2 Mbiri 5 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 5:1-14

1Pamene ntchito yonse imene Solomoni anagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka; siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Mulungu.

Bokosi la Chipangano Libweretsedwa mʼNyumba ya Mulungu

2Kenaka Solomoni anasonkhanitsa akuluakulu a Israeli mu Yerusalemu, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, mzinda wa Davide. 3Ndipo Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa mfumu nthawi ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri.

4Akuluakulu onse a Israeli atafika, Alevi ananyamula Bokosi la Chipangano, 5ndipo anabwera nalo bokosi lija pamodzi ndi tenti ya msonkhano ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼmenemo. Ansembe ndi Alevi ndiye anazinyamula, 6ndipo Mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Aisraeli amene anasonkhana naye anali patsogolo pa Bokosi la Chipangano, akupereka nsembe nkhosa zambiri ndi ngʼombe zambiri zosawerengeka.

7Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a Akerubi. 8Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira. 9Mitengoyi inali yayitali kwambiri ndipo inkaonekera kunja kwa chipinda chamʼkati cha Malo Opatulika, koma osati kunja kwa Malo Opatulikawo; ndipo mitengoyi ilipo mpaka lero lino. 10Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.

11Kenaka ansembe anatulukamo mʼMalo Opatulika. Ansembe onse amene anali mʼmenemo anali atadziyeretsa posayangʼaniranso magulu awo ochokera. 12Alevi onse amene anali oyimba: Asafu, Hemani, Yedutuni ndi ana ndiponso abale awo, amayima mbali ya kummawa kwa guwa lansembe atavala zovala zofewa zosalala akuyimba ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe. Ansembe onse amene amayimba malipenga analipo 120 pamodzi. 13Oyimba malipenga ndi oyimba nyimbo aja amayimba mogwirizana, monga liwu la munthu mmodzi, kutamanda ndi kuyamika Yehova. Mogwirizana ndi malipenga, ziwaya zamalipenga ndi zida zina, anakweza mawu awo motamanda Yehova poyimba kuti,

“Yehova ndi wabwino;

chikondi chake chikhala mpaka muyaya.”

Ndipo Nyumba ya Mulungu wa Yehova inadzaza ndi mtambo, 14choncho ansembe sanathe kugwira ntchito yawo chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulungu.

Het Boek

2 Kronieken 5:1-14

De ark wordt de tempel ingebracht

1Zo werd de laatste hand aan de tempel gelegd. Daarna gaf Salomo de geschenken die zijn vader, koning David, aan de Here had gewijd, een plaats in de tempel. Ook de andere voorwerpen en al het zilver en goud werden opgeslagen in de schatkamers van de tempel. 2Daarna riep Salomo alle leiders van Israël, stamhoofden en familiehoofden, naar Jeruzalem voor de plechtigheid van het overbrengen van de ark van het verbond vanuit de Stad van David (die ook wel Sion werd genoemd) naar de tempel. 3Dat gebeurde in de zevende maand tijdens de viering van het Loofhuttenfeest.

4-5 Onder het toeziend oog van de leiders van Israël tilden de Levieten de ark van het verbond op en namen ook de tent mee, samen met de andere heilige voorwerpen. 6Koning Salomo en het volk offerden zoveel schapen en ossen voor de ark dat men de tel kwijtraakte. 7-8 Daarna droegen de priesters de ark naar de binnenste kamer van de tempel, het Heilige der Heiligen, en zetten hem neer onder de vleugels van de cherubs, hun vleugels strekten zich uit over de ark en zijn draagstokken. 9Deze draagstokken waren zo lang dat hun uiteinden vanuit het vertrek ernaast zichtbaar waren. Vanuit de buitengang waren ze echter niet te zien. De ark staat daar nu nog steeds. 10Er lag in de ark niets anders dan de twee stenen plaquettes die Mozes er bij de berg Horeb had ingelegd, toen de Here een verbond sloot met het volk Israël, nadat ze uit Egypte waren vertrokken.

11-12 Nadat alle priesters de reinigingsceremonieën hadden ondergaan, zonder dat werd gelet op de afdeling waartoe zij behoorden, kwamen ze naar buiten. En wat prezen de Levieten de Here toen de priesters uit het Heilige der Heiligen tevoorschijn kwamen! De zangers waren Asaf, Heman, Jeduthun en al hun zonen en broers. Zij droegen kleding van fijn linnen en stonden aan de oostkant van het altaar. Het koor werd begeleid door honderdtwintig priesters met trompetten, terwijl anderen cimbalen, citers en harpen bespeelden. 13Het orkest en het koor prezen en dankten de Here eenstemmig. Hun lofprijzing werd begeleid door trompetgeschal, het gerinkel van cimbalen en het luide spel van de andere muzikanten, allen prezen en dankten de Here. Steeds weer herhaalden zij de woorden: ‘Hij is goed en zijn goedheid en liefde duren tot in eeuwigheid.’ 14En op datzelfde moment vulde de glorie van de Here de tempel in de gestalte van een lichtende wolk, waardoor de priesters niet konden blijven staan en hun dienst moesten onderbreken.