Ezekieli 20 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 20:1-49

Kuwukira kwa Israeli

1Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiwiri, ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kudzapempha nzeru kwa Yehova, ndipo anakhala pansi pamaso panga.

2Tsono Yehova anandiyankhula nati: 3“Iwe mwana wa munthu, ayankhule akuluakulu a Israeli ndi kuwawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Kodi mwabwera kudzapempha nzeru kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, Ine sindidzakulolani kupempha nzeru kwa Ine, akutero Ambuye Yehova.’

4“Kodi uwaweruza? Iwe mwana wa munthu, kodi ugamula mlandu wawo? Uwadziwitse tsono zonyansa zimene anachita makolo awo, uwawuze kuti, 5‘Ambuye Yehova akuti: Pa tsiku limene ndinasankha Israeli, ndinalumbira kwa zidzukulu za nyumba ya Yakobo ndipo ndinadziwulula kwa iwo ku Igupto. Ndinalumbira ndi kuwawuza kuti: Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 6Pa tsiku limenelo ndinalumbira kwa iwo kuti ndidzawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kupita nawo ku dziko limene ndinawapezera, dziko la mwana alirenji, dziko lokongola kwambiri kupambana mayiko ena. 7Ndipo ndinawawuza kuti, ‘Aliyense ataye zinthu zonse zonyansa zimene ankasangalala nazo, ndipo musadziyipitse ndi mafano a Igupto, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’

8“ ‘Koma iwo anandiwukira ndipo sanafune kundimvera. Palibe amene anataya zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo. Panalibenso amene anasiya mafano a ku Igupto. Tsono ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwaonetsa mkwiyo wanga mʼdziko la Igupto momwemo. 9Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene ankakhala pakati pawo. Paja ndinali nditaonetsa mphamvu zanga pamaso pa mitunduyo potulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto. 10Choncho ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kubwera nawo mʼchipululu. 11Ndinawapatsa malangizo anga ndi kuwadziwitsa malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. 12Ndinawapatsanso Masabata ngati chizindikiro pakati pathu, kuti adziwe kuti Ine Yehova ndinawapatula.

13“ ‘Komabe anthu a Israeli anandiwukira mʼchipululu. Iwo sanatsatire malangizo anga koma anakana malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. Ndipo anayipitsa kotheratu Masabata anga. Choncho, ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawononga mʼchipululu. 14Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Igupto. 15Ndinalumbiranso kwa iwo mʼchipululu muja, nditakweza dzanja, kuti sindidzawalowetsanso mʼdziko limene ndinawapatsa, dziko la mwana alirenji, lokoma kwambiri kuposa mayiko ena onse. 16Paja anakana malamulo anga, sanatsatire malangizo anga ndipo anayipitsa masabata anga. Mitima yawo inakonda mafano. 17Komabe ndinawamvera chisoni ndipo sindinawawononge kapena kuwatheratu mʼchipululu. 18Tsono kwa ana awo mʼchipululu ndinati, ‘Musatsatire malangizo a makolo anu kapena kusunga malamulo awo kapena kudziyipitsa ndi mafano awo. 19Ine ndine Yehova Mulungu wanu; tsatirani malangizo anga ndipo sungani malamulo anga. 20Masabata anga muziwasunga ngati opatulika kuti akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi inu. Mukatero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’

21“ ‘Koma ana awo anandiwukira. Iwo sanatsatire malangizo anga, sanamvere malamulo anga, ngakhale kuti amapereka moyo kwa munthu amene amawamvera. Ndiponso anayipitsa Masabata anga. Choncho ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawonongeratu mʼchipululu momwemo. 22Koma sindinatero chifukwa cha dzina langa kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Iguptomo. 23Choncho ndinalumbira mʼchipululu, nditakweza dzanja langa, kuti ndidzawabalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwamwazira ku mayiko akutali, 24chifukwa sanamvere malamulo anga, anakana malangizo anga, nayipitsa masabata anga, ndi kupembedza mafano a makolo awo. 25Ine ndinawapatsanso malangizo amene sanali abwino ndi malamulo amene sakanatha kupeza nawo moyo. 26Ndinawalekerera kuti adziyipitse ndi mphatso zawo zomwe, makamaka popereka ana awo oyamba kubadwa ngati nsembe zopsereza. Ndinatero kuti ndiwadetse nkhawa ndi kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.’

27“Tsono iwe mwana wa munthu, yankhula nawo Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti makolo anu anandinyozanso posaonetsa moyo wokhulupirika. 28Nditawalowetsa mʼdziko limene ndinachita kulumbirira kuti ndidzawapatsa, iwo tsono ankapita kulikonse kumene anaona chitunda chachitali ndi mtengo wa masamba ambiri kukapereka kumeneko nsembe ndi zopereka zawo zimene zinkandikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma ndiponso nsembe za zakumwa. 29Tsono ndinawafunsa kuti: Kodi chitunda chimene mukupitako nʼchotani? Chitundachi chakhala chikutchedwa mpaka lero kuti ‘Chitunda cha Chipembedzo.’

Chiweruzo ndi Kubwezeretsa

30“Tsono uwawuze Aisraeli kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi mudzadziyipitsa nokha monga anachitira makolo anu ndi kuchita chigololo ndi milungu yawo yonyansa? 31Pamene mubwera kudzapereka mphatso zanu ndi kudzapereka ana kuti akhale ngati nsembe zopsereza mumadziyipitsa ndi mafano anu mpaka lero. Kodi Aisraeli, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, sindidzalola kuti mupemphe nzeru kwa Ine.

32“ ‘Inu munanena kuti, ‘Tikufuna tikhale ngati anthu a mitundu ina, ngati anthu adziko lapansi, amene amapembedza mtengo ndi mwala.’ Koma zimene mukuganizazo sizidzachitika. 33Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga mokwiya kwambiri, Ine ndidzakhala wokulamulani. 34Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndikukusonkhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munamwazikirako, ndi dzanja langa lamphamvu ndi lotambasuka ndili wokwiya kwambiri. 35Ndidzakulowetsani mʼchipululu cha anthu a mitundu ina ndipo kumeneko, moonana maso ndi maso, ndidzakuzengani mlandu. 36Monga ndinawalangira makolo anu mʼchipululu cha dziko la Igupto, motero ndidzakulangani, akutero Ambuye Yehova. 37Ndidzakuwerengani ndi ndodo ya mʼbusa, kukulowetsani mʼchimango cha pangano langa. 38Ndidzakuchotserani anthu amene anandigalukira ndi kundiwukira. Ngakhale ndidzawatulutsa mʼdziko limene akukhalamo, koma sadzalowamo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

39“ ‘Koma inu Aisraeli, zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Pitani katumikireni mafano anu onse, aliyense wa inu! Koma mʼtsogolo mwake mudzandimvera ndithu ndipo simudzayipitsa dzina langa lopatulika popereka mphatso zanu kwa mafano. 40Pakuti pa phiri langa lopatulika, phiri lalitali la ku Israeli, akutero Ambuye Yehova, Aisraeli onse adzanditumikira, ndipo kumeneko Ine ndidzawalandira. Kumeneko ndidzayembekeza zopereka zanu ndi mphatso zanu zopambana, pamodzi ndi nsembe zanu zonse zopatulika. 41Ndidzakulandirani ngati nsembe ya fungo lokoma ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukusokhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munabalalitsidwirako. Motero ndidzadzionetsa pakati panu kuti ndine woyera ndipo mitundu ya anthu idzaona. 42Tsono mudzadziwa kuti ndine Yehova ndikadzabwera nanu ku dziko la Israeli, dziko limene ndinalumbira kuti ndidzapereka kwa makolo anu. 43Kumeneko mudzakumbukira makhalidwe anu ndi machitidwe anu onse amene munadziyipitsa nawo, ndipo mudzanyansidwa nokha chifukwa cha zoyipa zimene munachita. 44Inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzakuchitirani zabwino chifukwa cha dzina langa koma osati molingana ndi njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu okhota, inu Aisraeli, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Uneneri Wotsutsa Kummwera

45Yehova anandiyankhula nati: 46“Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane kummwera; ndipo lalika mawu odzudzula anthu akummwera ndipo unenere zodzudzula dziko la nkhalango ya kummwera. 47Iwuze nkhalango yakummwera kuti, ‘Imvani mawu a Yehova! Ambuye Yehova akuti: Ndikuyatsa moto ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse yayiwisi ndi yowuma yomwe. Malawi ake sadzazimitsika ndipo aliyense kuchokera kummwera mpaka kumpoto adzapsa nawo. 48Aliyense adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndayatsa motowo, ndipo sudzazimitsidwa.’ ”

49Ndipo ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova! Anthu akungondinena kuti, ‘Kodi suja amangonena nthano chabe ameneyu!’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以西结书 20:1-49

以色列人的悖逆

1第七年五月十日,有几个以色列的长老来到我这里,坐在我面前。 2耶和华对我说: 3“人子啊,你要告诉他们,主耶和华这样说,‘你们是来求问我吗?我凭我的永恒起誓,我决不让你们求问。’ 4人子啊,你要审判他们?你要审判他们?要使他们知道他们祖先所做的可憎之事。 5你要告诉他们,主耶和华这样说,‘我拣选以色列那日,曾向雅各家的后裔起誓,又在埃及向他们显现,告诉他们我是他们的上帝耶和华。 6那日我向他们起誓,要带领他们离开埃及,到我为他们预备的奶蜜之乡,世上最佳美的地方。 7我告诉他们要除掉他们祭拜的可憎之物,不可让埃及的偶像玷污自己,因为我是他们的上帝耶和华。

8“‘然而,他们却背叛我,不听我的话,没有除去他们祭拜的可憎之物和埃及的偶像。我本想在埃及向他们发烈怒,倾倒我的怒火, 9但我没有这样做,以免我的名在他们寄居的列邦面前被亵渎。因为列邦亲眼看见我向以色列人显现,把他们带出埃及10于是,我带他们离开埃及,进入旷野, 11向他们颁布我的律例和典章,若有人遵守,就必活着。 12我又让他们遵守我的安息日,作为我与他们之间的记号,好叫他们知道是我耶和华使他们成为圣洁之民。

13“‘可是,以色列人却在旷野背叛我,不遵行我的律例和典章——遵行的人必活着,大肆亵渎我的安息日。我本想在旷野向他们发烈怒,灭绝他们。 14但我没有这样做,以免我的名在周围列邦面前被亵渎,因为列邦亲眼看见我向以色列人显现,把他们带出埃及15我在旷野曾向他们发誓,不带他们进入我赐给他们的那奶蜜之乡,那世上最佳美的地方, 16因为他们不遵守我的典章,不顺从我的律例,亵渎我的安息日,心恋偶像。 17但我怜悯他们,没有毁灭他们,没有在旷野把他们全部灭绝。

18“‘我在旷野曾对他们的子孙说,不要效法你们祖先的律例,不要遵守他们的规条,不要拜他们的偶像,以致玷污自己。 19我是你们的上帝耶和华,你们要恪守我的律例,谨遵我的典章, 20尊我定的安息日为圣日,作为我与你们之间的记号,使你们知道我是你们的上帝耶和华。

21“‘可是,他们的子孙却背叛我,不恪守我的律例,不谨遵我的典章——遵守的人必活着。他们亵渎我的安息日。我本想在旷野向他们发烈怒,倾倒我的怒气, 22但我没有这样做,以免我的名在周围列邦面前被亵渎,因为列邦亲眼看见我向以色列人显现,把他们带出埃及23我在旷野起誓要把他们驱散到列国,分散到列邦, 24因为他们不遵行我的典章,弃绝我的律例,亵渎我的安息日,眼睛恋慕他们祖先的偶像。 25所以,我任由他们效法无用的律例,遵守无法使人活着的规条, 26任由他们把自己的长子烧作祭物献给偶像,以致玷污自己——好使他们充满恐惧,这样他们便知道我是耶和华。’

27“人子啊,你要告诉以色列人,主耶和华这样说,‘你们的祖先背信弃义,亵渎了我。 28当我引领他们进入我曾起誓要赐给他们的土地时,他们在所见的每一处高山或密林献祭,焚烧馨香的祭牲,向偶像奠酒,惹我发怒。 29我问他们,你们所去的高处是什么地方?’从此,那高处一直叫巴麻

30“所以,你要告诉以色列人,主耶和华这样说,‘你们仍像你们祖先一样与可憎的偶像苟合,玷污自己吗? 31你们至今仍把自己的儿子烧作祭物献给偶像,玷污自己吗?以色列人啊,我会让你们求问吗?主耶和华说,我凭我的永恒起誓,我决不让你们求问。

32“‘你们说要像外族人一样去供奉木头石头,你们的想法绝不能实现!’

33“主耶和华说,‘我凭我的永恒起誓,我要发烈怒,伸出大能的臂膀治理你们。 34我要发烈怒,伸出大能的臂膀把你们从列国中领出来,从你们散居的列邦聚集你们, 35领你们进入外族人的旷野,面对面地审判你们, 36就像我从前在埃及的旷野审判你们的祖先一样。这是主耶和华说的。 37我要对你们严加管教20:37 对你们严加管教”希伯来文是“让你们在杖下经过”。,使你们遵守我的约。 38我要铲除你们中间叛逆和犯罪的人。虽然我要领他们离开寄居之地,他们却不能回以色列。这样,你们就知道我是耶和华。’

39“主耶和华说,‘你们以色列人若不听我的话,就去供奉你们的偶像吧!但将来你们必不再向偶像献祭物亵渎我的圣名!’

40“主耶和华说,‘在我的圣山,就是以色列的高山上,所有的以色列人都要事奉我,我要在那里悦纳你们,要求你们献上供物、最好的礼物和一切圣物。 41当我把你们从列国领出来,从你们散居的列邦聚集起来时,你们必如馨香之祭一样蒙我悦纳,我必当着列国的面在你们中间彰显我的圣洁。 42我要把你们带回我起誓应许给你们祖先的以色列,这样你们就知道我是耶和华。 43你们在那里会想起以往玷污自己的行径,并因自己的一切恶行而憎恶自己。’ 44主耶和华说,‘以色列人啊,我为了自己的名,没有照你们的邪恶行径惩罚你们,这样你们便知道我是耶和华。’”

45耶和华对我说: 46“人子啊,你要面向南方,说预言斥责南地的树林。 47你要对南地的树林说,‘你要听耶和华的话。主耶和华说,我要在你那里燃起火来,烧毁你所有的青树和枯树。这不熄的烈火要从南到北烧焦一切。 48这样,世人便知道这烈火是我耶和华点燃的,它绝不会熄灭。’” 49于是我说:“唉,主耶和华啊,他们在议论我说,‘这人岂不是在说比喻吗?’”