Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 26

Zipatso Zoyamba ndi Chakhumi

1Mukalowa ndi kukhazikika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, mutengeko zina mwa zipatso zoyamba pa zonse zimene mudzakola mʼnthaka ya dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndi kuziyika mʼdengu. Mukatero mupite kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzakhazikitsako dzina lake ndipo mudzamuwuze wansembe amene ali pa ntchito pa nthawiyo kuti, “Ndikunenetsa lero kwa Yehova Mulungu wanu kuti ndabwera ku dziko limene Yehova analumbirira makolo athu kuti adzatipatsa ife.” Wansembe adzatenga dengulo mʼmanja mwanu ndi kuliyika pansi patsogolo pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. Ndipo mudzanenetsa pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, “Abambo anga anali Mwaramu woyendayenda, anapita ku Igupto ndi anthu ochepa nakhala kumeneko. Pambuyo pake anakhala mtundu waukulu, wamphamvu ndi wochuluka. Koma Aigupto anatisautsa natizunza, kumatigwiritsa ntchito yakalavulagaga. Kenaka tinafuwulira Yehova, Mulungu wa makolo athu ndipo Yehova anamva mawu athu ndi kuona kusauka, kuvutika ndi kuponderezedwa kwathu. Kotero Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndi mkono wotambasuka ndi zoopsa zazikulu ndi zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa. Iye anatibweretsa ku malo ano natipatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi lino. 10 Ndipo tsopano ndikubweretsa zipatso zoyamba zimene inu Yehova mwandipatsa.” Ikani dengulo pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kuwerama mopereka ulemu pamaso pake. 11 Ndipo inu ndi Alevi pamodzi ndi alendo okhala pakati panu mudzakondwera mʼzinthu zonse zabwino zimene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, inu ndi a pa banja panu.

12 Mukatha kupatula chakhumi pa zonse zimene mwakolola mʼchaka chachitatu chimene ndi chaka chakhumi, muzichipereka kwa wansembe, mlendo, ana ndi akazi amasiye, kuti pamenepo adye mʼmizinda yanu nakhuta. 13 Kenaka munene kwa Yehova Mulungu wanu kuti “Ndatulutsamo mʼnyumba mwanga gawo lopatulika ndipo ndalipereka kwa Mlevi, mlendo, ana ndi akazi amasiye, monga mwa zonse zimene munalamula. Sindinapatuke pa zimene munalamula kapena kuyiwala ndi chimodzi chomwe. 14 Sindinadye kalikonse ka gawo lopatulika pamene ndimalira maliro kapena kuchotsapo kalikonse ka gawo lopatulika pamene ndinali wodetsedwa, kapena kuperekako nsembe kwa akufa kalikonse ka gawoli. Ine ndamvera Yehova Mulungu wanga, ndachita chilichonse chimene inu munandilamula. 15 Yangʼanani pa dziko kuchokera kumwamba, ku malo anu wopatulika, ndi kudalitsa anthu anu Aisraeli ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi limene mwatipatsa ife monga momwe munalonjezera pa malumbiro anu kwa makolo athu.”

Tsatirani Malamulo a Yehova

16 Yehova Mulungu wanu akukulamulani lero lino kuti mutsate malangizo ndi malamulo ake ndipo muwasunge mosamalitsa ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 17 Mwanena motsimikiza lero lino kuti Yehova ndiye Mulungu wanu ndi kuti mudzayenda mʼnjira zake, kusunga malangizo, malamulo ndi zonse akukulamulani ndi kutinso mudzamumvera. 18 Ndipo Yehova wanenetsa lero lino kuti inu ndinu anthu ake, chuma chake chamtengowapatali monga momwe analonjezera, ndipo mukuyenera kusunga malamulo ake onse. 19 Iye wanenetsa kuti adzakuyikani kukhala oyamikika, otchuka ndi olemekezeka koposa mitundu yonse imene anayilenga. Komanso mudzakhala anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu monga momwe analonjezera.

Священное Писание (Восточный Перевод)

Второзаконие 26

Приношение первых плодов и десятины

1Когда ты придёшь в землю, которую Вечный, твой Бог, даёт тебе в наследие, завладеешь ею и поселишься в ней, то возьми все первые плоды, которые ты вырастишь на земле, которую Вечный, твой Бог, даёт тебе, и положи их в корзину. Затем иди на то место, которое Вечный, твой Бог, выберет для поклонения Ему, и скажи священнослужителю, что будет в те дни: «Я объявляю сегодня Вечному, твоему Богу, что я пришёл в землю, которую Вечный клялся нашим предкам дать нам». Священнослужитель возьмёт у тебя корзину и поставит её перед жертвенником Вечного, твоего Бога. Тогда ты объявишь перед Вечным, твоим Богом: «Мой отец был кочующим арамеем, он пришёл в Египет с немногими людьми, жил там и стал великим народом, могучим и многочисленным. Но египтяне плохо обращались с нами и причиняли нам страдания, принуждая к непосильному труду. Тогда мы взмолились Вечному, Богу наших предков, и Вечный услышал наш голос и увидел наше бедствие, непосильный труд и притеснение. Вечный вывел нас из Египта могучей и простёртой рукой, великим ужасом, знамениями и чудесами. Он привёл нас сюда и дал нам эту землю – землю, где течёт молоко и мёд; 10 и вот, теперь я приношу первые плоды с земли, которую Ты, Вечный, дал мне». Поставь корзину перед Вечным, твоим Богом, и склонись перед Ним. 11 Радуйся всему доброму, что Вечный, твой Бог, дал тебе и твоему дому, вместе с левитами и чужеземцами среди вас.

12 Отделив десятину от всего, что ты произвёл в третий год, год десятины, отдай её левиту, чужеземцу, сироте и вдове, чтобы они могли есть в твоих городах и насыщаться. 13 И скажи Вечному, твоему Богу: «Я взял из своего дома священную долю и отдал её левиту, чужеземцу, сироте и вдове, как Ты повелел. Я не уклонился от Твоих повелений и не забыл ни одного из них. 14 Я ничего не ел из священной доли, пребывая в трауре, не брал из неё ничего, будучи нечист, и не давал ничего из неё для мёртвого.[a] Я был послушен Вечному, моему Богу; Я сделал всё, что Ты повелел мне. 15 Посмотри с неба, Своего святого жилища, и благослови Свой народ Исраил и землю, которую Ты дал нам, как клялся нашим предкам, землю, где течёт молоко и мёд».

Повеление следовать законам Вечного

16 Сегодня Вечный, твой Бог, повелевает тебе следовать этим установлениям и законам, прилежно соблюдать их всем сердцем и всей душой. 17 Сегодня ты объявил, что Вечный – это твой Бог, и что ты будешь ходить Его путями, хранить Его установления, повеления и законы и слушаться Его. 18 А Вечный объявил сегодня, что ты – Его народ, Его драгоценное достояние, как Он и обещал, и что ты должен хранить все Его повеления. 19 Он объявил, что поставит тебя выше всех созданных Им народов, воздаст тебе хвалу, славу и честь, и ты будешь святым народом Вечного, твоего Бога, как Он и обещал.

Notas al pie

  1. 26:14 Для мёртвого – может иметься в виду посвящение части священной доли духу умершего или то, что она выделялась для ритуальной трапезы на похоронах. Все три перечисленных в этом стихе действия, соверши их говорящий, привели бы к осквернению священной доли.