Estere 7 – CCL & CARST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Estere 7:1-10

Hamani Aphedwa

1Choncho mfumu ndi Hamani anabwera kudzadya phwando la mfumukazi Estere. 2Pa tsiku lachiwiri akumwa vinyo, mfumu inafunsanso kuti, “Kodi iwe mfumukazi Estere, chimene ufuna kupempha nʼchiyani? Chimene uti upemphe ndidzakupatsa. Choncho ukufuna chiyani? Ngakhale utafuna theka la ufumu ndidzakupatsa.”

3Kenaka mfumukazi Estere anayankha kuti, “Ngati mwandikomera mtima, inu mfumu, ndipo ngati chingakukomereni mfumu, pempho ndi chokhumba changa ndi ichi, mulole kuti ine ndi abale anga tisungidwe tonse ndi moyo. 4Popeza ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti atiwononge, atiphe ndi kutifafaniziratu. Akanangotigulitsa kokha tikanakhala chete, chifukwa chimene mdani wathuyo akanakupatsani mfumu sibwenzi mutasowa nacho mtendere.”

5Mfumu Ahasiwero anamufunsa mfumukazi Estere, “Kodi iyeyu ndi ndani ndipo ali kuti amene saopa kuchita chinthu chotere?”

6Estere anati, “Wotizunza ndiponso mdani wathu! Munthu woyipayo ndi Hamani.”

Kenaka Hamani anagwidwa ndi mantha pamaso pa mfumu ndi mfumukazi. 7Mfumu itakwiya kwambiri inanyamuka pa phwando nipita ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu. Koma Hamani, pozindikira kuti mfumu yaganiza kale kumuchitira choyipa, anatsalira mʼnyumba kupempha Estere kuti apulumutse moyo wake.

8Mfumu itabwerera kuchokera ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu uja ndi kulowanso mʼchipinda chaphwando, anapeza Hamani atagona chafufumimba pa mpando wa khutagone pomwe Estere anakhalapo.

Mfumu inayankhula mokweza kuti, “Kodi afunanso kuvula mfumukazi momukakamiza pamene ine ndili mʼnyumba?”

Mfumu isanatsirize kuyankhula mawu awa, atumiki ake anaphimba nkhope ya Hamani. 9Haribona, mmodzi wa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu anati, “Mtanda wotalika mamita 23 uli mʼnyumba ya Hamani. Mtandawu, Hamani anapangira Mordekai, uja amene anapulumutsa mfumu ku chiwembu.”

Mfumu inati, “Mpachikeni pamenepo!” 10Choncho anamupachika Hamani pa mtanda umene anakonzera Mordekai. Kenaka mkwiyo wa mfumu unatsika.

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

Есфирь 7:1-10

Казнь Амана

1Царь с Аманом отправились пировать у царицы Есфири. 2И когда они пили вино во второй день, царь спросил опять:

– Царица Есфирь, чего ты хочешь? Всё тебе будет. Какова твоя просьба? Даже полцарства – всё получишь!

3И царица Есфирь ответила:

– О царь, если я нашла у тебя расположение и если это угодно царю, то сохрани мне жизнь – вот чего я хочу. И пощади мой народ – вот моя просьба. 4Ведь я и мой народ проданы на погибель, уничтожение и искоренение. Если бы нас всего лишь продали как рабов и рабынь, я бы смолчала и не стала из-за этого беспокоить царя7:4 Или: «…смолчала, хотя враг и не возместил бы ущерба царю»..

5Царь Ксеркс спросил царицу Есфирь:

– Кто же он? Кто осмелился такое сделать?

6Есфирь сказала:

– Противник и враг – этот подлый Аман.

И Аман задрожал от страха перед царём и царицей. 7Царь в гневе поднялся с места, оставил вино и вышел во дворцовый сад. А Аман, понимая, что царь уже решил его судьбу, остался, чтобы умолять царицу Есфирь даровать ему жизнь. 8В тот момент, когда царь вернулся из дворцового сада в пиршественный зал, Аман как раз приник к ложу, где возлежала царица Есфирь.

Царь вскричал:

– Да что же это такое, он ещё вздумал изнасиловать царицу прямо в моём дворце?!

Едва лишь слово слетело с уст царя, Аману накрыли лицо. 9И Харбона, один из евнухов, прислуживавших царю, сказал:

– Вот и виселица высотой в двадцать два метра7:9 Букв.: «пятьдесят локтей». стоит у Аманова дома; он приготовил её для Мардохея, чьё слово спасло царя.

Царь сказал:

– Вот и повесьте его на ней!

10И Амана повесили на виселице, которую он приготовил для Мардохея. И ярость царя улеглась.