2 Samueli 12 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 12:1-31

Natani Adzudzula Davide

1Tsono Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Atafika kwa Davide anati, “Panali anthu awiri mʼmizinda ina, wina wolemera ndi wina wosauka. 2Munthu wolemerayo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, 3koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo.

4“Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.”

5Davide anapsa mtima kwambiri chifukwa cha munthuyo ndipo anati kwa Natani, “Pali Yehova, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa basi! 6Iye ayenera kulipira mwana wankhosa wamkaziyo kanayi, chifukwa anachita chinthu chimenechi ndipo analibe chifundo.”

7Kenaka Natani anati kwa Davide, “Munthuyo ndinu! Yehova, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakudzoza kukhala mfumu ya Israeli, ndipo ndinakupulumutsa mʼdzanja la Sauli. 8Ndinakupatsanso banja la mbuye wako ndiponso akazi a mbuye wako mʼmanja mwako. Ine ndinakupatsanso banja la Israeli ndi Yuda. Ndipo ngati zinthu zonse izi zinali zochepa, Ine ndikanakupatsa zambiri. 9Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita chimene chili choyipa pamaso pake? Iwe unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndipo unatenga mkazi wake kukhala wako. Uriyayo unamupha ndi lupanga la Aamoni. 10Ndipo tsopano lupanga silidzachoka pa nyumba yako, chifukwa unandinyoza ine ndi kutenga mkazi wa Uriya Mhiti kukhala wako.’

11“Yehova akuti, ‘Ine ndidzabweretsa tsoka pa iwe lochokera mʼbanja lako. Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa wina amene ali pafupi nawe, ndipo iye adzagona ndi akazi ako masanasana Aisraeli onse akuona. 12Iwe unachita zimenezi mwamseri koma Ine ndidzachita izi masanasana Aisraeli onse akuona.’ ”

13Kenaka Davide anati kwa Natani, “Ine ndachimwira Yehova.”

Natani anayankha kuti, “Yehova wachotsa tchimo lanu. Simufa ayi. 14Komabe, popeza pochita zimenezi mwachititsa kuti adani a Yehova amunyoze, mwana amene akubalireniyo adzafa.”

15Natani atapita kwawo, Yehova anakantha mwana amene mkazi wa Uriya anabereka ndipo anayamba kudwala. 16Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu. Iye anasala chakudya ndipo analowa mʼnyumba mwake nagona pansi usiku wonse. 17Akuluakulu a banja lake anayima pambali pake kuti amudzutse, koma iye anakana, ndipo sanadye chakudya chilichonse pamodzi ndi iwo.

18Mwana anamwalira pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Antchito a Davide anaopa kumuwuza kuti mwanayo wamwalira, popeza ankaganiza kuti, “Pamene mwanayu anali ndi moyo, ife tinayankhula Davide koma sanatimvere. Nanga tingamuwuze bwanji kuti mwana wamwalira? Mwina atha kudzipweteka.”

19Davide anaona kuti antchito ake amanongʼonezana pakati pawo ndipo anazindikira kuti mwanayo wamwalira. Iye anafunsa kuti, “Kodi mwanayo wamwalira?”

Iwo anayankha kuti, “Inde wamwalira.”

20Ndipo Davide anayimirira. Anakasamba nadzola mafuta ndi kusintha zovala zake. Pambuyo pake anapita ku nyumba ya Yehova kukapembedza. Kenaka anapita ku nyumba kwake ndipo atapempha chakudya anamupatsa nadya.

21Antchito ake anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu motere? Pamene mwana anali ndi moyo, munkasala chakudya ndi kulira, koma tsopano pamene mwana wamwalira inu mukudzuka ndi kudya!”

22Iye anayankha kuti, “Pamene mwana anali ndi moyo ine ndinkasala zakudya ndi kulira. Ine ndinkaganiza kuti, ‘Akudziwa ndani? Yehova atha kundikomera mtima kuti mwanayo akhale ndi moyo.’ 23Koma tsopano wamwalira ndisaliranji chakudya? Kodi ndingathe kumubwezanso? Ine ndidzapita kumene kuli iyeko, koma iye sadzabwerera kwa ine.”

24Ndipo Davide anatonthoza mkazi wake Batiseba, napita kwa iye ndi kugona naye. Iye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha dzina lake Solomoni. Yehova ankamukonda iye. 25Ndipo chifukwa chakuti Yehova ankamukonda iyeyo, Yehovayo anatumiza mawu kwa mneneri Natani kuti akamutchule Yedidiya.

26Pa nthawi imeneyi Yowabu anamenyana ndi Raba ku Amoni ndipo analanda nsanja yaufumu. 27Ndipo Yowabu anatumiza amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Ine ndamenyana ndi Raba ndipo ndatenga zitsime zake za madzi. 28Ndipo tsopano sonkhanitsani asilikali onse ndipo muzungulire mzindawo ndi kuwulanda.”

29Kotero Davide anasonkhanitsa ankhondo onse ndipo anapita ku Raba kukawuthira nkhondo ndi kuwulanda. 30Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo ndipo Davide anavala chipewacho. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide, ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo, 31ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa, ndiponso yowomba njerwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka iye pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒母耳记下 12:1-31

拿单斥责大卫

1耶和华派拿单先知去见大卫拿单大卫说:“一座城里有两个人,一个富有,一个贫穷。 2富人拥有许多牛羊, 3穷人除了自己买来养的一只母羊羔以外,什么也没有。他悉心饲养母羊羔,让它跟自己的儿女一起长大,他吃什么,羊也吃什么,他喝什么,羊也喝什么,还睡在他的怀中,就像他的女儿一样。 4一天,富人家中来了客人,他舍不得拿自己的牛羊款待客人,却宰了穷人的羊给客人吃。” 5大卫听后非常愤怒,对拿单说:“我凭永活的耶和华起誓,这人实在该死! 6他真是没有半点怜悯之心,他必须偿还那穷人四倍!”

7拿单大卫说:“那人就是你!以色列的上帝耶和华这样说,‘我膏立你做以色列的王,从扫罗手中救你, 8将你主人的家业和妻妾交给你,把以色列犹大的国权赐给你。倘若还不够,我会再加倍地赐给你。 9你为什么蔑视我的命令,做出我视为可憎的事呢?你借亚扪人的刀杀了乌利亚,把他的妻子据为己有。 10因为你藐视我,把乌利亚的妻子据为己有,从今以后,杀戮流血的事必永不离开你的家。’ 11耶和华说,‘我要在你家中降下灾祸,我要当着你的面把你的妻妾交给你的近臣,他必在光天化日之下与她们行淫。 12你在暗地里做这恶事,我要让这样的恶事当着以色列人的面在光天化日之下临到你。’” 13大卫拿单说:“我得罪了耶和华。”拿单说:“耶和华已经赦免了你的罪,使你不致死亡。 14但你做的丑事给了仇敌亵渎耶和华的机会,所以你这个孩子必定死。” 15拿单说完,便回家去了。

耶和华击打乌利亚的妻子给大卫生的孩子,使他患重病。 16大卫为这孩子向上帝哀求,并且禁食,他进到里面,整夜躺在地上。 17宫里的老臣在旁边伺候,想要扶他起来,他却不肯,也不肯与他们一同吃饭。 18到了第七日,孩子死了。大卫的臣仆都不敢把这消息告诉他,因为他们心里想:“孩子还活着的时候,我们劝他,他尚且不听,若告诉他孩子死了,他会怎样折磨自己呢?” 19大卫看见他们交头接耳,知道孩子死了,便问他们:“孩子死了?”他们答道:“是的,他死了。” 20大卫听后,便从地上起来,沐浴更衣,抹上香膏,然后到耶和华的殿去敬拜。他回宫以后,吩咐人摆上食物,自己开始用膳。 21他的臣仆诧异地问他:“我们真不明白,孩子还活着的时候,你禁食、哀哭。孩子死了,你反倒起来进食。” 22大卫说:“不错,孩子活着的时候我禁食、哀哭,因为我想也许耶和华会向我开恩,让他活命。 23但现在他既然死了,我禁食又有什么用呢?能让他起死回生吗?我必去他那里,他却不能返回这里了。”

24大卫安慰妻子拔示芭,与她同房,她便生了一个儿子。大卫给孩子取名叫所罗门。耶和华喜爱这孩子, 25祂差遣拿单先知去赐给他一个名字——耶底底亚,意思是耶和华喜爱他。

大卫打败亚扪人

26那时,约押正攻打亚扪人的都城拉巴27他派人去向大卫禀告说:“我攻打拉巴,已经占领了城的水源。 28请你赶快带领其余的兵马前来围攻并占领这城,免得我攻取这城以后,人们用我的名字为这城命名。” 29于是,大卫便召集了所有的人去攻打拉巴,攻陷了那城, 30夺取了亚扪王头上的金冠。这金冠重达三十四公斤,上面还镶了宝石,人们将它戴在大卫头上。大卫从城里得到许多战利品, 31又把城里的人带出来,让他们从事锯木、耕田、砍树和做砖的工作。他用同样的方式对待亚扪其他城邑的居民。之后,大卫和全军返回耶路撒冷