Akolose 4 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Akolose 4:1-18

1Mabwana, antchito anu muzikhala nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziwa kuti nanunso muli nawo Ambuye anu mmwamba.

Malangizo Ena

2Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika. 3Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende. 4Pempherani kuti ndilalikire momveka bwino, monga ndikuyenera. 5Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo. 6Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.

Mawu Otsiriza

7Tukiko adzakuwuzani zonse za ine. Iye ndi mʼbale wokondedwa, mtumiki wokhulupirika ndiponso wantchito mnzanga mwa Ambuye. 8Ine ndikumutumiza kwa inu ndi cholinga choti mudziwe zimene tikukumana nazo ndiponso kuti alimbikitse mitima yanu. 9Iye akubwera ndi Onesimo, mʼbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ndi mmodzi mwa inu. Iwo adzakuwuzani zonse zimene zikuchitika kuno.

10Aristariko, wamʼndende mnzanga akupereka moni, Marko akuperekanso moni, msuweni wa Barnaba. (Inu munawuzidwa kale za Iye. Iye akabwera kwanuko, mulandireni). 11Yesu wotchedwa Yusto, akuperekanso moni. Amenewa ndi Ayuda okhawo pakati pa atumiki anzanga mu ufumu wa Mulungu, ndipo aonetsa kuti ndi chitonthozo kwa ine. 12Epafra ndi mmodzi mwa inu ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu, akupereka moni. Iyeyu nthawi zonse amakupemphererani mwamphamvu, kuti mukhazikike pa chifuniro chonse cha Mulungu, mukhale okhwima ndi otsimikiza kwathunthu. 13Ine ndikumuchitira umboni kuti amagwira ntchito mwamphamvu chifukwa cha inu ndiponso kwa amene ali ku Laodikaya ndi Herapoli. 14Luka, dotolo wathu wokondedwa ndi Dema, akupereka moni. 15Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake.

16Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya.

17Uzani Arkipo kuti, “Wonetsetsa kuti wamaliza ntchito imene unayilandira mwa Ambuye.”

18Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa moni uwu. Kumbukirani kuti ndili mu unyolo. Chisomo chikhale ndi inu.

Slovo na cestu

Koloským 4:1-18

1Na druhé straně vy, kteří máte pravomoc, buďte ke svým podřízeným spravedliví a nestranní. Nezapomeňte, že i vy máte Pána nad sebou. 2V modlitbách buďte vytrvalí a v děkování Bohu neúnavní. 3-4Modlete se i za nás, aby nám Bůh otevřel dveře k hlásání jeho poselství a dal nám i ochotné posluchače. Proste, abych mohl bez překážek pokračovat v osvětlování Kristova poselství, jak mi Bůh uložil a za co jsem právě ve vězení.

Jen prožité působí věrohodně

5Ve styku s lidmi, kteří nepatří k církvi, jednejte moudře a využívejte vhodné příležitosti, pokud je čas. 6Vaše řeč ať je vždycky přívětivá a výstižná; pak v ní každý nalezne pro sebe správnou odpověď.

7Můj drahý přítel Tychikus vám podrobně vylíčí, jak to se mnou vypadá. Věrně mi pomáhá v mé službě Pánu. Od něj budete mít nejpřesnější zprávy. 8Proto ho posílám, abyste nebyli zbytečně znepokojeni starostmi o můj osud. 9Provází ho váš krajan Onezimus, se kterým jsme se velmi sblížili. Ti vám všechno povědí.

10Pozdravuje vás můj spoluvězeň Aristarchos a Barnabášův bratranec Marek, o kterém jsem vám už psal; pokud k vám přijde, přijměte ho srdečně. 11Pozdravuje vás také Ježíš Justus. Tito tři jsou jediní ze židů, kteří zde se mnou spolupracují na Božím díle a jsou mi oporou.

12Dále vám posílá pozdrav váš krajan Epafras. Je to vskutku horlivý Kristův služebník a nepřetržitě se za vás modlí, abyste byli ve víře pevní a dovedli rozeznat Boží vůli ve všem, co děláte. 13A stejně jako vy mu leží na srdci i křesťané v Laodiceji a Hierapoli. 14I náš milý lékař Lukáš vás pozdravuje, a ještě Démas. 15Pozdravujte všechny v Laodiceji, hlavně Nymfu a ostatní, kteří se scházejí v jejím domě. 16Až tento dopis přečtete, pošlete ho do Laodiceje, ať se s ním seznámí i tam. A vy si zase vyžádejte dopis, který jsem napsal jim. 17Archippovi vyřiďte, ať svědomitě zastává službu, kterou byl pověřen.

18Nakonec připisuji pozdrav vlastní rukou. Myslete na moje pouta. Bůh vám žehnej.

Váš Pavel