2 Mafumu 22 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 22:1-20

Buku la Malamulo Lipezeka

1Yosiya anakhala mfumu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 31. Amayi ake anali Yedida mwana wa Adaiya wochokera ku Bozikati. 2Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira zonse za Davide kholo lake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.

3Mʼchaka cha 18 cha ufumu wake, Mfumu Yosiya anatuma mlembi wa nyumba ya mfumu, Safani, mwana wa Azariya, mwana wa Mesulamu, ku Nyumba ya Yehova. Iye anati, 4“Pita kwa mkulu wa ansembe Hilikiya ndipo ukamuwuze kuti awerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Yehova, zimene alonda a pa khomo anasonkhanitsa kwa anthu. 5Ndalamazo azipereke kwa anthu amene asankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Ndipo anthu amenewa azilipira antchito amene akukonzanso Nyumba ya Yehova, 6amisiri a matabwa, amisiri omanga ndi amisiri a miyala. Iwo akagulenso matabwa ndi miyala yosemedwa kuti akonzere Nyumba ya Yehova. 7Koma anthu amene apatsidwa ndalama zolipira antchito okonza Nyumbayo asawafunse za kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo, popeza ndi anthu wokhulupirika.”

8Mkulu wa ansembe Hilikiya anawuza Safani, mlembiyo kuti, “Ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Anapereka bukulo kwa Safani amene analiwerenga. 9Ndipo Safani mlembi uja, anapita nakafotokozera mfumu kuti, “Atumiki anu apereka ndalama zija zinali mʼNyumba ya Yehova kwa anthu amene akugwira ntchito ndi kuyangʼanira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova.” 10Kenaka Safani mlembiyo, anafotokozera mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku.” Ndipo Safani analiwerenga pamaso pa mfumu.

11Mfumu itamva mawu a mʼBuku la Malamulo, inangʼamba zovala zake. 12Iyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Akibo mwana wa Mikaya, Safani mlembi uja ndi Asaiya mtumiki wa mfumu, kuti, 13“Pitani mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa anthu onse a mʼdziko la Yuda, za zomwe zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu kwambiri pa ife ndipo watiyakira chifukwa makolo athu sanamvere mawu a buku ili. Iwo sanachite molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼmenemu zokhudza ife.”

14Choncho Hilikiya wansembe, Ahikamu, Akibo, Safani ndi Asaiya anapita kukayankhula ndi Hulida, mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala zaufumu. Mneneri wamkaziyu ankakhala mu Yerusalemu, ku chigawo chachiwiri cha mzindawo.

15Ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Kamuwuzeni munthu amene wakutumani kwa ine kuti, 16‘Ichi ndi chimene Yehova akunena: Taonani, ndidzabweretsa mavuto pa malo ano ndi pa anthu ake, molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga. 17Chifukwa anthuwo andisiya Ine ndi kumafukiza lubani kwa milungu ina nandikwiyitsa ndi mafano onse amene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzayaka pa malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’ 18Koma mfumu ya Yuda imene inakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova kayiwuzeni kuti, ‘Ichi ndi chimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena molingana ndi mawu amene unamva: 19Chifukwa unasweka mtima ndi kudzichepetsa wekha pamaso pa Yehova, pamene unamva zomwe zinayankhulidwa zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti adzakhala otembereredwa nasanduka bwinja, ndiponso chifukwa unangʼamba zovala ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, akutero Yehova. 20Choncho taona, Ine ndidzakutenga kupita kwa makolo ako ndipo udzayikidwa mʼmanda mwako mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene ndidzabweretse pamalo pano.’ ”

Ndipo anthu aja anabwerera nakafotokoza mawu amenewa kwa mfumu.

Het Boek

2 Koningen 22:1-20

Het herstel van de tempel door koning Josia

1-2 Josia, de nieuwe koning van Juda, was acht jaar oud. Hij regeerde eenendertig jaar in Jeruzalem. Jedida, een dochter van Adaja uit Bozkath, was zijn moeder. Zijn bewind was goed, want hij volgde het voorbeeld van zijn voorvader David door de Here volkomen te gehoorzamen.

3-4 In zijn achttiende regeringsjaar stuurde koning Josia zijn secretaris Safan, de zoon van Azalia en kleinzoon van Mesullam, naar de tempel om de hogepriester Hilkia de volgende opdracht te geven: ‘Verzamel het geld dat de priesters van de mensen ontvangen bij de deur van de tempel. 5-6 Geef het aan de bouwopzichters, zodat zij timmerlui en metselaars kunnen huren en hout en stenen kunnen kopen voor de restauratie van de tempel.’ 7De bouwopzichters hoefden geen verantwoording af te leggen voor hun uitgaven, want het waren allemaal eerlijke mannen.

8Op een dag kwam de hogepriester Hilkia bij secretaris Safan en vertelde hem: ‘Ik heb in de tempel een boekrol ontdekt, waarop de wetten van God staan geschreven.’ Hij gaf de boekrol aan Safan om hem te lezen. 9-10 Toen Safan de koning verslag uitbracht over de vorderingen bij het herstel van de tempel, vertelde hij hem ook over de boekrol die Hilkia had gevonden. Safan las de inhoud aan de koning voor. 11Nadat de koning had gehoord wat in de boekrol stond, scheurde hij ontzet zijn kleren. 12-13 Hij beval de priester Hilkia, Safan en Asaja, de persoonlijke dienaar van de koning, Safans zoon Ahikam en Michajaʼs zoon Achbor aan de Here te vragen: ‘Wat moeten wij doen? Wij hebben de aanwijzingen uit dit boek niet opgevolgd, uw toorn moet wel erg groot zijn, want ook onze voorouders hebben uw geboden niet nageleefd.’ 14De priester Hilkia, Ahikam, Achbor, Safan en Asaja gingen naar het nieuwe deel van Jeruzalem om de profetes Hulda op te zoeken. Zij was de vrouw van Sallum, de zoon van Tikva en kleinzoon van Harhas, die aan het hoofd stond van het kledingmagazijn.

15-16 Zij gaf hun de volgende boodschap door van de Here, de God van Israël: ‘Vertel de man die u naar Mij toestuurde, dat Ik deze stad en haar inwoners ga vernietigen, zoals staat in het boek dat u hebt gelezen. 17Want de inwoners van Juda hebben Mij de rug toegekeerd en afgoden aanbeden. Dat heeft Mij diep beledigd, mijn toorn tegen deze stad is hoog opgelaaid en zal niet meer doven. 18-19 Maar omdat u berouw had en zich zorgen maakte en u voor Mij vernederde, nadat u het boek en zijn waarschuwingen over vervloeking en ontvolking van het land had gelezen en omdat u uw kleren hebt gescheurd en hebt gehuild, zal Ik luisteren naar uw smeekbeden. 20Dit volk zal pas ten val komen nadat u bent gestorven, u zult zelf geen getuige zijn van de rampen die Ik over deze plaats ga brengen.’ Met die boodschap keerden zij naar de koning terug.