Ezekieli 39 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 39:1-29

1“Iwe mwana wa munthu, nenera modzudzula Gogi ndi kumuwuza kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa Mesaki ndi Tubala. 2Ine ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira kutsogolo. Ndidzakutenga kuchokera kutali kumpoto ndi kukutumiza kuti ukalimbane ndi anthu a ku mapiri a Israeli. 3Kenaka Ine ndidzathyola uta wa mʼdzanja lako lamanzere ndipo ndidzagwetsa mivi ya mʼdzanja lako lamanja. 4Udzagwa ku mapiri a ku Israeli, iwe ndi magulu ako onse ankhondo ndiponso mitundu ya anthu imene ili nawe. Ndidzakusandutsa chakudya cha mitundu yonse ya mbalame zodya nyama, ndiponso cha zirombo zakuthengo. 5Udzafera pa mtetete kuthengo, pakuti Ine ndayankhula. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 6Ndidzatumiza moto pa Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere mʼmbali mwa nyanja. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’

7“Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Israeli. Sindidzalola kuti dzina langa liyipitsidwenso, ndipo mitundu ya anthu idzadziwa kuti Ine Yehova ndine Woyera mu Israeli. 8Zikubwera! Ndipo zidzachitikadi, ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndiye tsiku limene ndinanena lija.

9“Pamenepo okhala mʼmizinda ya Israeli adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo kuti zikhale nkhuni ndipo adzazitentha; zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga za nkhondo ndi mikondo. Adzazisonkhera moto kwa zaka zisanu ndi ziwiri. 10Iwo sadzatolera nkhuni kuthengo kapena kukadula ku nkhalango, chifukwa adzasonkhera moto zidazo. Ndipo iwo adzafunkha amene anawafunkhawo, ndi kulanda chuma cha amene anawalanda, ndikutero Ine Ambuye Yehova.

11“Pa tsiku limenelo ndidzamupatsa Gogi manda mu Israeli, mʼchigwa cha apaulendo, kummawa kwa Nyanja Yakufa. Mandawo adzatseka njira ya apaulendo, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzayikidwa kumeneko. Ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.

12“Nyumba ya Israeli idzakhala ikukwirira mitembo kwa miyezi isanu ndi iwiri ndi cholinga choyeretsa dziko. 13Anthu onse a mʼdzikomo adzakwirira nawo mitembo. Ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetsa ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

14“Patapita miyezi isanu ndi iwiri adzalemba ntchito anthu ena odzayenda mʼdziko lonse kufunafuna mitembo imene inatsalira nʼkumayikwirira. Choncho adzayeretseratu dzikolo. 15Poyenda mʼdzikomo azidzati akaona fupa la munthu azidzayikapo chizindikiro pambali pake mpaka okumba manda atakalikwirira fupalo ku chigwa cha gulu lankhondo la Gogi. 16(Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu la nkhondo). Ndipo potero adzayeretsa dziko.

17“Tsono iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Itana mbalame za mitundu yonse ndi zirombo zonse zakuthengo ndipo uziwuze kuti, ‘Sonkhanani ndipo bwerani kuchokera ku mbali zonse ku nsembe imene ndikukonzerani inu, nsembe yayikulu pa mapiri a Israeli. Kumeneko inu mudzadya mnofu ndi kumwa magazi. 18Mudzadya mnofu wa anthu ankhondo amphamvu ndi kumwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo anaphedwa ngati nkhosa zazimuna, ana ankhosa onenepa, mbuzi ndiponso ngati ngʼombe zazimuna zonenepa za ku Basani. 19Ku phwando lansembe limene ndikukonzera inulo, mudzadya zonona mpaka kukhuta ndi kumwa magazi mpaka kuledzera. 20Pa tebulo langa mudzakhuta pakudya akavalo ndi okwerapo ake, anthu amphamvu ndi asilikali amitundumitundu,’ ndikutero Ine Ambuye Yehova.

21“Ine ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo adzaona mmene ndidzawalangire ndikadzayika dzanja langa pa iwo. 22Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo Aisraeli adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 23Ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti anthu a Israeli anatengedwa ukapolo chifukwa cha tchimo lawo, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho Ine ndinawabisira nkhope yanga ndi kuwapereka kwa adani awo. Motero anaphedwa pa nkhondo. 24Ndinawachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwawo ndi zolakwa zawo, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.

25“Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsopano ndidzakhazikanso pa bwino banja la Yakobo. Ndidzachitira chifundo Aisraeli onse, ndipo ndidzateteza dzina langa loyera. 26Anthuwo akadzakhala mwamtendere mʼdziko lawo popanda wina wowaopseza, pamenepo adzayiwala zamanyazi zawo zimene zinawachitikira chifukwa chosandikhulupirira Ine. 27Ndidzawabwezeranso kwawo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko a adani awo. Poteropo ndidzaonetsa pamaso pa anthu a mitundu yambiri kuti ndine Woyera. 28Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, ngakhale kuti ndinawapereka ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ine ndidzawasonkhanitsanso ku dziko lawo osasiyako wina mʼmbuyo. 29Ine sindidzawabisiranso nkhope yanga, pakuti ndidzathira Mzimu wanga pa Aisraeli. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以西结书 39:1-29

预言歌革被灭

1“人子啊,你要发预言斥责歌革,告诉他,主耶和华这样说,‘米设土巴的首领歌革啊,我要与你为敌。 2我要把你调转过来,使你从遥远的北方来到以色列的山中。 3我要打掉你左手的弓,击落你右手的箭。 4你和你的军队以及与你同来的各国联军都要倒毙在以色列的山岭上,我要把你们的尸体给各种猛禽野兽作食物。 5你必倒毙在田野之间,因为我已经宣告。这是主耶和华说的。 6我要火烧安居在玛各和海岛的人,他们就知道我是耶和华。

7“‘我要让我的以色列子民知道我的圣名,不再让我的圣名被亵渎。这样列国就知道我是耶和华——以色列的圣者。 8我所说的日子将要来临,一切必然实现。这是主耶和华说的。

9“‘以色列各城邑的居民都要出去捡兵器当柴烧,其中包括大小的盾牌、弓箭、矛枪等,足够用七年。 10他们不必到田间拾柴,或到林中伐木,因为有兵器当燃料。他们要抢夺那些抢夺过他们的人,掳掠那些掳掠过他们的人。这是主耶和华说的。

11“‘那一天我要把以色列境内、通往盐海东边的旅客之谷作为歌革的坟地,埋葬他和他的军队。这坟地将截断行人的去路,因此人称那地方为哈们·歌革谷。 12以色列人要用七个月来埋葬他们,使那地方洁净。 13以色列人都来埋葬他们。我彰显荣耀的那天将是以色列人扬眉吐气的日子。这是主耶和华说的。 14七个月后,他们会派人不断巡视那里,埋葬遗留在地面上的尸体,使那里洁净。 15如果巡视的人发现了骸骨,便在旁边立一个标记,好叫负责埋葬的人将骸骨埋葬在哈们·歌革谷。 16他们要这样使那地方洁净。那里有一座城叫哈摩那39:16 哈摩那”意思是“大群”。。’

17“人子啊,主耶和华说,‘你要召唤各类飞鸟和野兽,让它们聚集起来,从四面八方来赴我为它们预备的祭宴,就是以色列山岭上的大祭宴,在那里吃肉饮血。 18它们将吃到勇士的肉,喝到君王的血,好像吃公绵羊、羊羔、公山羊、公牛这些巴珊的肥畜。 19它们要在我为它们设的祭宴中任意吃肉饮血,直到吃饱喝醉为止。 20它们在我的宴席上要饱餐战马、车夫、勇士和军人的肉。这是主耶和华说的。

21“‘我要在各国中彰显我的荣耀,使他们看见我如何用大能审判歌革22从那天起,以色列必知道我是他们的上帝耶和华。 23列国必知道以色列人被掳走是因为他们犯罪背叛我,以致我掩面不顾他们,把他们交在敌人手中,让他们丧身刀下。 24我照他们的污秽和罪恶报应他们,掩面不顾他们。’

25“因此,主耶和华说,‘我要使雅各被掳的人回到故土,我要怜悯全以色列人,热心维护我的圣名。 26当他们在故土安居,没有人来威胁他们的时候,他们就会忘记自己所有的羞辱和得罪我的恶事。 27我从列国把他们领回,从敌国把他们召回来的时候,我要借着他们向列国彰显我的圣洁。 28我让他们被掳到各国,将来必召集他们返回故土,不撇下一人。这样,他们便知道我是他们的上帝耶和华。 29我不再掩面不顾以色列人,因为我要把我的灵浇灌在他们身上。这是主耶和华说的。’”