Ezekieli 12 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 12:1-28

Chifaniziro cha Otengedwa Ukapolo

1Yehova anayankhula nane kuti, 2“Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu owukira, iwowo maso openyera ali nawo, koma sakuona ndipo makutu omvera ali nawo, koma sakumva chifukwa choti ndi anthu owukira.

3“Choncho, iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Unyamuke nthawi yamasana iwo akuona. Uchite ngati wanyamuka kuchoka kumene ukukhala kupita ku dziko lachilendo iwowo akuona. Mwina adzamvetsetsa, paja ndi anthu aupandu. 4Utulutse katundu wako wopita naye ku ukapolo nthawi ya masana iwo akuona. Ndipo nthawi ya madzulo, iwo akuona, uchoke monga ngati ukupita ku ukapolo. 5Iwo akuona, ubowole pa khoma ndipo utulutsirepo katundu wako. 6Usenze katundu wako pa phewa iwo akuona, ndipo upite kunja ku mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone pansi, pakuti ndakusandutsa iwe chizindikiro chochenjeza Aisraeli.”

7Choncho ine ndinachita monga momwe anandilamulira. Nthawi yamasana ndinatulutsa zinthu zanga nditazimanga ngati ndikupita ku ukapolo. Ndipo nthawi yamadzulo ndinabowola khoma ndi manja anga. Pamene chisisira chinkayamba, ndinasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye iwo akuona.

8Mmawa mwake Yehova anandiyankhula nati: 9“Iwe mwana wa munthu, kodi anthu aupandu a Israeli sanakufunse kuti ukuchita chiyani?

10“Uwawuze kuti, ‘zimene ndikunena Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndi izi: Uthengawu ndi wonena za kalonga wa ku Yerusalemu pamodzi ndi banja lonse la Israeli amene akukhala kumeneko.’ 11Uwawuze kuti, ‘Ndiwe chizindikiro chowachenjeza.’

“Zidzakuchitikirani monga momwe zakuchitikira iwemu. Iwo adzatengedwa kupita ku ukapolo.”

12“Kalonga wawo adzatenga katundu wake nʼchisisira nʼkunyamuka. Adzatulukira pa bowo limene anthu anabowola pa khoma. Adzaphimba nkhope yake kuti asaone kumene akupita. 13Ndidzayala ukonde wanga pa iye ndi kumukola mu msampha wanga. Ndidzabwera naye ku Babuloni, dziko la Akaldeya, koma sadzaliona dzikolo, ndipo adzafera kumeneko. 14Ine ndidzabalalitsa kumbali zonse zinayi onse okhala naye pafupi, ndiwo omuthandiza ake pamodzi ndi ankhondo ake. Ndidzawalondola ndi lupanga losolola.

15“Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira ku mayiko ena. 16Koma ndidzasiyako ena pangʼono amene adzapulumuke ku lupanga, njala ndi mliri, kuti akafotokoze ntchito zawo zonse zonyansa pakati pa anthu achilendo kumene akupitako. Pamenepo adzadziwa kuti ndine Yehova.”

17Pambuyo pake Yehova anandiyankhulanso nati, 18“Iwe mwana wa munthu, uzinjenjemera ukamadya chakudya chako, ndipo uzinthunthumira ndi mantha ukamamwa madzi ako. 19Uwawuze anthu a mʼdzikomo kuti izi ndi zimene Ambuye Wamphamvuzonse akunena za anthu okhala mu Yerusalemu ndi dziko la Israeli: Iwo adzadya chakudya chawo ndi mantha ndi kumwa madzi awo ndi nkhawa. Zonse za mʼdziko lawo zidzalandidwa chifukwa cha ziwawa za anthu onse okhala mʼmenemo. 20Mizinda imene ili ndi anthu idzasakazika ndipo dziko lidzasanduka chipululu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

21Yehova anayankhulanso nane kuti, 22“Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukunenedwa mu Israeli ndi wotani: ‘Masiku akupita koma masomphenya onse sakukwaniritsidwa?’ 23Choncho uwawuze anthuwo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndidzawuthetsa mwambi umenewu ndipo sadzawunenanso mu Israeli.’ Uwawuze kuti, ‘masiku ayandikira oti zonse zimene ndinanena mʼmasomphenya zichitikedi. 24Pakuti masiku amenewo sikudzakhalanso masomphenya abodza kapena kuwombeza kwa chinyengo pakati pa anthu a Israeli. 25Koma Ine Ambuye ndidzayankhula chimene ndikufuna, ndipo chidzachitikadi, osachedwa ayi. Pakuti mʼmasiku anu omwe ano, inu anthu opanduka, ndidzakwaniritsa chilichonse chimene ndidzanena. Ndikutero Ine Yehova.’ ”

26Yehova anandiyankhula nati: 27“Iwe mwana wa munthu, Aisraeli akunena kuti, ‘masomphenya amene ukuona sadzachitika kwa zaka zambiri. Iwo akuti ukulosa za zinthu zimene zidzachitika ku tsogolo kwambiri.’

28“Choncho uwawuze kuti, ‘zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso; chilichonse chimene ndikunena chidzachitikadi. Ndikutero Ine Yehova.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以西结书 12:1-28

被掳的预兆

1耶和华对我说: 2“人子啊,你住在叛逆的人当中。他们有眼睛却视而不见,有耳朵却听而不闻,因为他们是叛逆的人。 3所以,人子啊,你要准备流亡的行装,在白天当着他们的面从你住的地方搬到别处。他们虽然叛逆,或许还会明白其中的意思。 4你要在白天当着他们的面把预备流亡的行装拿出来,你要在晚上当着他们的面像流亡的人一样出去。 5你要当着他们的面在墙上挖一个洞,带着行装钻出去。 6你要在天黑时当着他们的面背着行装出发。你要蒙着脸使自己看不见地,因为我要使你成为以色列人被掳的预兆。”

7于是,我遵命而行。白天我把预备流亡的行装拿出来,晚上用手挖通了墙,当着他们的面背着行装在夜色中出发。

8第二天早晨,耶和华对我说: 9“人子啊,那些叛逆的以色列人不是问你在做什么吗? 10你要对他们说,‘主耶和华说,这是关于耶路撒冷的首领和城中以色列人的预兆。’ 11你要说,‘我就是给你们的预兆,我所做的必发生在你们身上,你们必被掳流亡。’ 12他们当中的首领必在黑夜背着行装出发,在墙上挖洞钻出去,而且必蒙着脸,看不见地。 13我必撒开网罗捕捉他,把他带到迦勒底人的巴比伦。他必看不见那地方,却要死在那里。 14我要把他周围的随从和所有军队驱散到四方,并且拔刀追杀他们。 15当我把他们驱赶到各国,分散到列邦时,他们就知道我是耶和华。 16然而,我要使他们当中一些人免遭刀剑、饥荒和瘟疫,使他们可以在各国供述自己一切可憎的事。他们就知道我是耶和华。”

17耶和华对我说: 18“人子啊,你要战战兢兢地吃饭,惶惶恐恐地喝水, 19然后对这地方的人说,‘关于耶路撒冷以色列的居民,主耶和华这样说,他们必焦虑不安地吃饭,惶恐不已地喝水,他们的土地必因其中居民的暴行而荒无人烟。 20他们居住的城邑必沦为废墟,土地必一片荒凉,他们就知道我是耶和华。’”

21耶和华对我说: 22“人子啊,你们以色列有一句俗语,‘光阴流逝,异象都落空。’ 23主耶和华这样宣告,我要废掉这句俗语,使它从以色列人的口中消失。你要对他们说,‘日子已近,异象都要应验。’ 24以色列人中必不再有虚假的异象和谄媚的预言。 25我是耶和华,我的话都必实现,决不迟延。你们这叛逆的人啊,我说的话必在你们有生之年应验!”这是主耶和华说的。

26耶和华对我说: 27“人子啊,你看,以色列人在说,‘他见的异象是关乎多年后的事,他说的预言是针对遥远的未来。’ 28因此,你要对他们说,‘主耶和华这样说,我的话必应验,不再迟延。’这是主耶和华说的。”