Agalatiya 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Agalatiya 4:1-31

1Chimene ndikunena ndi chakuti, ngati mlowamʼmalo akali wamngʼono, sasiyana ndi kapolo, ngakhale kuti chuma chonse ndi chake. 2Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso anthu oyangʼanira chuma mpaka nthawi imene abambo ake anakhazikitsa. 3Chomwechonso, ife pamene tinali ana, tinali akapolo a miyambo ya dziko lapansi. 4Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, wobadwa mwa mayi, wobadwa pansi pa lamulo, 5kudzawombola amene anali pansi pa lamulo, kuti tilandiridwe monga ana. 6Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti, “Abba, Atate.” 7Choncho sindiwenso kapolo, koma mwana wa Mulungu. Tsono popeza ndiwe mwana wake, Mulungu wakusandutsanso mlowamʼmalo.

Nkhawa ya Paulo chifukwa cha Agalatiya

8Koma poyamba pamene simunkamudziwa Mulungu, munali akapolo a zimene mwachilengedwe si milungu. 9Koma tsopano pakuti mukumudziwa Mulungu, kapena ndinene kuti Mulungu akukudziwani, nʼchifukwa chiyani mukubwereranso ku miyambo yofowoka ndi yomvetsa chisoni? Kodi mukufuna musandukenso akapolo? 10Mumasunga masiku, miyezi ndi nyengo ndi zaka. 11Ine ndikuopa kuti mwina ntchito zanga pa inu ndinagwira pachabe.

12Abale, ndikukudandaulirani, mukhale ngati ine, popeza ine ndinakhala ngati inu. Inu simunandilakwire. 13Monga inu mukudziwa ndinkakulalikirani Uthenga Wabwino ndili wofowoka. 14Ngakhale kuti matendawo anali ngati mayesero kwa inu, simunandinyoze kapena kunyansidwa nane. Komatu inu munandilandira ngati kuti ndinali mngelo wa Mulungu, ngati kuti ndinali Khristu Yesu mwini. 15Kodi chimwemwe chanu chonse chija chili kuti? Ine nditha kuchitira umboni kuti, ngati kukanatheka, inu mukanakolowola maso anu ndi kundipatsa. 16Kodi tsopano ine ndasanduka mdani wanu chifukwa ndakuwuzani choonadi?

17Anthu amenewo akuchita changu kuti akukopeni, koma changu chawocho sichabwino. Chimene iwo akufuna ndi chakuti akuchotseni inu kwa ife, kuti mukachite changu powathandiza iwowo. 18Nʼkwabwino kuchita changu, ngati cholingacho chili chabwino ndi kukhala otero nthawi zonse osati pokhapo pamene ine ndili ndi inu. 19Ana anga okondedwa, inu amene ine ndikukumveraninso zowawa za kubereka kufikira Khristu atawumbidwa mwa inu, 20ine ndikanakonda ndikanakhala nanu tsopano kuti ndisinthe mawu anga, chifukwa ndathedwa nanu nzeru.

Hagara ndi Sara

21Tandiwuzani, inu, abale amene mukufuna kukhala pansi pa lamulo, kodi simukudziwa chimene lamulo limanena? 22Pakuti zinalembedwa kuti Abrahamu anali ndi ana aamuna awiri, wina mayi wake anali kapolo ndipo wina mayi wake anali mfulu. 23Mwana wake wobadwa mwa kapolo anabadwa mwathupi; koma mwana wake wobadwa mwa mfulu anabadwa monga mwa lonjezo.

24Zinthu izi zinali ngati fanizo, pakuti amayi awiriwa akuyimira mapangano awiri. Pangano limodzi ndi lochokera mʼPhiri la Sinai, ndiye Hagara, ndipo amabereka ana amene ndi akapolo. 25Tsono Hagara, akuyimira Phiri la Sinai ku Arabiya amene afanizidwa ndi mzinda wa Yerusalemu wa lero, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake. 26Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mayi wathu. 27Pakuti kwalembedwa kuti,

“Sangalala, iwe mayi wosabala,

amene sunabalepo mwana;

imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe,

iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;

chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri

kuposa mkazi wokwatiwa.”

28Tsono inu abale, ndinu ana alonjezo ngati Isake. 29Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero. 30Kodi Malemba akuti chiyani? “Muchotse kapoloyo pamodzi ndi mwana wake, chifukwa mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wamfulu.” 31Chifukwa chake, abale, ife sindife ana akapolo, koma ana a mfulu.