Danieli 4 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 4:1-37

Maloto Achiwiri a Nebukadinezara

1Mfumu Nebukadinezara anatumiza mawu awa kwa anthu a mitundu yonse, ndi chiyankhulo chilichonse, amene amakhala pa dziko lonse lapansi:

Mtendere uchuluke pakati panu!

2Chandikomera kukuwuzani zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wammwambamwamba wandichitira.

3Zizindikiro zake ndi zazikulu,

zozizwitsa zake ndi zamphamvu!

Ufumu wake ndi wamuyaya;

ulamuliro wake ndi wa mibadomibado.

4Ine Nebukadinezara, ndinali kwathu mʼnyumba yanga yaufumu, mwa mtendere ndipo ndinali wokhutitsidwa. 5Ndili chigonere pa bedi langa, ndinalota maloto amene anandichititsa mantha. Zinthu ndi masomphenya zimene ndinaziona zinandiopsa. 6Choncho ndinalamula kuti anthu onse a nzeru a ku Babuloni abwere pa maso panga kunditanthauzira malotowo. 7Pamene amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula anabwera, ndinawafotokozera maloto, koma sanathe kunditanthauzira. 8Potsiriza, anabwera Danieli uja amatchedwa Belitesezara, potsata dzina la mulungu wanga, ndipo mzimu wa milungu yoyera uli mwa iye. Iyeyu ndinamufotokozera malotowo.

9Ndinati, “Belitesezara, mkulu wa amatsenga, ndikudziwa kuti mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe, ndipo palibe chinsinsi chomwe sungachidziwe. Awa ndi maloto anga; unditanthauzire. 10Awa ndi masomphenya amene ine ndinaona pamene ndinali kugona pa bedi: Ndinaona, mtengo wautali kwambiri utayima pakati pa dziko lapansi. 11Mtengowo unakula ndi kulimba ndipo msonga yake inafika mpaka mlengalenga; umaonekera pa dziko lonse lapansi. 12Masamba ake anali okongola, zipatso zinali zochuluka, ndipo mu mtengomo munali chakudya chokwanira anthu onse. Zirombo zakuthengo zimapeza mthunzi mʼmunsi mwake, ndipo mbalame zamlengalenga zimakhala pa nthambi zake: Cholengedwa chilichonse chinkadya za mu mtengowu.

13“Ndikanali chigonere ndinaona mʼmasomphenya mngelo atayima pamaso panga, woyera, atatsika kuchokera kumwamba. 14Anayankhula mofuwula kuti, ‘Gwetsa mtengo ndi kusadza nthambi zake; yoyola masamba ake kuti nyama zakuthengo zithawe pa mthunzi pake ndi mbalame zithawe pa nthambi zake. 15Koma musiye tsinde ndi mizu yake mʼnthaka. Tsindelo mulimange maunyolo a chitsulo ndi mkuwa, zikhalebe mʼnthaka, nʼkudya udzu mʼmunda.

“ ‘Mumulole iye anyowe ndi mame akumwamba, ndipo iye akhale ndi nyama pakati pa zomera za mʼnthaka. 16Maganizo ake a umunthu asinthidwe ndipo apatsidwe maganizo a nyama ya kuthengo, mpaka zaka zisanu ndi ziwiri zitadutsa.

17“ ‘Angelo oyera ndiwo akutsimikiza chilangochi. Tsono anthu adziwe kuti Mulungu Wammwambamwamba ali ndi mphamvu yolamulira maufumu onse, ndipo amawapereka kwa aliyense akumufuna, ngakhale munthu wamba kuti alamulire.’

18“Amenewa ndi maloto amene ine, mfumu Nebukadinezara, ndinalota. Tsopano Belitesezara, undifotokozere tanthauzo lake, popeza palibe mwa anthu anzeru a mu ufumu wanga amene angathe kunditanthauzira. Koma iwe ukhoza, chifukwa mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe.”

Danieli Atanthauzira Maloto

19Pamenepo Danieli, amene amatchedwa Belitesezara, anavutika mu mtima kwambiri kwa kanthawi, ndipo anasautsidwa mʼmaganizo ake. Choncho mfumu inati, “Belitesezara usalole malotowa kapena tanthauzo lake likuopse.”

Belitesezara anayankha kuti, “Mbuye wanga, ndikanakonda malotowa akanakhudza adani anu okha, ndi tanthauzo lake kwa iwo okusautsani! 20Mtengo munawuona uja, umene unkakulirakulira kwambiri ndi kulimba, ndi msonga yake inafika mlengalenga, ndi kuonekera ku dziko lonse lapansi, 21mtengo umene masamba ake anali okongola ndiponso unali ndi zipatso zochuluka zokwanira kudya anthu onse a dziko lapansi. Mtengowu unkapereka mthunzi ku zirombo zonse zakuthengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinayika zisa pa nthambi zake. 22Inu mfumu, ndinu mtengo umenewo! Inu mwakhala wamkulu ndi wamphamvu; ukulu wanu wakula mpaka wakhudza mlengalenga, ndipo ufumu wanu wafika mpaka ku malo akutali a dziko lapansi.

23“Inu mfumu munaona mthenga woyera, akuchokera kumwamba ndipo anati, ‘Gwetsani mtengo ndipo muwuwononge, koma musiye tsinde ndi mizu yake. Tsindelo mulimange ndi unyolo wa chitsulo ndi mkuwa ndipo mulisiye pakati pa udzu wa mʼmunda. Mulole kuti linyowe ndi mame akumwamba. Likhale ngati nyama zakuthengo, mpaka zaka zidutse zisanu ndi ziwiri.’

24“Tanthauzo lake ndi ili mfumu, izi ndi zimene Mulungu Wammwambamwamba watsimikiza kuti zikugwereni mbuye wanga mfumu: 25Inu mudzachotsedwa pakati pa anthu ndipo mudzakhala ndi nyama zakuthengo; mudzadya udzu monga ngʼombe ndi kunyowa ndi mame akumwamba. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka mudzavomereze kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa ma ufumu a anthu, ndipo amawapereka kwa aliyense amene Iye wafuna. 26Lamulo losiya tsinde la mtengo ndi mizu yake litanthauza kuti ufumu wanu udzabwezeredwa kwa inu mukadzavomereza kuti Mulungu ndiye amalamulira. 27Nʼchifukwa chake mfumu, chikukomereni kulandira malangizo anga: Lekani machimo ndipo muzichita zabwino, lekani mphulupulu zanu ndipo muzikomera mtima anthu opsinjika. Nʼkutheka kuti mtendere wanu udzapitirira.”

Maloto Akwaniritsidwa

28Zonsezi zinamuchitikira mfumu Nebukadinezara. 29Itapita miyezi khumi ndi iwiri, pamene mfumu inkayenda pa denga la nyumba ya ufumu ya ku Babuloni, 30iye anati, “Kodi Babuloni si mzinda wamphamvu ndi wokongola umene ndinamanga ndi mphamvu zanga ngati nyumba yanga yaufumu, kuonetsera ulemerero wa ufumu wanga?”

31Akuyankhulabe izi mawu anamveka kuchokera kumwamba kuti, “Imvani izi, mfumu Nebukadinezara: Ufumu wako wachotsedwa. 32Udzachotsedwa pakati pa anthu ndipo udzakhala ndi zirombo zakuthengo; udzadya udzu monga ngʼombe. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka iwe utavomereza kuti Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene iye afuna.”

33Nthawi yomweyo zonse zimene zinanenedwa zokhudza Nebukadinezara zinakwaniritsidwa. Iye anachotsedwa pakati pa anthu ndipo ankadya udzu ngati ngʼombe. Thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba mpaka tsitsi lake linakula ngati nthenga za chiwombankhanga ndi zikhadabo ngati zikhadabo za mbalame.

34Pomaliza pa zaka zimenezo ine, Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndipo nzeru zanga zinabwereramo. Kenaka ndinatamanda Wammwambamwamba; ndinamupatsa ulemu ndi kumulemekeza Iye amene akhala nthawi zonse.

Ulamuliro wake ndi ulamuliro wa nthawi zonse;

ufumu wake udzakhala ku mibadomibado.

35Anthu onse a dziko lapansi

ali chabe pamaso pake.

Pakati pa angelo akumwamba

ndi anthu a dziko lapansi

palibe amene akhoza kumuletsa

Mulungu kuchita zimene afuna.

Kapena kunena kwa Iye kuti, “Kodi mwachita chiyani?”

36Pa nthawi yomweyo nzeru zanga zinabwereramo. Ndinalandiranso ulemu wanga ndi ufumu wanga. Nduna ndi akalonga anga anandilandiranso. Ndipo anandibwezera ufumu wanga ndi kukhalanso wamphamvu kuposa kale. 37Tsopano ine Nebukadinezara, ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba chifukwa zonse zimene amachita ndi zoyenera ndipo njira zake zonse ndi zachilungamo. Ndipo onse amene amayenda modzikuza adzawatsitsa.

New Serbian Translation

Књига пророка Данила 4:1-37

Други Навуходоносоров сан

1Цар Навуходоносор свим народима, племенима и језицима, који живе по свој земљи:

Нека се умножи ваше благостање!

2Чини ми задовољство да вам кажем о знацима и чудима, које је Бог Свевишњи учинио за мене.

3Како ли су велики његови знаци!

Како ли су силна његова чуда!

Царство његово вечно је царство,

а власт његова траје од нараштаја до нараштаја.

4Ја, Навуходоносор, живео сам спокојно у свом дому, цветајући у свом двору. 5А онда сам уснио сан који ме је преплашио. Док сам био на својој постељи, главом су ми пролазиле слике и виђења која су ме узнемирила. 6Зато сам издао заповест да се доведу сви вавилонски мудраци и да ми саопште тумачење сна. 7Када су дошли чаробњаци, гатари, Халдејци и звездознанци, испричао сам им свој сан, али нису могли да кажу његово тумачење. 8На крају је пред мене дошао Данило, у коме су духови светих богова. (Њему је име и Валтазар, према имену мога бога.) Тада сам му испричао свој сан, говорећи:

9„Валтазаре, главару чаробњака, знам да су у теби духови светих богова, и да ти ниједна тајна не задаје муку. Ево виђења које сам имао, а ти ми реци шта је његово значење. 10У виђењима која су ми на постељи пролазила главом, видео сам једно дрво насред земље; било је веома високо. 11Дрво је порасло и постало моћно. Висином је допирало до неба, тако да се видело са свих крајева земље. 12Лишће му је било предивно, а род обилан. На њему је било хране за све. Под њим су пољске звери налазиле хлад, а на његовим гранама су живеле птице небеске; сва су се створења хранила од њега.

13Док сам гледао виђења која су ми на постељи пролазила главом, гле, с неба сиђе свети стражар. 14Он снажно повика и рече овако: ’Посеците дрво, окрешите му гране, покидајте му лишће и побацајте му род; нека се разбеже звери испод њега и птице са његових грана. 15Ипак, оставите му у земљи пањ с кореном, окован обручем од гвожђа и бронзе, у пољској трави.

Нека га кваси роса небеска и нека са зверима дели траву земаљску. 16Нека му се људско срце промени у срце животињско, и нека седам времена4,16 Или: седам година, као у ст. 23, 25, 32. пређу преко њега.

17То је пресуда коју су стражари одредили, заповест коју су изрекли свети, да би сви живи знали да Свевишњи влада над људским царством. Он га даје коме хоће, и поставља над њим најнижег од људи.’

18То је сан који сам сањао ја, цар Навуходоносор, а ти ми га, Валтазаре, растумачи, пошто ниједан од мудраца у мом царству није могао да ми обзнани његово тумачење. Ипак, ти то можеш, јер је дух светих богова у теби.“

Данило тумачи сан

19На то се Данило, који се још зове и „Валтазар“, на тренутак смео; мисли су га узнемириле. Цар му рече: „Валтазаре, не дај да те узнемири сан и његово значење.“

Валтазар одговори: „Господару мој, нека тај сан буде за твоје мрзитеље, и његово значење за твоје непријатеље! 20Ти си видео дрво које је толико порасло и постало силно, да је висином досегло до неба, па га је цела земља могла видети. 21Лишће му је било предивно, а урод обилан, те је било хране за све. Под њим су пољске звери налазиле хлад, а птице небеске живеле у његовим гранама. 22Ти си, царе, то дрво, јер си постао велики и силан! Величина ти је порасла и досегла до неба, а твоја владавина до краја земље.

23Цар је видео и светог стражара, који је сишао са неба и рекао: ’Посеците дрво и уништите га, али му оставите у земљи пањ с кореном, окованог обручем од гвожђа и бронзе, у пољској трави. Нека га кваси роса небеска и нека са зверима дели траву земаљску, док преко њега не прође седам времена.’

24Ово је тумачење, о, царе: то је одлука Свевишњега, која ће се извршити на мом господару, цару. 25Прогнаће те из људског друштва, и боравиште ће ти бити међу пољским зверињем. Хранићеш се травом као говеда, квасиће те роса небеска, и седам ће времена прећи преко тебе, док не спознаш да Свевишњи влада над људским царством, и да га даје коме хоће. 26А то што су заповедили да се остави пањ с корењем, значи да ће ти се царство вратити кад спознаш да Небеса владају. 27Зато, о, царе, нека ти мој савет буде угодан: реши се својих греха чинећи правду, и својих безакоња милошћу према сиромасима, да би се продужило твоје благостање.“

Испуњење сна

28Све се то догодило Навуходоносору. 29Након дванаест месеци, док је шетао по крову царског двора у Вавилону, 30цар рече: „Није ли ово велики Вавилон, који сам подигао својом силном моћи себи за царску престоницу, на славу свога величанства?“

31Речи су још биле на царевим уснама кад је сишао глас с неба, говорећи: „Одлучено је за тебе, царе Навуходоносоре: одузима ти се царство. 32Прогнаће те из људског друштва, и боравиште ће ти бити међу пољским зверињем. Хранићеш се травом као говеда, и седам ће времена прећи преко тебе, док не увидиш да Свевишњи влада над људским царством, и да га даје коме хоће.“

33Одлука је одмах спроведена. Навуходоносор је био прогнан из људског друштва, јео је траву, квасила га је роса небеска, коса му је нарасла као орловско перје, а нокти као птичје канџе.

34Када се то време навршило, ја, Навуходоносор, подигао сам своје очи према небу и разум ми се вратио. Тада сам благословио Свевишњег, славећи и величајући онога који живи заувек.

Јер његова је владавина вечна владавина,

а његово царство траје од нараштаја до нараштаја.

35Сви становници земље

ништа не представљају;

он чини шта хоће

с небеском војском

и са становницима земље.

Ништа не може да заустави његову руку,

или да му каже: „Шта то радиш?“

36Истог часа ми се вратио разум, а уз моју царску част вратила ми се и слава и сјај. Тада су ме потражили моји саветници и великаши, па ми је било враћено царство. Уз то сам постао још моћнији. 37Сада ја, Навуходоносор, славим и узвисујем небеског цара, чија су сва дела истина, а путеви правда; он је онај који може да понизи оне који ходе охоло.