Deuteronomo 15 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 15:1-23

Chaka Chokhululukira Ngongole

1Kumapeto kwa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, muzikhululukirana ngongole. 2Zimenezi muzichita motere: wobwereketsa aliyense adzakhululukira ngongole imene anabwereketsa kwa Mwisraeli mnzake. Iye asadzafunenso kuti Mwisraeli mnzakeyo kapena mʼbale wake amubwezere chifukwa nthawi ya Ambuye yokhululukirana ngongole yalengezedwa. 3Mukhoza kulonjerera ngongole kwa mlendo, koma mukhululukire ngongole ina iliyonse imene mʼbale wanu ali nayo. 4Komabe pasadzakhale wosauka pakati panu chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani kwambiri mʼdziko limene adzakupatsani kuti likhale lanu ngati cholowa chanu. 5Adzakudalitsani pokhapokha ngati mudzamveradi Yehova Mulungu wanu posunga ndi kutsatira malamulo onse amene ndikukupatsani lero. 6Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani monga analonjeza, ndipo inu mudzabwereketsa chuma kwa mitundu yambiri ya anthu koma inu simudzabwereka kwa aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri ya anthu koma inuyo palibe amene adzakulamulireni.

7Ngati pali mʼbale wanu wina wosauka mu mzinda wanu wina uliwonse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musawumitse mitima yanu kapena kuchita kaligwiritsa kwa mʼbale wanu wosaukayo. 8Koma mukhale ofewa manja ndipo mumukongoze mʼbale wanu momasuka pa chilichonse chimene akufuna. 9Musayesere ndi pangʼono pomwe kusunga maganizo oyipa awa mu mtima mwanu: “Chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka chokhululukirana ngongole, chayandikira,” kuti musaonetse mtima woyipa kwa mʼbale wanu wosauka nʼkusamupatsa chilichonse. Iye angadzakunenereni inu mlandu kwa Ambuye, ndipo mudzapezeka wochimwa. 10Mumupatse iye mowolowamanja ndipo muchite zimenezi mosasungira kanthu kumtima. Tsono chifukwa cha zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse ndi pa chilichonse chimene mukhudza. 11Anthu osauka sadzatha mʼdziko lanu. Chomwecho ndikukulamulani kuti mukhale ofewa manja kwa abale anu ndi kwa osauka, osowa mʼdziko mwanu.

Kumasula Akapolo a Chihebri

12Ngati mʼbale wanu wamwamuna kapena wamkazi adzigulitsa yekha kwa inu, nakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, muzimumasula mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri. 13Ndipo pamene mumumasula, musangomulola apite chimanjamanja. 14Mumupatse mowolowamanja zochokera pa ziweto zanu, kopunthira tirigu ndi kopsinyira vinyo. Inu mumupatse iye monga Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani. 15Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto ndipo Yehova Mulungu wanu anakupulumutsani. Nʼchifukwa chake ndikukupatsani lamulo ili lero lino.

16Koma ngati kapoloyo akuwuzani kuti, “Ine sindikufuna kumasulidwa,” chifukwa choti wakukondani inuyo pamodzi ndi banja lanu ndiponso kuti kwamukomera iyeyo kuti azikhalabe nanu, 17pamenepo muzitenga chobowolera chachitsulo ndi kubowola khutu lake pa chitseko, ndipo mukatero adzakhala kapolo wanu moyo wake wonse. Mdzakazi wanu muzimuchitanso chimodzimodzi.

18Musaone ngati chopweteka kumasula wantchito wanu, chifukwa ntchito imene wayigwira pa zaka zisanu ndi chimodzi zimenezi ndi yopindula kawiri pa ntchito imene akanagwira waganyu chabe. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita.

Ziweto Zoyamba Kubadwa

19Mumupatulire Yehova Mulungu wanu choyamba kubadwa chachimuna chilichonse pa ngʼombe ndi nkhosa zanu. Musamazigwiritse ntchito ngʼombe zoyamba kubadwa kapena kumeta nkhosa zoyamba kubadwa. 20Inuyo ndi banja lanu, chaka chilichonse muzizidya zimenezi pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene Iye adzasankhe. 21Ngati chiweto chili ndi chilema monga kulumala kapena chosaona, kapena ngati chili ndi cholakwika chachikulu chilichonse, musachipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu. 22Muzichidya mʼmizinda yanuyanu. Onse odetsedwa monga mwa mwambo ndi oyeretsedwa omwe akhoza kuchidya monga akudya gwape kapena mbawala. 23Koma musadye magazi ake. Muwathire pansi ngati madzi.

Het Boek

Deuteronomium 15:1-23

Het jubeljaar

1‘Aan het einde van elk zevende jaar moeten alle schulden worden kwijtgescholden. 2Iedere schuldeiser zal de schuld die een andere Israëliet bij hem heeft, volledig kwijtschelden, want de Here heeft iedereen van zijn verplichtingen ontslagen. 3Deze kwijtschelding geldt niet voor buitenlanders, maar wat uw broeder u schuldig is, moet u hem kwijtschelden. 4-5 Niemand zal hierdoor arm worden want, als u dit gebod gehoorzaamt, zal de Here u rijk zegenen in het land dat Hij u geeft. De enige voorwaarde die de Here stelt voor zijn zegen, is dat u zorgvuldig leeft naar de geboden van de Here, uw God, die ik u vandaag geef. 6Hij zal u zegenen zoals Hij heeft beloofd. U zult aan vele volken geld uitlenen, maar zelf zult u nooit iets hoeven lenen. U zult heersen over vele volken, maar zij zullen niet over u heersen.

7Als er bij uw aankomst in het land dat de Here u zal geven, enkele armen onder u zijn, moet u uw hart en hand niet voor hen sluiten, 8u moet hun net zoveel lenen als zij nodig hebben. 9Denk erom! Weiger nooit een lening omdat het jaar van kwijtschelding voor de deur staat! Als u weigert te lenen, zal de arme tot de Here roepen en dan zal het u worden toegerekend als een zonde. 10U moet hem lenen wat hij nodig heeft, zonder te klagen! Want de Here zal u helpen bij alles wat u doet, als u zo aan uw broeder leent! 11Er zullen altijd arme mensen onder u zijn, daarom is dit gebod noodzakelijk. U moet uw arme broeder vrijgevig tegemoet treden en hem lenen wat hij nodig heeft.

12Als u een Hebreeuwse slaaf koopt—man of vrouw—moet u hem, nadat hij zes jaar voor u heeft gewerkt, vrijlaten. 13Stuur hem niet met lege handen weg! 14Geef hem een royaal afscheidsgeschenk van uw kudde, uw wijnpers en uw olijfpers. Deel met hem datgene waarin de Here, uw God, u heeft gezegend. 15Denk eraan dat u zelf slaven bent geweest in het land Egypte en dat de Here, uw God, u redde! Daarom geef ik u dit gebod. 16Maar stel dat uw Hebreeuwse slaaf niet weg wil omdat hij van u houdt, zich in uw huis prettig voelt en goed met u kan opschieten, 17neem dan een priem en steek die tegen de deur door zijn oor. Daarna zal hij voor altijd uw slaaf zijn. Hetzelfde moet u met uw slavinnen doen. 18Maar als u een slaaf vrijlaat, moet u dat niet met een spijtig gevoel doen, de slaaf heeft u immers in die zes jaar de helft minder gekost dan een gehuurde werkkracht. De Here, uw God, zal u voorspoed geven in alles wat u doet, omdat u hem hebt vrijgelaten!

19U moet alle eerstgeboren mannelijke dieren van uw kudden afzonderen voor God. Gebruik de eerstgeborenen van uw ossen niet om het land mee te bewerken en scheer de eerstgeborenen van uw geiten en schapen niet. 20Nee, u en uw gezin moeten deze dieren elk jaar voor de ogen van de Here, uw God, in zijn heiligdom opeten. 21Maar als een eerstgeboren dier een gebrek heeft, als hij lam of blind is of als er iets anders aan hem mankeert, mag u het niet offeren. 22Gebruik het dier dan als voedsel voor uw gezin thuis. Iedereen, rein of onrein, mag ervan eten zoals ook iedereen van een gazelle of een hert mag eten. 23Alleen het bloed mag u niet eten, giet het als water uit op de grond.’