Aefeso 3 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aefeso 3:1-21

Paulo Mlaliki wa Anthu a Mitundu Ina

1Nʼchifukwa chake ine Paulo, ndili wamʼndende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu anthu a mitundu ina.

2Ndithudi, inu munamva za ntchito yachisomo cha Mulungu imene anandipatsa chifukwa cha inu, 3ndicho chinsinsi chimene chinawululidwa kwa ine mwa vumbulutso, monga ndinakulemberani kale mwachidule. 4Pamene mukuwerenga izi, inu mudzazindikira za chidziwitso changa pa chinsinsi cha Khristu, 5chimene sichinawululidwe kwa anthu amibado ina monga momwe tsopano chawululidwa ndi Mzimu wa Mulungu mwa atumwi oyera ndi aneneri. 6Chinsinsicho nʼchakuti, kudzera mu Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina ndi olowamʼmalo pamodzi ndi Aisraeli, ndi ziwalo za thupi limodzi, ndi olandira nawo pamodzi malonjezo a mwa Khristu Yesu.

7Mwachisomo cha Mulungu ndi mphamvu zake, ine ndinasanduka mtumiki wa Uthenga Wabwinowu. 8Ngakhale ndili wamngʼono kwambiri pakati pa anthu onse a Mulungu, anandipatsa chisomo chimenechi cholalikira kwa anthu a mitundu ina chuma chopanda malire cha Khristu. 9Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse. 10Cholinga chake tsopano nʼchakuti, kudzera mwa mpingo, mafumu ndi a ulamuliro onse a kumwamba adziwe nzeru zochuluka za Mulungu. 11Chimenechi chinali chikonzero chamuyaya cha Mulungu, chimene chinachitika kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye athu. 12Mwa Khristu ndi mwa chikhulupiriro chathu mwa Iye, timayandikira kwa Mulungu momasuka ndi molimbika mtima. 13Choncho, ine ndikukupemphani kuti musakhumudwe popeza ndikusautsidwa chifukwa cha inu pakuti masautso angawa ndi ulemerero wanu.

Paulo Apempherera Aefeso

14Nʼchifukwa chake ine ndikugwada pamaso pa Atate, 15amene banja lililonse kumwamba ndi pa dziko lapansi limatchulidwa ndi dzina lawo. 16Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake, 17kuti Khristu akhazikike mʼmitima mwanu mwachikhulupiriro. Ndipo ndikukupemphererani kuti muzikike ndi kukhazikika mʼchikondi 18kuti mukhale ndi mphamvu, kuti pamodzi ndi anthu oyera mtima onse muthe kuzindikira kupingasa, kutalika ndi kukwera komanso kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. 19Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.

20Tsopano kwa Iye amene angathe kuchita zochuluka kuposa zimene tingapemphe, kapena kuganiza molingana ndi mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwa ife, 21Iyeyo akhale ndi ulemu mu mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibado yonse mpaka muyaya. Ameni.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以弗所書 3:1-21

外族人的福音使者

1為此,我保羅為了把基督耶穌傳給你們外族人而作了囚犯。 2相信你們已經聽說了,上帝委派我將祂的恩典傳給你們。 3祂藉著啟示讓我明白福音的奧祕,正如我前面簡要提過的。 4你們讀過之後,就能明白我對基督的奧祕有深刻的認識。 5自古以來,上帝沒有讓人知道這奧祕,如今祂藉著聖靈將這奧祕啟示給祂的聖使徒和先知。 6這奧祕就是外族人能夠在基督耶穌裡藉著福音與以色列人同作後嗣,同為一體,同享應許。

7上帝運用大能賜給我恩典,叫我成為這福音的使者。 8我本來比最卑微的聖徒還卑微,卻蒙上帝賜我這恩典,讓我把基督那測不透的豐富傳給外族人, 9讓全人類都明白世代隱藏在創造萬物的上帝裡面的奧祕, 10目的是為了透過教會讓天上的執政者和掌權者現在可以看出上帝豐富的智慧。 11這是上帝萬世以前在我們主基督耶穌裡定好的計劃。 12我們靠著基督、藉著信祂可以坦然無懼、毫無疑慮地來到上帝面前。 13所以,我請求各位不要因我為你們受苦而沮喪,這其實是你們的榮耀。

基督的愛

14-15為此,我跪在天地萬物的本源——天父面前, 16祈求祂按照自己豐富的榮耀,藉著祂的靈,以大能使你們內在的生命剛強起來, 17使基督藉著你們的信心住在你們心裡,使你們在愛中扎根、堅立, 18以便能夠與眾聖徒一同領悟基督的愛是多麼長闊高深, 19並知道基督的愛是遠超過人所能理解的愛,好叫上帝無限的豐富充滿你們。

20上帝的能力運行在我們裡面,能夠豐豐富富地成就一切,超過我們所求所想的。 21願祂在教會中,在基督耶穌裡得到榮耀,直到世世代代,永永遠遠。阿們!