Deuteronomo 33 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 33:1-29

Mose Adalitsa Mafuko a Aisraeli

1Awa ndi madalitso amene Mose, munthu wa Mulungu, anawapereka kwa Aisraeli asanafe. 2Iye anati:

“Yehova anabwera kuchokera ku Sinai

ndipo anatulukira kuchokera ku Seiri;

anawala kuchokera pa Phiri la Parani.

Iye anabwera ndi chiwunyinji cha angelo

kuchokera kummwera, moto woyaka uli mʼdzanja mwake.

3Ndithu ndinu amene mumakonda anthu anu;

opatulika ake onse ali mʼmanja mwake.

Onse amagwada pansi pa mapazi anu

kuchokera kwa inu amalandira malangizo,

4malamulo amene Mose anatipatsa,

chuma chopambana cha mtundu wa Yakobo.

5Iye anali mfumu ya Yesuruni

pamene atsogoleri a anthu anasonkhana,

pamodzi ndi mafuko a Israeli.

6“Lolani Rubeni akhale ndi moyo ndipo asafe,

anthu ake asachepe pa chiwerengero.”

7Ndipo ponena za Yuda anati:

“Inu Yehova, imvani kulira kwa Yuda;

mubweretseni kwa anthu ake.

Ndi manja ake omwe adziteteze yekha.

Inu khalani thandizo lake polimbana ndi adani ake!”

8Za fuko la Alevi anati:

“Tumimu wanu ndi Urimu ndi za

mtumiki wanu wokhulupirika.

Munamuyesa ku Masa;

munalimbana naye ku madzi a ku Meriba.

9Iye ananena za abambo ake ndi amayi ake kuti,

‘Sindilabadira za iwo.’

Sanasamale za abale ake

kapena ana ake,

koma anayangʼanira mawu anu

ndipo anateteza pangano lanu.

10Iye amaphunzitsa Yakobo malangizo anu

ndi malamulo anu kwa Israeli.

Amafukiza lubani pamaso panu

ndiponso amapereka nsembe zanu zonse zopsereza pa guwa lanu.

11Inu Yehova, dalitsani luso lake lonse

ndipo mukondwere ndi ntchito za manja ake.

Menyani adani awo mʼchiwuno

kanthani amene amuwukira kuti asadzukenso.”

12Za fuko la Benjamini anati:

“Wokondedwa wa Yehova akhale mwamtendere mwa Iye,

pakuti amamuteteza tsiku lonse,

ndipo amene Yehova amamukonda amawusa pa mapewa ake.”

13Za fuko la Yosefe anati:

“Yehova adalitse dziko lake

ndi mame ambiri ochokera kumwamba

ndiponso madzi ambiri ochokera pansi pa nthaka;

14ndi zinthu zambiri zimene zimacha ndi dzuwa

ndiponso ndi zokolola zabwino kwambiri zimene zimacha ndi mwezi uliwonse;

15ndi zipatso zabwino kwambiri zochokera mʼmapiri amakedzanawa

ndiponso zokolola zochuluka zochokera ku zitunda zakalekale;

16ndi mphatso zabwino kwambiri zochokera pa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo

ndiponso kukoma mtima kwa Iye amene amakhala mʼchitsamba choyaka moto.

Madalitso onsewa akhale pa mutu pa Yosefe,

wapaderadera pakati pa abale ake.

17Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa;

nyanga zake zili ngati za njati.

Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina,

ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi.

Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu;

nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”

18Za fuko la Zebuloni anati:

“Kondwera Zebuloni, pamene ukutuluka,

ndipo iwe, Isakara, kondwera mʼmatenti ako.

19Adzayitanira mitundu ya anthu kumapiri,

kumeneko adzaperekako nsembe zachilungamo;

kumeneko adzadyerera zinthu zochuluka zochokera ku nyanja,

chuma chobisika mu mchenga.”

20Za fuko la Gadi anati:

“Wodala amene amakulitsa malire a Gadi!

Gadi amakhala kumeneko ngati mkango,

kukhadzula mkono kapena mutu.

21Iye anadzisankhira dziko labwino kwambiri;

gawo la mtsogoleri anasungira iye.

Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana,

anachita chifuniro cha Yehova molungama,

ndiponso malamulo onena za Israeli.”

22Za fuko la Dani anati:

“Dani ndi mwana wamkango,

amene akutuluka ku Basani.”

23Za fuko la Nafutali anati:

“Nafutali wadzaza ndi kukoma mtima kwa Yehova

ndipo ndi wodzaza ndi madalitso ake;

cholowa chake chidzakhala mbali ya kummwera kwa nyanja.”

24Za fuko la Aseri anati:

“Mwana wodalitsika kwambiri ndi Aseri;

abale ake amukomere mtima,

ndipo asambe mapazi ake mʼmafuta.

25Zotsekera za zipata zako zidzakhala za chitsulo ndi za mkuwa,

ndi mphamvu zako zidzakhala ngati masiku a moyo wako.

26“Palibe wina wofanana ndi Mulungu wa Yesuruni,

amene amakwera pa thambo kukuthandizani

ndiponso pa mitambo ya ulemerero wake.

27Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu,

ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha.

Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu,

adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’

28Motero Israeli adzakhala yekha mwamtendere;

zidzukulu za Yakobo zili pa mtendere

mʼdziko la tirigu ndi vinyo watsopano,

kumene thambo limagwetsa mame.

29Iwe Israeli, ndiwe wodala!

Wofanana nanu ndani

anthu opulumutsidwa ndi Yehova?

Iye ndiye chishango ndi mthandizi wanu

ndi lupanga lanu la ulemerero.

Adani ako adzakugonjera,

ndipo iwe udzapondereza pansi malo awo achipembedzo.”