2 Mbiri 12 – CCL & CARSA

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 12:1-16

Sisaki Athira Nkhondo Dziko la Yuda

1Rehobowamu atakhazikika monga mfumu nakhaladi wamphamvu, iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse anasiya malamulo a Yehova. 2Chifukwa anakhala osakhulupirika pamaso pa Yehova, Sisaki mfumu ya dziko la Igupto inathira nkhondo Yerusalemu mʼchaka chachisanu cha mfumu Rehobowamu. 3Sisakiyo anabwera ndi magaleta 1,200 ndi anthu okwera akavalo 60,000 ndiponso asilikali osawerengeka ochokera ku Libiya, Suki ndi Kusi amene anabwera naye kuchokera ku Igupto. 4Iye analanda mizinda yotetezedwa ya Yuda ndipo anafika mpaka ku Yerusalemu.

5Ndipo mneneri Semaya anabwera kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a Yuda amene anasonkhana mu Yerusalemu chifukwa cha Sisaki ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova akuti, ‘Inu mwandisiya, choncho Inenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisaki.’ ”

6Atsogoleri a Israeli pamodzi ndi mfumu anadzichepetsa nati, “Yehova ndi wolungama.”

7Yehova ataona kuti adzichepetsa, anayankhula ndi Semaya kuti, “Pakuti adzichepetsa, Ine sindiwawononga koma posachedwapa ndiwapulumutsa. Sinditsanulira ukali wanga pa Yerusalemu kudzera mwa Sisaki. 8Komabe iwo adzakhala pansi pa ulamuliro wake, kuti aphunzire kudziwa kusiyanitsa pakati pa kutumikira Ine ndi kutumikira mafumu a mayiko ena.”

9Sisaki mfumu ya dziko la Igupto atathira nkhondo Yerusalemu, iye anatenga chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu. Iye anatenga zinthu zonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomoni anapanga. 10Ndipo mfumu inapereka zishango zamkuwa kwa oyangʼanira mʼmalo mwake ndipo iwo anazipereka kwa oyangʼanira alonda amene amayangʼanira pa chipata cha nyumba yaufumu. 11Nthawi ina iliyonse imene mfumu ikupita ku Nyumba ya Yehova, alonda amapita nayo atanyamula zishango, ndipo kenaka amakazibwezera ku chipinda cha alonda.

12Pakuti mfumu Rehobowamu inadzichepetsa, mkwiyo wa Yehova unamuchokera, sanawonongedweretu. Kunena zoona, munali zinthu zina zabwino mu Yuda.

13Mfumu Rehobowamu anayika maziko a ufumu wake mwamphamvu mu Yerusalemu ndipo anapitirira kukhala mfumu. Iye anali ndi zaka 41 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka 17 mu Yerusalemu, mzinda wa Yehova umene anasankha pakati pa mafuko a Aisraeli mmene Yehova anakhazikikamo. Dzina la amayi ake linali Naama, amene anali Mwamoni. 14Rehobowamu anachita zoyipa chifuwa mtima wake sunafunefune Yehova.

15Ntchito za Rehobowamu, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri la mneneri Semaya ndi mlosi Ido amene amalemba mbiri? Panali nkhondo yosatha pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu. 16Rehobowamu anamwalira, ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Ndipo mwana wake Abiya analowa ufumu mʼmalo wake.

Священное Писание (Восточный перевод), версия с «Аллахом»

2 Летопись 12:1-16

Вторжение египтян в Иудею

(3 Цар. 14:25-28)

1После того как Реховоам утвердил свою власть и стал силён, он вместе со всем Исраилом12:1 То есть Иудея; так же во многих местах данной книги. Автор Летописей считает граждан Иудеи истинным Исраилом, народом Всевышнего. См. вступление к книге «Первая летопись». оставил Закон Вечного. 2Они нарушили верность Вечному, и вот Сусаким12:2 Сусаким – фараон Шешонк I, основатель XXII (ливийской) династии, правил с 950 по 929 гг. до н. э., царь Египта, на пятом году правления Реховоама напал на Иерусалим. 3С тысячью и двумя сотнями колесниц, шестьюдесятью тысячами всадников и бесчисленным множеством пеших воинов из ливийцев, сукхитов и эфиопов, которые пришли с ним из Египта, 4он завладел всеми укреплёнными городами Иудеи и подошёл к самому Иерусалиму. 5Пророк Шемая пришёл к Реховоаму и к вождям Иудеи, которые собрались в Иерусалиме из-за страха перед Сусакимом, и сказал им:

– Так говорит Вечный: Вы оставили Меня, и Я оставлю вас и отдам в руки Сусакиму.

6Вожди Исраила и царь смирились и сказали:

– Вечный праведен.

7Когда Вечный увидел, что они смирились, тогда к Шемае было слово Вечного:

– Так как они смирились, Я не истреблю их и вскоре спасу. Мой гнев не изольётся на Иерусалим через Сусакима. 8Но им придётся покориться ему, чтобы они познали разницу между служением Мне и служением царям чужих земель.

9Когда Сусаким, царь Египта, пришёл в Иерусалим, он унёс сокровища храма Вечного и сокровища царского дворца. Он забрал всё, включая и золотые щиты, которые сделал Сулейман. 10Царь Реховоам сделал вместо них щиты из бронзы и вверил их начальникам стражи, что охраняла вход в царский дворец. 11Всякий раз, когда царь шёл в храм Вечного, стража со щитами шла с ним, а после этого возвращала их в комнату стражи.

12Так как Реховоам смирил себя, гнев Вечного на него прекратился и не погубил его окончательно. Да и в Иудее было что-то доброе.

Конец правления Реховоама

(3 Цар. 14:21-24, 29-31)

13Царь Реховоам утвердился в Иерусалиме и царствовал. Ему был сорок один год, когда он стал царём, и правил он семнадцать лет в Иерусалиме, городе, который Вечный избрал среди всех родов Исраила для пребывания там. Мать Реховоама звали Наама, она была аммонитянкой. 14Он творил зло, потому что не отдал своего сердца тому, чтобы искать Вечного.

15События царствования Реховоама, от первых до последних, описаны в «Записях пророка Шемаи» и в «Записях провидца Иддо», вошедших в родословия. Между Реховоамом и Иеровоамом всё время шла война. 16Реховоам упокоился со своими предками и был похоронен в Городе Давуда. И царём вместо него стал его сын Авия.