Levitiko 11 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 11:1-47

Chakudya Choyeretsedwa ndi Chodetsedwa

1Yehova anayankhula ndi Mose ndi Aaroni kuti, 2“Awuze Aisraeli kuti, ‘Nyama zomwe mukhoza kudya mwa nyama zonse za dziko lapansi ndi izi: 3Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya.

4“ ‘Koma pali nyama zina zimene zimabzikula kokha kapena ndi zogawikana zipondero zimene simukuyenera kudya. Nyama zimenezi ndi ngamira, ngakhale imabzikula ilibe zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 5Ina ndi mbira, ngakhale imabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 6Inanso ndi kalulu, ngakhale amabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi wodetsedwa, musadye. 7Nkhumba simabzikula ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 8Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa chifukwa ndi yodetsedwa.

9“ ‘Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi a mʼnyanja ndi a mʼmitsinje mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba. 10Koma zamoyo zonse za mʼnyanja kapena za mʼmitsinje zimene zilibe minga ya pa msana ndi mamba, kaya ndi tizirombo tonse ta mʼmadzi ndi zamoyo zonse zopezeka mʼmenemo ndi zodetsedwa kwa inu. 11Pakuti zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu, nyama yake musadye, ndipo zikafa zikhalebe zodetsedwa kwa inu. 12Chamoyo chilichonse cha mʼmadzi chimene chilibe minga ya pa msana kapena mamba ndi chodetsedwa kwa inu.

13“ ‘Mbalame zimene simukuyenera kudya chifukwa ndi zodetsedwa ndi izi: mphungu, nkhwazi, mwimba, 14nankapakapa, akamtema a mitundu yonse, 15akhungubwi a mitundu yonse, 16kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo ndi mtundu uliwonse wa akabawi 17kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi, 18tsekwe, vuwo, dembo, 19indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.

20“ ‘Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa. 21Komabe mwa zowuluka zokhala ndi miyendo inayi zimene mukhoza kudya ndi zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira. 22Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse. 23Koma za mapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inayi muzitenge kukhala zodetsedwa kwa inu.

24“ ‘Zimenezi zidzakudetsani. Aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 25Aliyense wonyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

26“ ‘Nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogawikana koma mapazi ake wosagawikana, kapena imene sibzikula muyiyese yodetsedwa kwa inu ndipo munthu aliyense akakhudza nyama yakufayo, adzakhala wodetsedwa. 27Mwa nyama zonse zoyenda ndi miyendo inayi, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo kuphazi muzitenge kukhala zodetsedwa ndipo aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 28Aliyense wonyamula nyamazi zitafa ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu.

29“ ‘Mwa nyama zokwawa, zimene zili zodetsedwa kwa inu ndi izi: likongwe, mbewa, msambulu za mitundu yonse, 30gondwa, mngʼazi, buluzi, dududu ndi nanzikambe. 31Mwa nyama zonse zoyenda pansi, zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu. Munthu aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 32Iliyonse mwa nyama zimenezi ikafa ndi kugwera pa chiwiya chilichonse, kaya chimagwira ntchito yotani, kaya ndi chopangidwa ndi mtengo, kaya ndi cha nsalu, kaya ndi cha chikopa kapena chiguduli chiwiyacho chidzakhala chodetsedwa. Muchiviyike mʼmadzi chiwiyacho komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo, ndipo kenaka chidzakhala choyeretsedwa. 33Tsono nyama ina iliyonse mwa zimenezi ikagwera mʼmbiya ya dothi, ndiye kuti chilichonse cha mʼmbiyamo chidzakhala chodetsedwa, ndipo muyenera kuswa mbiyayo. 34Chakudya chilichonse chimene mungadye chikakhala kuti chathiridwa mʼmbiyamo, ndiye kuti chakudyacho chidzakhala chodetsedwa, ndipo madzi akumwa wochokera mʼmbiya zotere ndi wodetsedwa. 35Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse kaya pa uvuni, kapena pa mʼphika, ndiye kuti zinthuzo zidzakhala zodetsedwa, ndipo ziphwanyidwe popeza ndi zodetsedwa. 36Koma kasupe kapena chitsime chamadzi chidzakhala choyeretsedwa ngakhale kuti chilichonse chokhudza nyama yakufayo chidzakhala chodetsedwa. Zimenezi muzitenge kukhala zodetsedwa. 37Chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo chikagwera pa mbewu zimene akuti adzale, mbewu zimenezo zidzakhalabe zabwino. 38Koma mbewuzo zikakhala zonyowa ndi madzi, ndipo chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo chikagwera pa mbewuzo, mbewuzo zikhale zodetsedwa kwa inu.

39“ ‘Ngati nyama imene mumaloledwa kudya yafa yokha, ndiye kuti aliyense wokhudza nyama yakufayo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 40Aliyense amene adyako nyama yakufayo achape zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Aliyense amene wanyamula nyama yakufayo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

41“ ‘Chinthu chilichonse chokwawa pansi ndi chonyansa, simuyenera kudya. 42Musadye chilichonse chokwawa pansi, choyenda chamimba kapena choyenda ndi miyendo inayi kapenanso yambiri popeza ndi chodetsedwa. 43Musadzisandutse nokha odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. Musadziyipitse nazo, kuti mukhale odetsedwa. 44Ine ndine Yehova Mulungu wanu, choncho dziyeretseni kuti mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera. Musadzisandutse odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. 45Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani ku Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera.

46“ ‘Amenewa ndi malamulo onena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda mʼmadzi ndiponso chamoyo chilichonse chokwawa. 47Muzisiyanitsa pakati pa chodetsedwa ndi choyeretsedwa, komanso pakati pa zomwe mutha kudya ndi zomwe simuyenera kudya.’ ”

Het Boek

Leviticus 11:1-47

Reine en onreine dieren

1Toen zei de Here tegen Mozes en Aäron: 2-3 ‘Zeg tegen het volk Israël dat ze alle dieren die gespleten hoeven hebben en hun voedsel herkauwen, mogen eten.

4-7Dat houdt in dat de volgende dieren niet mogen worden gegeten: de kameel (hij herkauwt wel, maar heeft geen gespleten hoeven), de klipdas (deze herkauwt ook, maar heeft evenmin gespleten hoeven), de haas (die herkauwt ook, maar heeft ook geen gespleten hoeven), het zwijn (deze heeft wel gespleten hoeven, maar herkauwt niet). Al deze dieren moet u als onrein beschouwen. 8Niemand mag hun vlees eten of hun kadavers aanraken, zij zijn verboden voedsel.

9Wat vis betreft, mag alles worden gegeten wat vinnen en schubben heeft. Het maakt niet uit of ze in de rivier of in zee zijn gevangen. 10Maar alle andere waterdieren zijn streng verboden voor u. 11Niemand mag hun vlees eten en hun kadavers moet u als weerzinwekkend beschouwen. 12Ik herhaal: elk waterdier dat geen vinnen of schubben heeft, is voor u verboden voedsel.

13-19Wat de vogels betreft, zijn dit de soorten die niet mogen worden gegeten: de arend, de lammergier, de zee-arend, de wouw en alle soorten gieren, alle soorten raven, de struisvogel, de kat-uil, de meeuw en alle soorten sperwers, de steenuil, de aalscholver en de oehoe, de witte uil, de pelikaan, de aasgier en de ooievaar, alle soorten reigers, de hop en de vleermuis.

20-22Vliegende insecten met vier poten mogen niet worden gegeten, met uitzondering van hen die springen: dus wel alle soorten sprinkhanen, treksprinkhanen, veldsprinkhanen en kleine treksprinkhanen. 23Alle andere vliegende insecten met vier poten mogen absoluut niet worden gegeten. 24-25 Ieder die hun dode lichamen aanraakt, is tot de avond onrein en moet onmiddellijk zijn kleren wassen. Tot de avond blijft hij onrein.

26Onrein wordt ook ieder die in aanraking komt met dieren die wel gespleten, maar geen geheel doorkloofde hoeven hebben of die niet herkauwen. 27Zoolgangers mogen niet worden gegeten. 28Ieder die hun kadaver aanraakt, zal tot de avond onrein zijn. Hij die het kadaver ook nog oppakt, moet direct zijn kleren wassen en blijft onrein tot de avond. Deze dieren zijn voor iedereen verboden.

29-30 Dit zijn de onreine soorten van de dieren die over de grond kruipen: de mol, de muis en alle soorten padden, de egel, de varaan, de hagedis, de slak en het kameleon. 31Ieder die hun dode lichamen aanraakt, zal tot de avond onrein zijn. 32Elk voorwerp waarop dat dode lichaam valt, elk houten of stoffen voorwerp, elk vel en elke zak, alles wat ermee in aanraking komt, moet in het water worden gelegd en zal tot de avond onrein zijn. Daarna mag het weer worden gebruikt. 33Als zoʼn dier in een stenen pot valt, is de inhoud onrein en moet die pot worden stukgeslagen. 34Als het water waarmee het onreine voorwerp is afgewassen, in aanraking komt met voedsel, is dat ook allemaal onrein. Elke drank die in de onreine pot zit, zal ook onrein zijn. 35Als het lichaam van zoʼn dier in aanraking komt met een stenen oven, is deze onrein en moet worden afgebroken. 36Als het lichaam in een bron valt of in een volle waterbak, is dat water niet onrein. Degene die het lichaam er uit haalt, is echter wel onrein. 37Als het dode lichaam in aanraking komt met zaaizaad, zal dat niet onrein zijn. 38Maar als het zaad vochtig is en het lichaam komt er mee in aanraking, dan is het zaad wel onrein. 39Als een dier dat mag worden gegeten, dood gevonden wordt, is ieder die het kadaver aanraakt tot de avond onrein. 40Degene die het vlees eet of het kadaver aanraakt, moet zijn kleren wassen en is onrein tot de avond.

41Kruipende dieren mogen niet worden gegeten. 42Daartoe behoren de reptielen die zich op hun buik voortbewegen en de kruipende dieren met poten. Geen enkel kruipend dier met vier of meer poten mag worden gegeten, want het is onrein. 43Verontreinig uzelf niet met deze dieren, opdat u niet onrein wordt. 44Ik ben de Here, uw God. Heilig u en wees heilig, want Ik ben heilig, daarom moet u óók heilig zijn en mag u zich niet verontreinigen met een van deze kruipende dieren. 45Want Ik ben de Here, die u uit Egypte heeft geleid om uw God te zijn. Daarom moet u heilig zijn, omdat Ik heilig ben. 46Dit zijn de wetten aangaande het vee, de vogels, de waterdieren en de dieren die over de grond kruipen. 47Deze wetten maken het onderscheid duidelijk tussen rein en onrein, tussen wat wel en wat niet mag worden gegeten.’