Ahebri 11 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ahebri 11:1-40

Za Chikhulupiriro cha anthu Akale

1Tsopano chikhulupiriro ndi kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndi kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu. 2Ndi chikhulupiriro chimenechi makolo athu akale anayamikidwa.

3Ndi chikhulupiriro timazindikira kuti dziko lapansi ndi la mmwamba zinapangidwa ndi Mawu a Mulungu, ndikuti zinthu zoonekazi zinachokera ku zinthu zosaoneka. 4Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa imene Kaini anapereka. Ndi chikhulupiriro anatchedwa munthu wolungama Mulungu atayamikira zopereka zake. Ngakhale iye anafa, akuyankhulabe chifukwa cha chikhulupiriro chakecho.

5Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa wamoyo, motero iye sanalawe imfa; sanapezeke chifukwa Mulungu anamutenga. Pakuti asanatengedwe anayamikiridwa kuti ankakondweretsa Mulungu. 6Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.

7Ndi chikhulupiriro, Nowa atachenjezedwa za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anachita mantha napanga chombo kuti apulumutsire banja lake. Ndi chikhulupiriro chake anatsutsa dziko lapansi ndipo analandira chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.

8Ndi chikhulupiriro Abrahamu atayitanidwa kuti apite ku dziko limene anamulonjeza kuti lidzakhala lake, anamvera ndi kupita, ngakhale sanadziwe kumene ankapita. 9Ndi chikhulupiriro chomwecho anakhala ngati mlendo mʼdziko lija limene Mulungu anamulonjeza. Anakhala mʼmatenti monganso anachitira Isake ndi Yakobo, amene nawonso analonjezedwanso. 10Pakuti amadikira mudzi wokhala ndi maziko, umene mmisiri ndi womanga wake ndi Mulungu.

11Ndi chikhulupiriro Sara analandira mphamvu zokhala ndi pakati ngakhale kuti zaka zake zobala mwana zinali zitapita kale, popeza anamutenga amene analonjeza kukhala wokhulupirika. 12Nʼchifukwa chake mwa munthu mmodzi, amene anali ngati wakufa, munatuluka mibado yochuluka ngati nyenyezi ndi yosawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.

13Onsewa anakhalabe mwachikhulupiriro mpaka anafa. Iwo sanalandire zimene Mulungu anawalonjeza; iwo anangozionera chapatali ndi kuzilandira. Ndipo iwo anavomereza kuti analidi alendo ndi osakhazikika pa dziko lapansi. 14Anthu amene amanena zinthu zotere amaonekeratu kuti akufuna dziko lawo lenileni. 15Akanakhala kuti akuganizira za dziko limene analisiya akanapeza mpata obwerera kwawo. 16Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.

17Ndi chikhulupiriro Abrahamu, Mulungu atamuyesa, anapereka Isake ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu anamulonjeza, anakhala wokonzeka kupereka nsembe mwana wake mmodzi yekhayo. 18Za mwana ameneyu Mulungu anamuwuza iye kuti, “Zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.” 19Abrahamu amazindikira kuti Mulungu angathe kuukitsa akufa, ndipo tingathe kunena mofanizira kuti iye analandiranso Isake ngati wouka kwa akufa.

20Ndi chikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau pa zatsogolo lawo.

21Ndi chikhulupiriro, pamene Yakobo ankamwalira anadalitsa ana awiri a Yosefe, ndipo anapembedza Mulungu atatsamira ndodo yake.

22Ndi chikhulupiriro Yosefe ali pafupi kumwalira anayankhula za kutuluka kwa Aisraeli mu Igupto ndipo anawawuza zoti adzachite ndi mafupa ake.

23Ndi chikhulupiriro Mose atabadwa makolo ake anamubisa miyezi itatu, chifukwa iwo anaona kuti mwanayo anali wokongola ndipo sanaope konse lamulo la mfumu.

24Ndi chikhulupiriro Mose atakula, anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao. 25Iye anasankha kuzunzika nawo limodzi anthu a Mulungu kuposa kusangalala ndi zokondweretsa za uchimo kwa nthawi yochepa. 26Anaona kuti kuzunzika chifukwa cha Khristu kunali kwa mtengowapatali kuposa chuma cha ku Igupto, chifukwa amaona mphotho ya mʼtsogolo. 27Ndi chikhulupiriro anachoka ku Igupto wosaopa ukali wa mfumu. Iye anapirira chifukwa anamuona Mulungu amene ndi wosaonekayo. 28Ndi chikhulupiriro anachita Paska ndi kuwaza magazi, kuti mngelo wowononga ana oyamba kubadwa asaphe ana oyamba kubadwa a Aisraeli.

29Ndi chikhulupiriro Aisraeli anawoloka Nyanja Yofiira ngati pa mtunda powuma, koma Aigupto atayesa kutero anamizidwa.

30Ndi chikhulupiriro mpanda wa Yeriko unagwa, Aisraeli atawuzungulira kasanu ndi kawiri.

31Ndi chikhulupiriro Rahabe, mkazi wadama sanaphedwe pamodzi ndi osamvera aja chifukwa analandira bwino ozonda aja ku nyumba kwake.

32Kodi ndinenenso chiyani? Nthawi yandichepera yoti ndinene za Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita, Davide, Samueli ndi aneneri, 33amene ndi chikhulupiriro anagonjetsa mafumu, anakhazikitsa chilungamo ndi kulandira zimene zinalonjezedwa. Anatseka pakamwa pa mikango, 34anazimitsa moto waukali, ndipo anapulumuka osaphedwa ndi lupanga. Anali ofowoka koma analandira mphamvu; anasanduka amphamvu pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani awo. 35Amayi ena analandira anthu awo amene anafa, ataukitsidwanso. Enanso anazunzidwa ndipo anakana kumasulidwa, kuti adzaukenso ndi moyo wabwino. 36Ena anawaseka ndi kuwakwapula, pamenenso ena anamangidwa ndi kupita ku ndende. 37Anagendedwa miyala; anachekedwa pakati; ena anaphedwa ndi lupanga. Iwo anayendayenda atavala zikopa zankhosa ndi zikopa zambuzi, umphawi okhaokha, ozunzidwa ndi kuvutitsidwa. 38Dziko lapansi silinawayenere. Anayendayenda mʼzipululu ndi mapiri, ndiponso mʼmapanga ndi mʼmaenje.

39Onsewa anayamikidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, komabe palibe wa iwo amene analandira zimene analonjezedwa. 40Mulungu anatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe angwiro popanda ife.

King James Version

Hebrews 11:1-40

1Now faith is the substance of things hoped for, the evidence of things not seen. 2For by it the elders obtained a good report. 3Through faith we understand that the worlds were framed by the word of God, so that things which are seen were not made of things which do appear. 4By faith Abel offered unto God a more excellent sacrifice than Cain, by which he obtained witness that he was righteous, God testifying of his gifts: and by it he being dead yet speaketh. 5By faith Enoch was translated that he should not see death; and was not found, because God had translated him: for before his translation he had this testimony, that he pleased God. 6But without faith it is impossible to please him: for he that cometh to God must believe that he is, and that he is a rewarder of them that diligently seek him. 7By faith Noah, being warned of God of things not seen as yet, moved with fear, prepared an ark to the saving of his house; by the which he condemned the world, and became heir of the righteousness which is by faith. 8By faith Abraham, when he was called to go out into a place which he should after receive for an inheritance, obeyed; and he went out, not knowing whither he went. 9By faith he sojourned in the land of promise, as in a strange country, dwelling in tabernacles with Isaac and Jacob, the heirs with him of the same promise: 10For he looked for a city which hath foundations, whose builder and maker is God. 11Through faith also Sara herself received strength to conceive seed, and was delivered of a child when she was past age, because she judged him faithful who had promised. 12Therefore sprang there even of one, and him as good as dead, so many as the stars of the sky in multitude, and as the sand which is by the sea shore innumerable. 13These all died in faith, not having received the promises, but having seen them afar off, and were persuaded of them, and embraced them, and confessed that they were strangers and pilgrims on the earth. 14For they that say such things declare plainly that they seek a country. 15And truly, if they had been mindful of that country from whence they came out, they might have had opportunity to have returned. 16But now they desire a better country, that is, an heavenly: wherefore God is not ashamed to be called their God: for he hath prepared for them a city. 17By faith Abraham, when he was tried, offered up Isaac: and he that had received the promises offered up his only begotten son, 18Of whom it was said, That in Isaac shall thy seed be called: 19Accounting that God was able to raise him up, even from the dead; from whence also he received him in a figure. 20By faith Isaac blessed Jacob and Esau concerning things to come. 21By faith Jacob, when he was a dying, blessed both the sons of Joseph; and worshipped, leaning upon the top of his staff. 22By faith Joseph, when he died, made mention of the departing of the children of Israel; and gave commandment concerning his bones. 23By faith Moses, when he was born, was hid three months of his parents, because they saw he was a proper child; and they were not afraid of the king’s commandment. 24By faith Moses, when he was come to years, refused to be called the son of Pharaoh’s daughter; 25Choosing rather to suffer affliction with the people of God, than to enjoy the pleasures of sin for a season; 26Esteeming the reproach of Christ greater riches than the treasures in Egypt: for he had respect unto the recompence of the reward. 27By faith he forsook Egypt, not fearing the wrath of the king: for he endured, as seeing him who is invisible. 28Through faith he kept the passover, and the sprinkling of blood, lest he that destroyed the firstborn should touch them. 29By faith they passed through the Red sea as by dry land: which the Egyptians assaying to do were drowned. 30By faith the walls of Jericho fell down, after they were compassed about seven days. 31By faith the harlot Rahab perished not with them that believed not, when she had received the spies with peace. 32And what shall I more say? for the time would fail me to tell of Gedeon, and of Barak, and of Samson, and of Jephthae; of David also, and Samuel, and of the prophets: 33Who through faith subdued kingdoms, wrought righteousness, obtained promises, stopped the mouths of lions, 34Quenched the violence of fire, escaped the edge of the sword, out of weakness were made strong, waxed valiant in fight, turned to flight the armies of the aliens. 35Women received their dead raised to life again: and others were tortured, not accepting deliverance; that they might obtain a better resurrection: 36And others had trial of cruel mockings and scourgings, yea, moreover of bonds and imprisonment: 37They were stoned, they were sawn asunder, were tempted, were slain with the sword: they wandered about in sheepskins and goatskins; being destitute, afflicted, tormented; 38(Of whom the world was not worthy:) they wandered in deserts, and in mountains, and in dens and caves of the earth. 39And these all, having obtained a good report through faith, received not the promise: 40God having provided some better thing for us, that they without us should not be made perfect.