Estere 8 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Estere 8:1-17

Lamulo la Mfumu Lothandiza Ayuda

1Tsiku lomwelo mfumu Ahasiwero anamupatsa mfumukazi Estere nyumba ya Hamani, mdani wa Ayuda. Ndipo Mordekai anafika pamaso pa mfumu, popeza Estere anamuwuza ubale wawo. 2Mfumu inavula mphete yake yodindira imene analanda kwa Hamani ndipo Estere anamusankha Mordekai kukhala woyangʼanira nyumba ya Hamani.

3Estere anayankhulanso ndi mfumu ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake. Uku akulira iye anapempha mfumu kuti iletse choyipa, makamaka chiwembu chimene Hamani Mwagagi anakonza kuti awononge a Yuda. 4Ndipo mfumu inamuloza Estere ndi ndodo yake yagolide ndipo Estere anadzuka ndi kuyima pamaso pake.

5Iye anati, “Ngati chikomera mfumu ndi kukukondweretsani, ngati pempho langa muliona kuti ndi loyenera ndi kuti mukondwera nane tsono mfumu ilole kuti lamulo lilembedwe kusintha mawu a mʼmakalata amene Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, anatumiza ku zigawo zonse za mfumu. Paja Hamani analemba kuti Ayuda onse awonongedwe. 6Kodi ndingapirire bwanji pamene ndi kuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndingapirire bwanji pamene abale anga akuwonongedwa?”

7Mfumu Ahasiwero anamuyankha mfumukazi Estere ndi Mordekai Myuda kuti, “Ndapereka nyumba ya Hamani kwa Estere ndipo Hamaniyo amupachika kale pa mtanda chifukwa anafuna kuwononga Ayuda. 8Tsono inu awiri, lembani za Ayudawo monga mufunira. Mulembe mʼdzina la mfumu ndipo musindikize chizindikiro cha mphete ya mfumu popeza kuti cholembedwa mʼdzina la mfumu ndi kusindikizidwa ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu sichingasinthidwe.”

9Nthawi yomweyo, pa tsiku la 23 la mwezi wachitatu wa Sivani, mfumu inayitana alembi ake. Analemba zonse zokhudza Ayuda monga ananenera Mordekai. Analembera akazembe, abwanamkubwa ndi nduna za zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Zimene analamula Mordekai zinalembedwa mʼzilembo za chigawo chilichonse ndi chiyankhulo cha mtundu uliwonse wa anthu. Ayudanso anawalembera mʼmalemba awo ndi chiyankhulo chawo. 10Mordekai analemba makalatawo mʼdzina la mfumu Ahasiwero, nawadinda ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu. Ndipo anawatumiza ndi anthu amithenga amene anakwera pa akavalo a ufumu othamanga kwambiri obadwa mu khola la ufumu.

11Mʼmakalata amenewa mfumu inalola kuti Ayuda okhala mu mzinda uliwonse akhale ndi ufulu wokumana ndi kudzitchinjiriza komanso kuwononga, kupha ndi kufafaniziratu gulu lililonse la nkhondo la anthu a mtundu uliwonse kapena chigawo chimene chingawathire nkhondo. Ayudawo analoledwa kuwononga gulu lankhondo lija, ana awo ndi akazi awo komanso kuti afunkhe katundu wawo. 12Ayuda analoledwa kuchita zimenezi mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku limodzi lokha la 13 la mwezi wa 12, mwezi wa Adara. 13Mawu a mʼmakalatawo anayenera kudziwitsidwa kwa anthu a mtundu uliwonse mu chigawo chilichonse kuti ndi lamulo ndithu kwa anthu a mtundu uliwonse ndi kuti Ayuda adzakhale okonzeka pa tsikulo kulipsira kwa adani awo.

14Atawalamulira a mfumu, amithenga aja anapita nawo makalata mwachangu, atakwera pa akavalo a mfumu. Ndipo lamulolo analiperekanso ku likulu la mzinda wa Susa.

15Mordekai anachoka pamaso pa mfumu atavala zovala zaufumu zooneka ngati mtambo ndi zofewa zoyera, chipewa chachikulu cha golide ndi mkanjo wapepo. Ndipo mzinda wa Susa unafuwula mokondwa. 16Kwa Ayuda inali nthawi ya nkhope zowala ndi za chimwemwe, chikondwerero ndi ulemu. 17Mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse, kumene mawu a mfumu onena za lamulo lake anafika, kunali chimwemwe ndi chikondwerero pakati pa Ayuda. Linali tsiku la phwando ndi chikondwerero. Ndipo anthu ambiri a mitundu ina anazitcha Ayuda chifukwa anachita mantha ndi Ayudawo.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以斯帖記 8:1-17

猶太人獲拯救

1當天,亞哈隨魯王把猶太人的仇敵哈曼的家產賜給以斯帖王后。末底改也來到王面前,因為以斯帖陳明了他們的親屬關係。 2王摘下自己的戒指,就是從哈曼手中取回的,賜給末底改以斯帖末底改管理哈曼的家產。

3以斯帖又俯伏在王的腳前,流淚哀求王廢掉亞甲哈曼加害猶太人的陰謀。 4王向以斯帖伸出金杖,以斯帖就起來站在王面前, 5說:「王若願意,我若得到王的恩寵,王若認為好,並且喜悅我,就請王降旨,廢除亞甲哈米大他的兒子哈曼陰謀滅絕各省猶太人的諭旨。 6我怎能忍心看我本族的人受害?我怎能忍心看我的親族被殺?」 7亞哈隨魯王對以斯帖王后和猶太末底改說:「我已把哈曼的家產賜給以斯帖,並把他吊在木架上了,因為他想害猶太人。 8現在,你們盡可奉王的名寫諭旨給猶太人,用王的戒指蓋印,因為奉王的名所寫、用王的戒指蓋印的諭旨是不可廢除的。」

9三月,即西彎月二十三日,王的書記被召來,按照末底改的一切吩咐用各省的文字和各族的語言,包括猶太人的文字和語言寫諭旨,傳給從印度古實的一百二十七省的猶太人、總督、省長和官員。 10末底改亞哈隨魯王的名寫諭旨,用王的戒指蓋印,讓信差騎王室快馬送往各地。 11-12諭旨上說,王准許各城的猶太人在十二月,即亞達月十三日,聚集起來自衛,剷除、殺光、滅盡各族各省攻擊他們的仇敵及其兒女、妻子,奪取仇敵的財物。 13諭旨的抄本頒佈到各省,昭告各族,使猶太人在那天預備好向仇敵報仇。 14信差接到王的命令,急忙騎上王室快馬上路。在書珊城也頒佈了諭旨。

15末底改身穿藍色和白色朝服,頭戴大金冠,披著紫色細麻布外袍,從王那裡出來,書珊城的人都歡呼雀躍。 16猶太人高興歡喜,感到快樂光榮。 17各省各城,凡諭旨所到之處,猶太人都歡喜快樂,設宴慶祝。許多當地人因懼怕猶太人而入了猶太籍。