Chivumbulutso 17 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 17:1-18

Mkazi Wachiwerewere

1Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri. 2Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.”

3Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 4Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake. 5Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa:

BABULONI WAMKULU

MAYI WA AKAZI ADAMA

NDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI.

6Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu.

Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri. 7Kenaka mngelo uja anati kwa ine, “Bwanji ukudabwa? Ndikufotokozera chinsinsi cha mkaziyu ndi chinsinsi cha chirombo chimene wakwerapochi chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 8Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera.

9“Zimenezi zikufunika kuganizira mwanzeru. Mitu isanu ndi iwiriyo ndi mapiri asanu ndi awiri pomwe mkazi uja amakhalirapo. Yomweyonso ndi mafumu asanu ndi awiri. 10Mafumu asanu anagwa, imodzi ilipo ndipo ina sinabwere; koma pamene idzafika, idzayenera kukhala kwa kanthawi kochepa. 11Chirombo chomwe chinalipo kale ndipo tsopano kulibe ndiyo mfumu yachisanu ndi chitatu. Iyo ndi ya mʼgulu la asanu ndi awiriwo ndipo ikupita kukawonongedwa.

12“Nyanga khumi unaziona zija ndi mafumu khumi amene sanapatsidwe ulamuliro, koma adzapatsidwa ulamuliro pamodzi ndi chirombo kwa ora limodzi. 13Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho. 14Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”

15Kenaka mngeloyo anati kwa ine, “Madzi amene unawaona pamene mkazi wadamayo anakhalapo ndiwo anthu ochuluka, mitundu ndi ziyankhulo. 16Nyanga khumi ndi chirombo unazionazo zidzadya mkazi wadamayo. Zidzamufwifwitsa ndi kumusiya wamaliseche; zidzadya nyama yake ndi kumutentha ndi moto. 17Pakuti Mulungu wayika ichi mʼmitima mwawo kuti akwaniritse cholinga chake povomerezana kupereka mphamvu zawo zolamulira kwa chirombo, kufikira Mawu a Mulungu atakwaniritsidwa. 18Mkazi unamuonayo ndi mzinda waukulu umene ulamulira mafumu a dziko lapansi.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

启示录 17:1-18

大淫妇的下场

1拿着七碗的七位天使中有一位前来对我说:“你过来!我要让你看那坐在众水之上的大淫妇将要遭受的刑罚。 2地上的君王与她行淫,地上其他人也因喝了她淫乱的酒而酩酊大醉。”

3那时,我被圣灵感动,被天使带到旷野,在那里见到一个妇人骑着一只朱红色的怪兽。怪兽有七头十角,浑身写满亵渎上帝的名号。 4那妇人身穿紫色和朱红色的袍子,用黄金、宝石及珍珠装扮自己。她手中拿着金杯,里面盛满了她淫乱的污秽、可憎之物。 5在她额上还写了一个神秘的名号:“大巴比伦——地上淫妇及可憎事物之母”。 6我又见她醉了,因她喝了众圣徒的血,就是为耶稣做见证之人的血。

我看见她,非常惊奇。 7天使对我说:“你为什么这样惊奇呢?我要将这妇人和她骑的七头十角怪兽的奥秘告诉你。 8你看见的这怪兽以前出现过,现今没有出现,将来要从无底坑上来,然后走向灭亡。那些住在地上、自创世以来名字没有记在生命册上的人,都因见到这只从前出现过、现今没有出现、将来会再出现的怪兽而感到惊奇。 9这里需要智慧才能明白,它的七个头代表那妇人坐镇的七座山,又代表七个王。 10其中五个已经衰亡,一个还在,另外一个还未来到,他来后只能短暂存留。 11那从前出现过、现今没有出现的怪兽是第八个王,他是七个王之一,也要走向灭亡。 12你看见的那十个角象征另外十个还没有得势的王,他们将取得王权和那怪兽一同统治短暂的一段时期。 13他们一致同意把自己所有的能力和权柄交给那怪兽。 14他们将与羔羊交战,但羔羊必胜过他们,因为羔羊是万主之主,万王之王。那些跟随羔羊的是被呼召、蒙拣选、忠心耿耿的人。”

15天使又对我说:“你看见的那淫妇所坐的众水象征来自各民族、各国家、各语言族群的人。 16怪兽和它头上的十角必憎恨那淫妇,使她赤身露体、景况凄凉。它们要吃她的肉,最后用火将她烧尽。 17因为上帝使众王定意这样做,好完成祂的旨意。他们便同心将政权交给那怪兽,直到上帝的话得到实现。 18你看见的那妇人就是那掌管世上众王的大城。”