Deuteronomo 8 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 8:1-20

Musayiwale Yehova

1Samalani potsata lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero, kuti mukhale ndi moyo ndi kuchulukana kuti mulande ndi kulowa mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu. 2Kumbukirani mmene Yehova Mulungu wanu anakutsogolerani njira yonse mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kukutsitsani ndi kukuyesani kuti adziwe chimene chinali mu mtima mwanu ngati mungathe kusunga malamulo ake kapena ayi. 3Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova. 4Mʼzaka makumi anayi zimenezi, zovala zanu sizinangʼambike ndipo mapazi anu sanatupe. 5Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani.

6Samalirani malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira yake ndi kumuopa Iye. 7Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino, dziko lokhala ndi mitsinje ndi mathawale a madzi, akasupe oyenderera mu zigwa ndi mʼmapiri, 8dziko lokhala ndi tirigu ndi barele, mpesa ndi mitengo ya mkuyu, makangadza, mafuta a olivi ndi uchi; 9dziko limene buledi sadzasowa ndipo simudzasowa chilichonse; dziko limene miyala yake ndi chitsulo ndipo ku mapiri ake mukhoza kukumbako mkuwa.

10Mukadya ndi kukhuta, yamikani Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani. 11Samalani kuopa kuti mungayiwale Yehova Mulungu wanu posasunga malamulo, zikhazikitso ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, 12kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo, 13ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka, 14mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo. 15Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma. 16Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino. 17Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, “Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi.” 18Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.

19Ine ndine mboni yokutsutsani lero lino, kuti mukayiwala Yehova Mulungu wanu ndi kutsata milungu ina nʼkumayigwadira, mudzawonongeka ndithu. 20Monga mitundu ina ya anthu imene Yehova anayiwononga pamaso panu, inunso mudzawonongedwa chifukwa chosamvera Yehova Mulungu wanu.