Deuteronomo 28 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 28:1-68

Madalitso Akumvera

1Ngati mumvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamalitsa malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, Yehova Mulungu wanu adzakukwezani pamwamba pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi. 2Madalitso awa adzabwera kwa inu ndi kuyenda nanu ngati mumvera Yehova Mulungu wanu:

3Mudzadalitsika mʼmizinda yanu ndi kudalitsika mʼdzikolo.

4Yehova adzadalitsa ana anu, zokolola za mʼdziko lanu, ngʼombe zanu pamodzi ndi ziweto zanu zonse.

5Dengu lanu ndi chiwaya chanu cha buledi zidzadalitsika.

6Mudzadalitsika pa kulowa kwanu ndi pa kutuluka kwanu.

7Yehova adzaonetsetsa kuti adani anu amene adzakuwukirani agonjetsedwe pamaso panu. Iwo adzabwera kwa inu kuchokera mbali imodzi koma adzakuthawani ku mbali zisanu ndi ziwiri.

8Yehova adzatumiza madalitso pa nkhokwe zanu ndi pa chilichonse chimene muchikhudza. Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene akukupatsani.

9Yehova Mulungu wanu adzachititsa kuti mukhale anthu ake opatulika, monga momwe analonjezera pa malumbiro ake, ngati musunga malamulo ake ndi kuyenda mʼnjira zake. 10Pamenepo anthu onse a dziko lapansi adzaona kuti mumadziwika ndi dzina la Yehova ndipo adzakuopani. 11Yehova adzakupambanitsani kwambiri ndipo adzakupatsani ana ambiri, ziweto zambiri, ndi zokolola zochuluka, mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani.

12Yehova adzatsekula kumwamba kumene amasungirako chuma chake, kutumiza mvula mʼdziko lanu pa nthawi yake ndi kudalitsa ntchito yonse ya manja anu. Mudzakongoza mitundu yambiri koma inu simudzakongola kwa aliyense. 13Yehova adzakuthandizani kukhala mutu osati mchira. Mukakhala ndi chidwi ndi malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero lino ndi kuwatsata mosamalitsa, inu mudzakhala apamwamba nthawi zonse osati apansi. 14Musapatukire ku dzanja lamanja kapena lamanzere pa lamulo lina lililonse limene ndikukupatsani lero lino ndi kumatsatira kapena kuyitumikira milungu ina.

Matemberero Akusamvera

15Koma ngati simumvera Yehova Mulungu wanu ndi kusatsata mosamalitsa malamulo ake ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, matemberero awa adzabwera pa inu ndikukugonjetsani:

16Mudzatembereredwa mu mzinda ndi kutembereredwa mʼmudzi.

17Dengu lanu ndi chiwaya chanu cha buledi zidzatembereredwa.

18Zipatso za mʼmimba mwanu zidzatembereredwa, ndiponso zomera za mʼdziko lanu, ana angʼombe zanu ndi ana ankhosa zanu zidzatembereredwa.

19Mudzatembereredwa pa kulowa kwanu ndi pa kutuluka kwanu.

20Yehova adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndi minyozo pa chilichonse chimene mudzachichita mpaka mudzawonongedwa ndi kukhala bwinja mofulumira chifukwa cha zoyipa zimene mwazichita pa kumutaya Yehova. 21Yehova adzakugwetserani mliri wa matenda mpaka atakuwonongani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali. 22Yehova adzakukanthani ndi nthenda yowondetsa, ya malungo ndi ya zotupatupa, ndi kutentha kwakukulu ndi chilala, ndi chinsikwi ndi chiwawu zimene zidzakusautsani mpaka mutawonongeka. 23Mitambo ya pamutu panu idzawuma ngati mkuwa ndipo sidzagwetsa mvula mpaka nthaka yanu idzawuma gwaa ngati chitsulo. 24Mʼmalo mwa mvula Yehova adzakupatsani fumbi ndi dothi ndipo lidzakugwerani kuchokera kumwamba mpaka mutawonongeka.

25Yehova adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Mudzadzera njira imodzi pokalimbana ndi adani anu koma pothawa mudzabalalika mbali zisanu ndi ziwiri. Mudzakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi. 26Mitembo yanu idzadyedwa ndi mbalame zamumlengalenga ndi nyama zakutchire, ndipo palibe amene adzaziyingitse. 27Yehova adzakusautsani ndi zithupsa za ku Igupto ndi zotupatupa, zipere, ndi mphere zimene simudzachiritsika nazo. 28Yehova adzakusautsani inu ndi misala, khungu ndi chisokonekero cha maganizo. 29Masanasana mudzayenda ngati muli mu mdima, kumafufuzira njira ngati wosaona. Mudzakhala olephera pa chilichonse mungachite. Tsiku ndi tsiku mudzaponderezedwa ndi kuberedwa wopanda wokupulumutsani.

30Mudzachita chinkhoswe ndi mkazi, koma wina adzakulandani ndi kumukwatira. Mudzamanga nyumba koma simudzagonamo. Mudzalima munda wamphesa koma simudzadyako zipatso zake. 31Ngʼombe yanu yamtheno idzaphedwa inu muli pomwepo koma simudzadyako. Bulu wanu adzalandidwa kwa inu mwamakani osabwera nayenso. Nkhosa zanu zidzapatsidwa kwa adani anu, ndipo palibe amene adzazipulumutsa. 32Ana anu aamuna ndi aakazi adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina ndipo inu mudzafika potopa ndi kulefuka nʼkudikirira tsiku ndi tsiku kuti mwina anawo abwerako. 33Anthu amene simukuwadziwa adzakudyerani zokolola zanu, ndipo mudzakhala mukuponderezedwa mwankhanza masiku onse. 34Zimene muzidzaziona zidzakusokonezani mitu. 35Yehova adzakusautsani ndi zithupsa zaululu ndi zosachiritsika za mʼmawondo ndi mʼmiyendo ndipo zidzafalikira kuchoka kuphazi mpaka kumutu.

36Yehova adzakuthamangitsirani, inu ndi mafumu anu amene muwayika, ku dziko losadziwika kwa inu ndi kwa makolo anu. Kumeneko mudzakapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi miyala. 37Inu mudzakhala chinthu chochititsa mantha kuchisunga ndiponso chinthu chotukwanidwa ndi chonyozeka kwa anthu a mitundu yonse kumene Yehova adzakuthamangitsirani.

38Mudzadzala mbewu zambiri ku munda koma mudzakolola pangʼono, chifukwa dzombe lidzaziwononga. 39Mudzadzala mpesa ndi kulimirira koma vinyo wake simudzamumwa kapena kukolola mphesazo, chifukwa mphutsi zidzadya mphesazo. 40Mudzakhala ndi mitengo ya olivi mʼdziko lanu lonse koma simudzagwiritsa ntchito mafuta ake, chifukwa zipatso zake zidzayoyoka. 41Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi koma sadzakhala anu, chifukwa adzapita ku ukapolo. 42Magulumagulu a dzombe adzawononga mitengo yanu ndi mbewu za mʼdziko lanu.

43Mlendo wokhala pakati panu adzatukuka kuposa inu, koma inuyo mudzaloweralowera pansi. 44Iye adzakubwereketsani, koma inu simudzatha kubwereketsa. Iye adzakhala mutu ndipo inu mudzakhala mchira.

45Matemberero onsewa adzabwera pa inu. Adzakulondolani ndi kukugonjetsani mpaka mutawonongeka, chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene anakupatsani. 46Matemberero amenewa adzakhala chizindikiro ndi chozizwitsa kwa inu ndi zidzukulu zanu mpaka kalekale. 47Pakuti inu simunatumikire Yehova Mulungu wanu pa nthawi imene zinthu zinkakuyenderani bwino, 48chomwecho pa nthawi ya njala ndi ludzu, ya maliseche ndi umphawi woopsa, mudzatumikira adani amene Yehova adzakutumizirani. Iye adzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwanu kufikira atakuwonongani.

49Yehova adzakutumizirani mtundu wa anthu kuchokera kutali kumapeto kwa dziko lapansi nudzachita ngati mphungu yowulukira pansi, mtundu wa anthu umene chiyankhulo chawo simudzachimva, 50mtundu wooneka wochititsa mantha, wopanda ulemu kwa okalamba kapena chisoni kwa ana. 51Iwo adzagwira ana a ziweto zanu, natenga zokolola za mʼdziko lanu kufikira mutawonongeka. Iwo sadzakusiyirani tirigu, vinyo watsopano kapena mafuta a olivi, kapena mwana wangʼombe aliyense kapena mwana wankhosa mpaka mutasanduka bwinja. 52Iwo adzathira nkhondo mizinda yonse mʼdziko lanu lonse mpaka malinga anu ataliatali omwe mumadalira aja atagwa. Adzathira nkhondo mizinda yonse ya mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.

53Chifukwa cha zosautsa zimene mdani wanu adzabweretsa pa nthawi yokuthirani nkhondo, inu mudzadya ana anu, mnofu wa ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani. 54Ngakhale munthu woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu sadzakhala ndi chifundo pa mʼbale wake weniweni kapena mkazi wake amene iye amamukonda kapena ana ake otsalawo, 55ndipo sadzagawirako aliyense wa iwo mnofu wa ana ake amene akudyawo. Kadzakhala kali komweko basi kamene kamutsalira chifukwa cha msautso umene mdani wanu adzagwetsa pa nthawi yothira nkhondo mizinda yanu yonse. 56Mayi woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu, uja woti sangayerekeze kuponda pansi, adzabisira mwamuna wake amene amamukonda ndi ana ake omwe aamuna ndi aakazi 57zotsalira za uchembere zochoka mʼmimba mwake ndi ana amene wabereka. Pakuti adzafuna kuti adye zimenezi yekha mobisa pa nthawi yothiridwa nkhondo chifukwa cha masautso amene mdani wanu adzagwetsa pa inu mʼmizinda yanu.

58Ngati simutsata mosamalitsa mawu onse a malamulo awa amene alembedwa mʼbuku lino, komanso ngati simuopa dzina la ulemerero ndi loopsa, dzina la Yehova Mulungu wanu, 59Yehova adzatumiza pa inu ndi zidzukulu zanu miliri yoopsa, zosautsa zowawa ndi zokhalitsa, ndi matenda aakulu ndi ovuta kuchiritsika. 60Adzakubweretserani matenda onse a ku Igupto aja mumawaopawa ndipo adzakukanirirani. 61Yehova adzakubweretseraninso mtundu uliwonse wa matenda ndi zosautsa zimene sizinalembedwe mʼbuku la malamulo lino, mpaka mutawonongeka. 62Inu aja munali ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba mudzatsala ochepa chabe chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu. 63Monga kunamukomera Yehova kukulemeretsani ndi kukuchulukitsani, momwemonso kudzamukondweretsa kukunthani ndi kukuwonongani. Inu mudzazulidwa kukuchotsani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali.

64Kenaka Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu yonse, kuchokera ku mapeto a dziko kufika ku mapeto ena. Kumeneko mudzapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi ya miyala, imene inu eni kapena makolo anu sanayidziwepo. 65Pakati pa mitundu ya anthu imeneyi simudzapeza mpata, popanda malo woti nʼkuyikapo phazi. Kumeneko Yehova adzakupatsani moyo wa nkhawa, maso otopa ndi chiyembekezo, ndi mtima wosakhazikika. 66Inu mudzakhala osakhazikika mopitirira, odzazidwa ndi mantha usiku ndi usana womwe, osowa chitsimikizo cha pa moyo wanu. 67Mmawa muzidzati, “Chikhala anali madzulo!” ndipo madzulo mudzati, “Chikhala unali mmawa!” Mudzanena zimenezi chifukwa cha mantha amene adzakhale mu mtima mwanu ndi chifukwa cha zomwe muzidzaziona. 68Yehova adzakubwezani ku Igupto pa sitima zapamadzi paulendo umene Ine ndinati musawuyendenso. Kumeneko mudzadzitsatsa nokha kwa adani anu monga akapolo aamuna ndi aakazi, koma palibe amene adzakuguleni.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

申命記 28:1-68

遵守誡命蒙祝福

1「你們若全心順服你們的上帝耶和華,謹遵祂今天藉我吩咐你們的一切誡命,祂必使你們超越天下萬國。 2你們若聽從你們的上帝耶和華的話,以下的福氣必臨到你們,追隨你們。

3「無論你們住在城裡還是鄉村,都必蒙福。

4「你們必子孫昌盛,五穀豐登,牛羊成群。

5「你們的籃子和揉麵盆都必蒙福。

6「你們必出入平安。

7「耶和華必使來犯之敵敗在你們面前、潰不成軍、四散逃命。

8「耶和華必使你們凡事蒙福、五穀滿倉。你們的上帝耶和華必在祂賜給你們的土地上賜福你們。

9「你們若遵守你們上帝耶和華的誡命,遵行祂的旨意,祂必按自己的誓言使你們成為祂聖潔的子民。 10天下萬民將看出你們是耶和華的子民,並懼怕你們。

11「在耶和華向你們祖先起誓要賜給你們的土地上,祂必使你們子孫昌盛、牛羊成群、五穀豐登。 12耶和華要為你們打開天上美好的倉庫,使你們風調雨順、凡事蒙福。你們必借貸給多國,卻無需向別國借貸。 13-14你們若聽從你們的上帝耶和華藉我今天吩咐你們的誡命,謹慎遵行,毫不偏離,也不隨從、供奉別的神明,祂必使你們做首不做尾,居上不居下。

違背誡命受咒詛

15「你們若不聽從你們的上帝耶和華,不謹遵祂今天藉我吩咐你們的一切誡命和律例,祂必使以下的咒詛臨到你們。

16「無論你們住在城裡還是鄉村,都必受咒詛。

17「你們的籃子和揉麵盆都必受咒詛。

18「婦女所生的,土地所產的,牛羊所生的都必受咒詛。

19「你們出入都必受咒詛。

20「因為你們背棄耶和華,祂要使你們凡事受咒詛、混亂不堪、飽受責罰,直到你們被毀滅,迅速滅亡。

21「祂要使瘟疫緊緊跟隨你們,直到你們在將要佔領的土地上被滅絕。

22「祂要使你們遭受癆病、熱症、瘧疾、炙熱、刀劍、乾旱和黴爛之災,直到你們滅亡。

23「祂要使你們頭頂的天如銅,腳下的地如鐵。

24「祂要使雨水變為塵土,降在你們身上,直到你們滅亡。

25「祂要使你們被敵人擊敗、潰不成軍、四散逃命,下場令天下萬國驚懼。 26你們的屍體要成為飛禽走獸的食物,必無人趕走牠們。

27「祂要使你們患埃及的膿瘡、腫瘤和癬疥,無藥可治。

28「祂要使你們發瘋、失明、心智錯亂。

29「你們必在大白天摸索,就像盲人在黑暗中摸索一樣,你們的道路必不得亨通,你們要終日受人欺壓搶掠,無人搭救。

30「你們聘了妻子,別人必佔有她;你們蓋了房屋,必不能住在裡面;你們栽種葡萄園,必吃不到園中的出產。

31「你們必看著自己的牛被宰殺卻吃不到肉,自己的驢被搶走後一去不還,自己的羊被敵人擄走卻無人搭救, 32自己的兒女被外族人擄走,你們終日望眼欲穿,卻無能為力。

33「與你們素不相識的民族必吃光你們土地的出產和勞碌所得,你們必常受欺壓, 34以致眼前的一切令你們發瘋。

35「耶和華要使你們從頭到腳長滿毒瘡,無藥可治。

36「耶和華要帶你們和你們的王到一個你們和你們祖先都不知道的國家,你們要在那裡供奉木石神像。

37「在耶和華驅逐你們去的列國,你們的下場將很可怕,受盡嘲笑和譏諷。

38「你們種的多,卻收的少,因為莊稼必被蝗蟲吃掉。

39「你們栽種、修剪葡萄園,卻吃不到葡萄,也喝不到葡萄酒,因為葡萄必被蟲子吃掉。

40「你們境內長滿橄欖樹,卻沒有橄欖油抹身,因為橄欖必未熟先落。

41「你們生兒育女,卻留不住一個,因為他們必被擄走。

42「蝗蟲要吃光你們的樹木和地上的出產。

43「你們中間的外族人要日益興旺,你們卻要日漸衰微。

44「他們要借貸給你們,你們卻不能借貸給他們。他們要做首,你們要做尾。

45「如果你們不聽你們上帝耶和華的話,不遵守祂吩咐你們的誡命和律例,這些咒詛都必臨到你們、追趕你們,直到毀滅你們。 46這些咒詛要永遠成為你們和你們子孫的警戒和徵兆。 47如果你們在富足時不心甘情願地事奉你們的上帝耶和華, 48你們必失去所有,饑餓乾渴、赤身裸體地侍奉耶和華派來攻擊你們的敵人。祂要把鐵軛加在你們的頸上,直到消滅你們。

49「耶和華要使一國從遙遠的地極興起,他們要如鷹飛來襲擊你們。你們不懂他們的語言。 50他們面目猙獰,不尊重年老的,也不憐憫年少的。 51他們要吃光你們的牛羊、五穀、新酒和油,直到消滅你們。 52在你們的上帝耶和華所賜給你們的土地上,他們要把你們圍困在各個城邑中,直到你們所依賴的高大堅固的城牆都倒塌。

53「當你們被敵人圍困、陷入絕境時,你們必吃自己的親生骨肉——你們的上帝耶和華賜給你們的兒女。 54-55因為被敵人困在城中,饑餓難熬,連你們中間最溫柔體貼的男人也要獨自吞吃子女的肉,不肯分給自己的兄弟、愛妻和剩下的兒女。 56-57因為被敵人困在城中,饑餓難熬,連你們中間最溫柔、嬌嫩得連腳也不肯踏在地上的婦女,都要偷偷吃掉自己生的嬰兒和胎胞,不肯分給所愛的丈夫和子女。

58「如果你們不謹遵這書上所寫的一切律法,不敬畏你們的上帝耶和華那榮耀、可畏的名, 59祂必使你們及子孫遭遇嚴重而長久的災難和疾病, 60使你們所懼怕的埃及人的疾病都降在你們身上,纏擾你們, 61還使一切未記在這律法書上的疾病和災難降在你們身上,直到消滅你們。 62如果你們不聽從你們的上帝耶和華的話,即使你們的人數多如天上的星,也將所剩無幾。 63正如耶和華喜歡賜福你們,使你們人丁興旺,祂也同樣會不惜消滅你們,使你們在將要佔領的土地上滅亡。

64「耶和華要把你們分散到天下萬邦,你們要在那裡供奉祖祖輩輩素不認識的木石神像。 65你們在萬邦中將不得安寧,沒有落腳之地,耶和華必使你們膽戰心驚、目光呆滯、精神頹廢。 66你們必惴惴不安,晝夜恐懼,生死難料。 67你們必看見可怕之事,以致心中充滿恐懼,早上盼望天黑,晚上盼望天亮。 68耶和華必沿著我曾說你們再不會走的路線,用船把你們送回埃及。你們將在那裡賣身做敵人的僕婢,卻無人買。」