Chivumbulutso 10 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 10:1-11

Mngelo ndi Kabuku

1Kenaka ndinaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba. Anavala mtambo ndipo anali ndi utawaleza pamutu pake. Nkhope yake inali ngati dzuwa, ndipo miyendo yake inali ngati mizati yamoto. 2Mʼdzanja lake munali kabuku kakangʼono kotsekulidwa. Phazi lake lamanja linaponda mʼnyanja ndipo phazi lake lamanzere linaponda pa mtunda. 3Mngeloyo anafuwula kwambiri ngati kubangula kwa mkango. Atangofuwula, kunamveka kugunda kwa mabingu asanu ndi awiri. 4Mabingu asanu ndi awiriwo atangogunda, ine ndinkati ndizilemba; koma ndinamva mawu kuchokera kumwamba kuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi awiriwo anena ndipo usazilembe.”

5Kenaka mngelo amene ndinamuona ataponda mʼnyanja ndi ku mtunda uja, anakweza dzanja lake lamanja kumwamba. 6Mngeloyo analumbira mʼdzina la Iye wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene analenga kumwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo, nati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano! 7Koma patsala pangʼono kuti mngelo wachisanu ndi chiwiri uja awombe lipenga lake, chinsinsi cha Mulungu chidzachitika monga momwe analengezera kwa atumiki ake, aneneri.”

8Pamenepo mawu amene ndinamva kuchokera kumwamba aja, anandiyankhulanso, anati, “Pita katenge buku lotsekulidwalo mʼdzanja la mngelo amene waponda pa nyanja ndi pa mtundayo.”

9Choncho ndinapita kwa mngeloyo ndipo ndinamupempha kuti andipatse kabukuko. Iye anati, “Tenga, idya. Mʼmimba mwako kaziwawa koma mʼkamwa mwako kazizuna ngati uchi.” 10Ndinatenga kabukuko mʼdzanja la mngeloyo ndipo ndinadyadi. Mʼkamwa mwanga kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, mʼmimbamu munkawawa. 11Ndipo anandiwuza kuti, “Iwe uyenera kulalikiranso za mitundu yambiri ya anthu, za mayiko, ziyankhulo ndi za mafumu.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

啟示錄 10:1-11

天使與小書卷

1我看見另一位大力天使從天而降。他身披雲霞,頭頂彩虹,臉如太陽,雙腿如火柱, 2手中拿著一卷打開了的小書卷,右腳踏在海中,左腳踏在地上。 3他大喊的時候,聲如獅吼,之後有七聲雷鳴。 4我正要將雷鳴的意思記錄下來,就聽見天上有聲音說:「你要封住七聲雷鳴所說的事,別寫下來。」

5我剛才所見的那位腳踏海洋和陸地的天使向天舉起右手, 6憑著活到永永遠遠、創造天地海洋和其中一切的上帝起誓說:「必不再耽延了。 7等第七位天使吹響號角時,上帝奧祕的計劃就實現了,正如上帝向祂的奴僕——眾先知所宣告的。」

8先前從天上對我說話的聲音又吩咐我:「你去,從那位腳踏海洋陸地的天使手中把展開的小書卷拿來。」

9於是,我走到那天使面前,請他將小書卷給我。他對我說:「拿去,把它吃了。你的腹中會感到苦澀,可是你口中會覺得甘甜如蜜。」 10我就從天使手中接過小書卷,將它吃了,我口中果然甘甜如蜜,之後腹中覺得苦澀。 11那天使又對我說:「你必要再對許多民族、國家、語言族群、君王說預言。」