2 Mbiri 16 – CCL & NIVUK

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 16:1-14

Zaka Zotsiriza za Asa

1Mʼchaka cha 36 cha ufumu wa Asa, Baasa mfumu ya Israeli inapita kukathira nkhondo dziko la Yuda. Anamangira mpanda mzinda wa Rama kuletsa aliyense kutuluka kapena kulowa mʼdziko la Asa mfumu ya Yuda.

2Ndipo Asa anatenga siliva ndi golide ku malo osungirako a mʼNyumba ya Mulungu ndi ku nyumba yake yaufumu ndi kuzitumiza kwa Beni-Hadadi mfumu ya Aramu imene inkakhala mu Damasiko. 3Iye anati, “Pakhale pangano pakati pa inu ndi ine, monga zinalili pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Taonani, ine ndikutumiza kwa inu siliva ndi golide. Tsopano thetsani mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti achoke kwa ine.”

4Beni-Hadadi anagwirizana ndi mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira nkhondo ake kukathira nkhondo mizinda ya Israeli. Iwo anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Maimu ndi mizinda yonse yosungira chuma ya Nafutali. 5Baasa atamva izi, anasiya kumanga Rama ndipo anayimitsa ntchito yakeyo. 6Ndipo mfumu Asa anabwera ndi Ayuda onse, ndipo anachotsa miyala ndi matabwa ku Rama amene Baasa amagwiritsa ntchito. Ndi zimenezi Asa ankamangira Geba ndi Mizipa.

7Nthawi imeneyi mlosi Hanani anabwera kwa Asa mfumu ya Yuda ndipo anati kwa iye, “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Aramu osati Yehova Mulungu wanu, gulu la ankhondo la mfumu ya ku Aramu lapulumuka mʼmanja mwanu. 8Kodi Akusi ndi Alibiya sanali gulu lankhondo lamphamvu lokhala ndi magaleta ochuluka ndi okwera magaleta ake? Koma pamene inu munadalira Yehova, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. 9Pakuti Yehova amayangʼana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi kuti alimbikitse iwo amene mitima yawo ayipereka kwathunthu kwa Iye. Inu mwachita chinthu chopusa ndipo kuyambira lero mudzakhala pa nkhondo.”

10Asa anamupsera mtima mlosi uja chifukwa cha izi mwakuti anakwiya kwambiri namuyika mʼndende. Pa nthawi yomweyonso Asa anazunza mwankhanza anthu ena.

11Ntchito zina za mfumu Asa, kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli. 12Mʼchaka cha 39 cha ufumu wake, Asa anayamba kudwala nthenda ya mapazi. Ngakhale nthendayo inali yaululu kwambiri, komabe iye sanafunefune Yehova, koma anafuna thandizo kwa asingʼanga. 13Ndipo mʼchaka cha 41 cha ufumu wake, Asa anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. 14Iye anayikidwa mʼmanda amene anadzisemera yekha mu Mzinda wa Davide. Anagoneka mtembo wake pa chithatha chimene anayikapo zonunkhira zamitundumitundu, ndipo anasonkha chimoto chachikulu pomuchitira ulemu.

New International Version – UK

2 Chronicles 16:1-14

Asa’s last years

1In the thirty-sixth year of Asa’s reign Baasha king of Israel went up against Judah and fortified Ramah to prevent anyone from leaving or entering the territory of Asa king of Judah.

2Asa then took the silver and gold out of the treasuries of the Lord’s temple and of his own palace and sent it to Ben-Hadad king of Aram, who was ruling in Damascus. 3‘Let there be a treaty between me and you,’ he said, ‘as there was between my father and your father. See, I am sending you silver and gold. Now break your treaty with Baasha king of Israel so that he will withdraw from me.’

4Ben-Hadad agreed with King Asa and sent the commanders of his forces against the towns of Israel. They conquered Ijon, Dan, Abel Maim16:4 Also known as Abel Beth Maakah and all the store cities of Naphtali. 5When Baasha heard this, he stopped building Ramah and abandoned his work. 6Then King Asa brought all the men of Judah, and they carried away from Ramah the stones and timber Baasha had been using. With them he built up Geba and Mizpah.

7At that time Hanani the seer came to Asa king of Judah and said to him: ‘Because you relied on the king of Aram and not on the Lord your God, the army of the king of Aram has escaped from your hand. 8Were not the Cushites16:8 That is, people from the upper Nile region and Libyans a mighty army with great numbers of chariots and horsemen16:8 Or charioteers? Yet when you relied on the Lord, he delivered them into your hand. 9For the eyes of the Lord range throughout the earth to strengthen those whose hearts are fully committed to him. You have done a foolish thing, and from now on you will be at war.’

10Asa was angry with the seer because of this; he was so enraged that he put him in prison. At the same time Asa brutally oppressed some of the people.

11The events of Asa’s reign, from beginning to end, are written in the book of the kings of Judah and Israel. 12In the thirty-ninth year of his reign Asa was afflicted with a disease in his feet. Though his disease was severe, even in his illness he did not seek help from the Lord, but only from the doctors. 13Then in the forty-first year of his reign Asa died and rested with his ancestors. 14They buried him in the tomb that he had cut out for himself in the City of David. They laid him on a bier covered with spices and various blended perfumes, and they made a huge fire in his honour.