2 Mafumu 25 – CCL & CST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 25:1-30

1Choncho mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse la ankhondo, nadzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Iye anamanga misasa kunja kwa mzindawo ndipo anamanga mitumbira ya nkhondo kuzungulira mzindawo. 2Mzindawo anawuzinga mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha Mfumu Zedekiya. 3Pa tsiku lachisanu ndi chinayi pa mwezi wachinayi, njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti anthu analibe chakudya. 4Pamenepo khoma la mzindawo linabowoledwa ndipo gulu lonse la ankhondo linathawa usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Iwo anathawira cha ku Araba, 5koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika. 6Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula, kumene anagamula mlandu wa Zedekiyayo. 7Iwo anapha ana a Zedekiya iyeyo akuona. Kenaka anakolowola maso a Zedekiya namumanga ndi unyolo wamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni.

8Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, mʼchaka cha 19 cha Nebukadinezara, mfumu ya Babuloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, nduna ya mfumu ya Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. 9Iye anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu pamodzi ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse yofunika. 10Gulu lonse la ankhondo la ku Babuloni limene linali ndi mkulu wa asilikali oteteza mfumu ija, linagumula malinga ozungulira Yerusalemu. 11Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, ndi ena amene anathawira kwa mfumu ya Babuloni, pamodzi ndi ena onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 12Koma mkulu wa asilikaliyo anasiya anthu ena osauka kwambiri mʼdzikomo kuti azisamalira minda ya mpesa ndi minda ina.

13Ababuloni anaphwanya zipilala zamkuwa, maphaka ndiponso mbiya ya mkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo anatenga mkuwawo napita nawo ku Babuloni. 14Iwo anatenganso miphika, mafosholo, mbaniro za nyale, mbale ndi ziwiya zonse zamkuwa zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼNyumbayo. 15Mkulu wa asilikali uja anatenganso zofukizira lubani ndi mbale zowazira magazi. Zonsezi zinali zopangidwa ndi golide wabwino kwambiri kapena siliva.

16Mkuwa wochokera ku zipilala ziwiri zija, mbiya ija ndi maphaka aja, zimene Solomoni anapanga mʼNyumba ya Yehova, kuchuluka kwake kunali kosawerengeka. 17Chipilala chilichonse chinali chotalika mamita asanu ndi atatu. Mutu wa mkuwa umene unali pamwamba pa chipilalacho unali mita imodzi ndi theka ndipo unakongoletsedwa ndi ukonde wa makangadza a mkuwa amene anazungulira mutuwo. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi chinacho, ndipo chinali ndi ukonde.

18Mkulu wa asilikali uja anagwira ukapolo mkulu wa ansembe Seraya, Zefaniya wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apakhomo. 19Mwa anthu amene anali mu mzindamo, anatenga mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso alangizi asanu a mfumu. Anatenganso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankalemba anthu ntchito ya usilikali mʼdzikomo pamodzi ndi anthu ake 60 amene anali mu mzindamo. 20Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anawatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya Babuloni ku Ribula. 21Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloni inalamula kuti awakwapule ndi kuwapha.

Choncho Ayuda anatengedwa ukapolo kuwachotsa mʼdziko lawo.

22Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala woyangʼanira anthu amene anatsala ku Yuda. 23Atsogoleri onse ankhondo ndi anthu awo atamva kuti mfumu ya Babuloni yasankha Gedaliya kukhala bwanamkubwa, anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. Atsogoleriwo mayina awo anali awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti wa ku Netofa ndi Yaazaniya mwana wa Maakati, pamodzi ndi anthu awo. 24Gedaliya analumbira powatsimikizira iwo ndi anthu awo. Iye anati, “Musachite mantha ndi atsogoleri Ababuloniwa. Khalani mʼdziko muno ndipo tumikirani mfumu ya Babuloni. Mukatero zinthu zidzakuyenderani bwino.”

25Koma pa mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaeli mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa banja laufumu, anabwera ndi anthu khumi ndipo anapha Gedaliya pamodzi ndi Ayuda ndi anthu a ku Babuloni amene anali naye limodzi ku Mizipa. 26Chifukwa cha zimenezi, anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo anathawira ku Igupto chifukwa choopa Ababuloni.

Kumasulidwa kwa Yehoyakini

27Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini mfumu ya Yuda, chaka chimene Evili-Merodaki anakhala mfumu ya Babuloni, anamasula Yehoyakini mʼndende pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27. 28Anamukomera mtima namukweza kupambana mafumu ena onse amene anali naye ku Babuloni. 29Choncho Yoyakini anavula zovala zake za ku ndende, ndipo ankadya ndi mfumu masiku onse a moyo wake. 30Mfumu inkamupatsa Yehoyakini chakudya tsiku lililonse pa moyo wake wonse.

Nueva Versión Internacional (Castilian)

2 Reyes 25:1-30

1En el año noveno del reinado de Sedequías, a los diez días del mes décimo, Nabucodonosor, rey de Babilonia, marchó con todo su ejército y atacó contra Jerusalén. Acampó frente a la ciudad y construyó una rampa de asalto a su alrededor. 2La ciudad estuvo sitiada hasta el año undécimo del reinado de Sedequías.

3A los nueve días del mes cuarto,25:3 cuarto. El texto hebreo no incluye esta palabra, pero véase Jer 52:6. cuando el hambre se agravó en la ciudad, y no había más alimento para el pueblo, 4se abrió una brecha en el muro de la ciudad, de modo que, aunque los babilonios la tenían cercada, todo el ejército se escapó de noche por la puerta que estaba entre los dos muros, junto al jardín real. Huyeron camino al Arabá,25:4 Arabá. Alt. valle del Jordán. 5pero el ejército babilonio persiguió a Sedequías hasta alcanzarlo en la llanura de Jericó. Sus soldados se dispersaron, abandonándolo, 6y los babilonios lo capturaron. Entonces lo llevaron ante el rey de Babilonia, que estaba en Riblá. Allí Sedequías recibió su sentencia. 7Ante sus propios ojos degollaron a sus hijos, y después le sacaron los ojos, lo ataron con cadenas de bronce y lo llevaron a Babilonia.

8A los siete días del mes quinto del año diecinueve del reinado de Nabucodonosor, rey de Babilonia, su ministro Nabuzaradán, que era el comandante de la guardia, fue a Jerusalén 9y le prendió fuego al templo del Señor, al palacio real y a todas las casas de Jerusalén, incluso a todos los edificios importantes. 10Entonces el ejército babilonio bajo su mando derribó las murallas que rodeaban la ciudad. 11Nabuzaradán además deportó a la gente que quedaba en la ciudad, es decir, al resto de la muchedumbre y a los que se habían aliado con el rey de Babilonia. 12Sin embargo, dejó a algunos de los más pobres para que se encargaran de los viñedos y de los campos.

13Los babilonios quebraron las columnas de bronce, las bases y la fuente25:13 la fuente. Lit. el mar; también en v. 16. de bronce que estaban en el templo del Señor, y se llevaron todo el bronce a Babilonia. 14También se llevaron las ollas, las tenazas, las despabiladeras, la vajilla y todos los utensilios de bronce que se usaban para el culto. 15Además, el comandante de la guardia se apoderó de los incensarios y de los tazones, todo lo cual era de oro y de plata.

16El bronce de las dos columnas, de la fuente y de las bases, que Salomón había hecho para el templo del Señor, era tanto que no se podía pesar. 17Cada columna medía ocho metros de altura. El capitel de bronce que estaba encima de cada columna medía metro y medio25:17 ocho metros … metro y medio. Lit. dieciocho codos … tres codos. de altura y estaba decorado alrededor con una red y con granadas de bronce. Las dos columnas tenían el mismo adorno.

18El comandante de la guardia tomó presos a Seraías, sacerdote principal, a Sofonías, sacerdote de segundo rango, y a los tres porteros. 19De los que quedaban en la ciudad, apresó al oficial encargado de las tropas, a cinco de los servidores personales del rey, al cronista principal del ejército, encargado de reclutar soldados de entre el pueblo, y a sesenta ciudadanos que todavía estaban en la ciudad. 20Después de apresarlos, Nabuzaradán, comandante de la guardia, se los llevó al rey de Babilonia, que estaba en Riblá. 21Allí, en el territorio de Jamat, el rey los hizo ejecutar.

Así Judá fue desterrado y llevado cautivo.

22Nabucodonosor, rey de Babilonia, nombró a Guedalías, hijo de Ajicán y nieto de Safán, para gobernar a la gente que había dejado en Judá. 23Cuando los oficiales del ejército de Judá y sus tropas se enteraron de que el rey de Babilonia había nombrado gobernador a Guedalías, fueron a ver a este en Mizpa. Los oficiales eran Ismael hijo de Netanías, Johanán hijo de Carea, Seraías hijo de Tanjumet, oriundo de Netofa, y Jazanías, hijo de un hombre de Macá. 24Guedalías les hizo este juramento a ellos y a sus tropas: «No temáis a los oficiales babilonios. Si vosotros os quedáis en el país y servís al rey de Babilonia, os aseguro que os irá bien».

25Pero a los siete meses Ismael, hijo de Netanías y nieto de Elisama, que era de la estirpe real, y diez hombres que lo acompañaban, fueron y asesinaron a Guedalías; también mataron a los hombres de Judá y a los babilonios que formaban parte de su séquito en Mizpa. 26Acto seguido, todos huyeron a Egipto, grandes y pequeños, junto con los oficiales, pues temían a los babilonios.

Liberación del rey Joaquín

25:27-30Jer 52:31-34

27En el día veintisiete del mes duodécimo del año treinta y siete del exilio de Joaquín, rey de Judá, Evil Merodac, rey de Babilonia, en el año primero de su reinado, sacó a Joaquín de la cárcel. 28Lo trató amablemente y le dio una posición más alta que la de los otros reyes que estaban con él en Babilonia. 29Joaquín dejó su ropa de prisionero, y por el resto de su vida comió a la mesa del rey. 30Además, durante toda su vida Joaquín gozó de una pensión diaria que le proveía el rey de Babilonia.