Ezekieli 45 – CCL & KLB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 45:1-25

Magawidwe a Dziko

1“ ‘Mukamadzagawa dziko kuti fuko lililonse lilandire cholowa chake, mudzapatuleko chigawo chimodzi kuti chikhale cha Yehova. Mulitali mwake mudzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita khumi. Malo onsewo adzakhale opatulika. 2Mʼkati mwa chigawo chimenechi, malo a mamita 250 mbali iliyonse adzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. Pozungulira pake ponse padzakhala malo a mamita 25. 3Mʼchigawo chopatulikacho muyeze malo a makilomita 12 ndi theka mulitali mwake, makilomita asanu mulifupi mwake. Pamenepo padzakhala malo opatulika kwambiri. 4Malo opatulika amenewa adzakhalanso a ansembe amene amatumikira ku malo opatulika, amene amayandikira Yehova kuti amutumikire. Pamenepo padzakhala malo omangapo nyumba zawo ndi malo omangapo Nyumba ya Mulungu. 5Alevi otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzakhala ndi malo a makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake ndi makilomita asanu mulifupi mwake. Kumeneko ndiko kudzakhale midzi yawo.

6“ ‘Moyandikana ndi malo opatulika, padzakhale malo a makilomita awiri ndi theka mulifupi mwake ndi makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake; kuti akhale malo a mzinda. Malo amenewa adzakhala a Aisraeli onse.

7“ ‘Mfumu idzakhale ndi malo okhudzana ndi chigawo cha malo opatulika ndi cha mzinda. Malowo ayandikane ndi zigawozo chakummawa ndi chakumadzulo. Malowo atalike ngati chigawo chimodzi cha fuko la Israeli kuyambira ku malire akummawa mpaka ku malire akumadzulo. 8Malowa adzakhala chigawo cha mfumu mu Israeli. Choncho mafumu anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzidzalola Aisraeli kuti akhale ndi zigawo zawozawo.

9“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsono pakwana, inu akalonga a Israeli. Lekani nkhanza zanu ndi kupondereza anthu anga. Muzitsata chilungamo ndi kuchita zokomera anthu. Musapirikitse anthu anga mʼdzikomo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 10Miyeso yanu yoyezera zinthu monga efa ndi bati zizikhala zokhulupirika. 11Efa ndi bati ikhale miyeso yolingana kukula kwake. Muyeso wa homeri ukhale wokwanira mabati khumi, ukhalenso wokwanira maefa khumi. Ndiye kuti kukula kwa miyeso iwiriyo kuzidzatsata kukula kwa homeriyo. 12Muyeso wa sekeli ukhale wokwanira magera makumi awiri. Muyeso wa mina ukhale wolemera masekeli 60.

Zopereka ndi Masiku Achikondwerero

13“ ‘Zopereka zomwe mudzidzapereka ndi izi: chimodzi mwa zigawo 60 za tirigu, barelenso chimodzimodzi ndiponso gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa barele wa homeri. 14Gawo loyenera la mafuta, loyezedwa ndi bati, ndiponso chigawo mwa zigawo 100 za mafuta. Miyeso yake ili motere: mabati khumi afanana ndi homeri imodzi kapena kori imodzi. 15Muperekenso nkhosa imodzi pa gulu lankhosa 200 za pa msipu wabwino wa mu Israeli. Izi zidzagwiritsidwa ntchito monga nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano ndi nsembe zopepesera milandu ya anthu. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 16Anthu onse a mʼdzikomo azidzapereka zimenezi kwa mfumu ya Israeli. 17Udzakhala udindo wa mfumu kupereka zofunikira ku nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, ndi nsembe za zakumwa pa nthawi ya zikondwerero, chikondwerero cha mwezi watsopano ndi cha masabata, nthawi yonse ya zikondwerero zoyikika za Aisraeli. Mfumuyo idzapereka nsembe zopepesera machimo, nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano kuti zikhale nsembe zopepesera machimo a Aisraeli.

18“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba muzitenga mwana wangʼombe wamwamuna wopanda chilema ndi kuchita mwambo woyeretsa malo opatulika. 19Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera machimoyo ndipo awapake pa mphuthu za Nyumba ya Mulungu, pa ngodya zinayi za pamwamba pa guwa lansembe ndi pa mphuthu za pa chipata cha bwalo la mʼkati. 20Muzichita chimodzimodzi pa tsiku la chisanu ndi chiwiri la mwezi, kuchitira aliyense amene wachimwa mosafuna kapena mosadziwa. Motero Nyumba ya Mulungu idzakhala yoyera.

21“ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita chikondwerero cha Paska, chikondwerero chake cha masiku asanu ndi awiri. Pa masiku amenewo muzidzadya buledi wopanda yisiti. 22Pa tsiku loyamba la chikondwererocho, mfumu ipereke nsembe ya ngʼombe yayimuna monga nsembe yopepesera machimo ake ndi machimo a anthu onse a mʼdziko. 23Pa masiku asanu ndi awiri a chikondwererocho, mfumu ipereke kwa Yehova nsembe zopsereza izi: ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, zonsezi zopanda chilema. Pa masikuwa mfumu iziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo. 24Pamodzi ndi ngʼombe iliyonse yayimuna ndi nkhosa iliyonse yayimuna, mfumu ipereke chopereka cha chakudya chokwanira efa imodzi ndiponso mafuta okwanira hini imodzi pa efa iliyonse.

25“ ‘Pa nthawi ya chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri, chimene chimayamba pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mfumuyo iziperekanso nsembe za mtundu womwewo: nsembe zopepesera machimo, nsembe zopsereza, nsembe za chakudya ndi za mafuta.’ ”

Korean Living Bible

에스겔 45:1-25

거룩하게 구별한 땅

1“너희가 땅을 분배할 때에는 한 구역을 거룩하게 구별하여 나 여호와 에게 바쳐라. 그 땅은 길이가 13.1킬로미터이며 폭이 45:1 또는 10,000규빗, 곧 5.3킬로미터10.5킬로미터이다. 그 구역 전체가 거룩한 땅이 될 것이다.

2그 중에서도 성소에 속할 땅은 가로 세로 262.5미터의 정사각형 땅이며 그 땅 26.3미터 폭의 사방 둘레는 빈터가 되게 하라.

3그 구별한 땅 중에서 길이 13.1킬로미터와 폭 5.3킬로미터를 측량하여 그 구역 내에 성전을 세워라.

4그 땅은 거룩한 곳으로 성소에서 나를 섬기는 제사장들이 사용할 것이며 제사장들의 집과 성전을 짓는 터가 될 것이다.

5그리고 그 나머지 땅인 길이 13.1킬로미터와 폭 5.3킬로미터의 땅은 성전에서 섬기는 레위 사람들의 소유로 주어 그들이 사는 부락이 되게 하라.

6“그리고 거룩하게 구별한 땅과 인접한 폭 2.6킬로미터와 길이 13.1킬로미터의 땅은 이스라엘 백성이 누구든지 살 수 있는 성의 기지로 삼아라.

7“거룩하게 구별된 땅과 성의 기지 양쪽 옆으로 인접해 있는 땅은 왕이 차지할 땅이다. 그것은 서쪽으로 서쪽 국경까지 뻗고 동쪽으로는 동쪽 국경까지 뻗어 그 길이가 이스라엘 한 지파에게 분배된 땅의 길이와 같다.

8이 땅이 왕의 소유가 되면 내 왕들이 다시는 내 백성을 억압하지 않을 것이다. 그리고 나머지 땅은 이스라엘 백성에게 지파대로 나누어 주도록 하라.

9“나 여호와가 말한다. 이스라엘의 통치자들아, 너희가 오랫동안 범죄하였다. 너희는 횡포와 탄압을 중단하고 공정하고 옳은 일을 하며 내 백성을 착취하는 일을 버려라. 이것은 나 주 여호와의 말이다.

10“너희는 45:10 또는 ‘공평한 저울과 공평한 에바와 공평한 밧을 쓸지니’정확한 저울과 되를 사용하라.

11마른 것을 되는 에바와 액체를 되는 밧의 용량을 동일하게 하고 그 기준은 호멜로 하라. 한 호멜은 10에바이며 10밧이다.

12그리고 한 세겔은 20게라이고 20세겔과 25세겔과 15세겔을 모두 합한 60세겔이 한 미나이다.”

예물과 명절에 대한 규정

13“너희가 바쳐야 할 예물의 기준은 이렇다. 밀과 보리는 너희 수확의 60분의 을 바치고

14기름은 너희 수확에서 밧으로 되어 100분의 을 바쳐라. 10밧이 한 호멜이며 한 고르이다.

15그리고 이스라엘의 모든 목장에서 양 200마리에 한 마리씩 바쳐라. 이 모든 예물은 백성의 죄가 용서받을 수 있도록 곡식으로 드리는 소제와 불로 태워 바치는 번제와 화해를 위한 화목제물로 사용되어야 할 것이다. 이것은 나 주 여호와의 말이다.

16이 땅에 사는 모든 백성은 이 예물을 이스라엘 왕에게 드려야 하며

17명절과 매월 초하루와 안식일과 이스라엘의 모든 지정된 명절에 번제와 소제와 술을 따르는 전제를 준비하는 것은 왕이 해야 할 일이다. 왕은 또 이스라엘 백성의 죄를 씻기 위해 속죄제와 소제와 번제와 화목제를 준비해야 한다.

18“나 여호와가 말한다. 정월 초하룻날에 너희는 흠 없는 수송아지 한 마리를 가져다가 성소를 정결하게 하라.

19제사장은 속죄제물의 피를 가져다가 성전의 문설주와 제단 밑받침 네 모퉁이와 안뜰로 들어가는 출입문 기둥에 발라야 한다.

20너희는 또 무심결에 범죄하거나 무지해서 범죄한 자를 위해 그 달 7일에도 그렇게 하여 45:20 또는 ‘전을 속죄할지니라’성전을 거룩하게 하라.

21“1월 14일에는 7일 동안 계속되는 유월절을 지키고 이 기간 동안은 누룩 넣지 않은 빵을 먹어라.

22이 명절 45:22 또는 ‘그 날에’첫날에 왕은 자기와 모든 백성을 위해 죄를 씻는 속죄제물로 송아지 한 마리를 준비할 것이며

23그는 또 그 명절 7일 동안에 매일 흠 없는 것으로 수송아지 일곱 마리와 숫양 일곱 마리를 나 여호와에게 바칠 번제물로 준비하고 속죄제물로 매일 숫염소 한 마리를 준비해야 한다.

24또 곡식으로 드리는 소제로는 수송아지 한 마리와 숫양 한 마리에 대해서 각각 밀가루 45:24 히 ‘한 에바’22리터씩 준비하고 밀가루 22리터에 대해서는 기름 45:24 히 ‘한 힌’약 4리터씩 준비해야 한다.

25“7월 15일부터 시작되는 명절 7일 동안에도 왕은 매일 똑같은 것을 준비하여 속죄제와 번제와 소제와 기름을 드릴 수 있도록 하라.”