Afilipi 3 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Afilipi 3:1-21

Osakhulupirira za Thupi

1Abale anga, ndikupitiriza kunena kuti, kondwani mwa Ambuye! Sizondivuta kuti ndilembenso mawu omwewo, ndipo zimenezi nʼzokuthandizani inuyo.

2Chenjerani ndi agalu amenewa, anthu ochita zoyipa, anthu amene amadula thupi lawo. 3Pakuti ochita mdulidwe weniweni ndife. Ife amene timatumikira Mulungu motsogozedwa ndi Mzimu. Ife amene timanyadira Khristu, ndipo sitidalira zinthu za thupi 4ngakhale kuti ineyo ndili ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupizo.

Ngati pali winanso amene akuganiza kuti ali ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupi, ineyo ndili ndi zifukwa zoposa pamenepo. 5Ndinachita mdulidwe pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditangobadwa. Ndine wa mtundu wa Israeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa Ahebri, kunena za malamulo, ndinali Mfarisi. 6Kunena za changu changa, ndinkazunza mpingo. Kunena za chilungamo chopezeka chifukwa chotsata malamulo, ineyo ndinali wopanda cholakwa.

7Koma zonse zimene ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziona kuti nʼzosapindulitsa chifukwa cha Khristu. 8Kuwonjeza pamenepo, ndikuziona zonse kuti nʼzopanda phindu poyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu Ambuye anga. Nʼchifukwa cha Yesuyo ndataya zinthu zonse ndipo ndikuziyesa zinyalala kuti ndipindule Khristu 9ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro. 10Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake 11kuti nanenso ndidzaukitsidwe kwa akufa.

Kuthamanga Mpaka Kumapeto pa Mpikisano wa Liwiro

12Sikuti ndazipeza kale zonsezi, kapena kuti ndakhala kale wangwiro, koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuti ndipeze chimene Khristu Yesu anandiyitanira. 13Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga. 14Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.

Kutsanzira Paulo

15Choncho ife tonse amene tili okhwima pa moyo wauzimu, tikhale ndi maganizo omwewa. Ndipo ngati pena ndi pena muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa, pameneponso Mulungu adzakuwunikirani. 16Tiyeni ife tizikhala mogwirizana ndi zimene tinapeza kale basi.

17Abale, nonsenu pamodzi mudzinditsanzira ine, ndipo monga inu muli ndi chitsanzo, phunzirani kwa amene akukhala moyo motsatira momwe timakhalira. 18Pakuti monga ndakhala ndikukuwuzani kawirikawiri mʼmbuyomu, ndipo tsopano ndikunenanso ndi misozi kuti, anthu ambiri akukhala monga adani a mtanda wa Khristu. 19Mapeto awo ndi chiwonongeko, mulungu wawo ndi mimba zawo, ndipo ulemerero wawo ndi manyazi awo. Mtima wawo uli pa zinthu za dziko lapansi. 20Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu. 21Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

腓立比书 3:1-21

认识基督最宝贵

1弟兄姊妹,你们要靠主喜乐!我再把这些事写给你们,对我来说并不麻烦,对你们却有好处。 2你们要提防那些犬类,那些作恶的人,那些鼓吹必须受割礼3:2 割礼”参见创世记17章;希腊文用夸张的字眼描述割礼,有讽刺之意。才能得救的人。 3因为真正受割礼的人是我们这些靠着上帝的灵敬拜、以基督耶稣为荣、不倚靠自身条件的人。 4其实我也可以靠自身的条件。如果别人觉得可以靠自身的条件,我更可以。 5我出生后第八天就受了割礼,我是以色列人,属于便雅悯支派,是地地道道的希伯来人。论守律法,我是法利赛人; 6论热心,我曾经迫害教会;论律法要求的义,我是无可指责的。 7但是为了基督,我从前以为有价值的,现在认为毫无价值。 8不但如此,我看万事都毫无价值,因为认识我主基督耶稣最宝贵。我为祂失去了一切,我把失去的一切视为垃圾,好得到基督, 9与祂联合。我成为义人不是因为遵行律法,而是因为信靠基督。这义从上帝而来,以信为基础。 10我渴望认识基督和祂复活的大能,与祂一同受苦,甚至到死的地步3:10 甚至到死的地步”或译“效法祂的死”。11这样我无论如何都可以从死里复活。

直奔标竿

12这并不是说我已经得到了或者纯全了,我还要竭力追求,或者可以达到基督耶稣要我达到的目标。 13弟兄姊妹,我并非以为自己已经得到了,我只专注一件事,就是忘记背后,努力向前, 14直奔目标,要赢得上帝借着基督耶稣从天上呼召我去得的奖赏。 15我们中间成熟的基督徒都应该有这样的看法。即使你们在什么事上看法不同,上帝也必让你们明白。 16然而,我们长进到什么程度,就照着什么程度去行。

17弟兄姊妹,你们要一同效法我,也要向那些以我们为榜样的人学习。 18我已经多次告诉你们,现在又流着泪提醒你们:有许多人行事为人与基督的十字架为敌。 19他们的神就是自己的肚腹,他们以自己的羞耻为荣,只想着地上的事,他们的结局是灭亡。 20我们却是天上的国民,殷切等候从天降临的救主,就是主耶稣基督。 21那时,祂要以降服万物的大能将我们这卑贱的躯体改变成像祂那样荣耀的身体。