Aroma 10 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aroma 10:1-21

1Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe. 2Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso. 3Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu. 4Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.

5Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.” 6Koma chilungamo cha chikhulupiriro chikuti, “Usanene mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndani amene akwere kumwamba?’ ” (ndiko, kukatsitsa Khristu) 7“kapena ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’ ” (ndiko, kukamutenga Khristu kwa akufa). 8Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira, 9kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. 10Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa. 11Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.” 12Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye 13pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”

14Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo? 15Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”

16Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?” 17Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu. 18Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti,

“Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi.

Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”

19Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti,

“Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake.

Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”

20Ndipo Yesaya molimba mtima akuti,

“Anandipeza anthu amene sanali kundifunafuna.

Ndinadzionetsera kwa amene sanafunse za Ine.”

21Koma zokhudzana ndi Aisraeli akuti,

“Tsiku lonse ndinatambasulira manja anga

kwa anthu osandimvera ndi okanika.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

罗马书 10:1-21

1弟兄姊妹,我心里切望并向上帝祈求的,就是以色列人能够得救。 2我可以证明,他们对上帝有热心,但不是基于真知。 3他们不知道上帝所赐的义,想努力建立自己的义,不肯服从上帝的义。 4其实基督是律法的终极目的,使所有信靠祂的人都可以得到义。

求告主名的都必得救

5关于律法的义,摩西写道:“人若遵行律法的诫命,就必活着。” 6但是论到以信心为基础的义,圣经上说:“不要心里说,‘谁要升到天上去呢?’意思是谁要把基督领下来, 7或说,‘谁要下到阴间去呢?’意思是谁要把基督从死人中领上来。” 8其实这里是说:“这道近在咫尺,就在你口里,在你心中。”这道就是我们所传的信主之道。 9你若口里承认耶稣是主,心里相信上帝使祂从死里复活,就必得救。 10因为人心里相信,就可以被称为义人,口里承认,就可以得救。 11正如圣经上说:“信靠祂的人必不致蒙羞。” 12犹太人和希腊人并没有分别,因为主是所有人的主,祂厚待所有求告祂的人, 13因为“凡求告主名的都必得救。”

14可是,人还没信祂,怎能求告祂呢?还没听说过祂,怎能信祂呢?没有人传道,怎能听说过祂呢? 15人没有受差遣,怎能传道呢?正如圣经上说:“那传福音之人的脚踪是何等佳美!” 16只是并非人人都信福音,就像以赛亚先知所说的:“主啊!谁相信我们所传的呢?”

17由此可见,听了道,才会信道;有了基督的话,才有道可听。 18但我要问,以色列人没有听过吗?当然听过。因为

“他们的声音传遍天下,

他们的话语传到地极。”

19我再问,难道以色列人不知道吗?首先,摩西说:

“我要借无名之民挑起你们的嫉妒,

用愚昧的国民激起你们的怒气。”

20后来,以赛亚先知又放胆地说:

“我让没有寻找我的人寻见,

我向没有求问我的人显现。”

21至于以色列人,他说:

“我整天伸出双手招呼那悖逆顽固的百姓。”