft, moet de priester die plek onderzoeken. Als de plek onderhuids zit en er zit dun, geel haar op, zal de priester hem onrein verklaren, het is dan melaatsheid van het hoofd of de kin. 31Als de priester echter constateert dat de aangetaste plek niet onderhuids zit en er zich geen zwart haar op bevindt, moet hij de man of de vrouw zeven dagen in afzondering houden. 32-33 Na die zeven dagen moet hij de plek opnieuw onderzoeken en als dan blijkt dat de plek zich niet heeft uitgebreid en er geen geel haar op zit en de plek niet onderhuids zit, moet hij zich scheren zonder de uitslag aan te raken. De priester zal hem daarna weer zeven dagen in afzondering houden. 34Op de zevende dag moet hij hem weer onderzoeken en als dan blijkt dat de plek zich niet heeft uitgebreid en niet onderhuids zit, zal de priester hem genezen verklaren en hij zal zijn kleren wassen en rein zijn. 35-36 Maar als de plek zich later toch weer uitbreidt, zal de priester hem weer onderzoeken en zonder af te wachten of er geel haar groeit, zal de priester hem onrein verklaren, want hij is dan melaats. 37Maar als de plek even groot is gebleven en er zwart haar op groeit, is hij genezen en niet melaats. De priester zal hem rein verklaren. 38Als een man of een vrouw witte blaren op de huid heeft, moeten zij dit aan de priester laten zien. 39Als de priester ziet dat deze plekken slinken, is het geen melaatsheid, maar een gewone huidinfectie. 40Als een man zijn haar op zijn kruin verliest, wordt hij gewoon kaal en is hij niet onrein. 41Als zijn hoofdhaar van voren uitvalt, wordt hij daar gewoon kaal en is hij niet onrein. 42-44Maar als op de kale kruin of op het kale voorhoofd een roodachtige witte zwelling aanwezig is, is hij daar melaats en moet de priester hem onrein verklaren.

45Ieder bij wie melaatsheid is geconstateerd, moet zijn kleren scheuren, blootshoofds lopen en zijn bovenlip bedekken. Overal waar hij loopt, moet hij roepen: “Melaats, melaats!” 46Zolang de ziekte duurt, is hij onrein en moet hij buiten het kamp blijven.

47-48 Als het vermoeden bestaat dat in een linnen of wollen kleed of weefsel, in een stuk leer of een leren voorwerp melaatsheid zit en de aangetaste plek is groenachtig of roodachtig, 49kan het melaatsheid zijn en moet het voorwerp voor onderzoek naar de priester worden gebracht. 50De priester zal het voorwerp zeven dagen in afzondering houden. 51Op de zevende dag zal hij het voorwerp opnieuw onderzoeken. 52Als de plek zich heeft uitgebreid, is het een besmettelijke melaatsheid en moet het wollen, linnen of leren voorwerp worden verbrand, want het is onrein. 53-54 Maar als bij het tweede onderzoek blijkt dat de plek zich niet heeft uitgebreid, zal de priester opdracht geven het verdachte voorwerp te wassen en het daarna nog eens zeven dagen in afzondering te houden. 55Als na die zeven dagen de plek niet van kleur is veranderd, al heeft ze zich niet uitgebreid, dan is het melaatsheid en moet het voorwerp worden verbrand, want het is dan door en door geïnfecteerd. 56Als de priester echter constateert dat de plek na het wassen minder is geworden, moet hij de plek uit de stof of uit het leer wegsnijden. 57Als daarna opnieuw plekken verschijnen op het voorwerp, is het zeker melaatsheid en moet het worden verbrand. 58Maar als na het wassen verder niets gebeurt, mag het voorwerp na een tweede wasbeurt weer worden gebruikt.

59Dit zijn de voorschriften betreffende melaatsheid in een weefsel of in een voorwerp van leer, zodat iedereen weet wanneer het rein of onrein is.’