2 Akorinto 7 – CCL & CST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Akorinto 7:1-16

1Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi malonjezo amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.

Chimwemwe cha Paulo

2Mutipatse malo mʼmitima mwanu. Ife sitinalakwire munthu aliyense, kapena kuyipitsa munthu aliyense, kapena kumuchenjerera munthu aliyense. 3Sindikunena izi kuti mupezeke olakwa. Ndinanena kale kuti ife timakuganizirani kwambiri kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire. 4Ndimakukhulupirirani kwambiri ndipo ndimakunyadirani kwambiri. Ndikulimbikitsidwa kwambiri; mʼmasautso athu onse, chimwemwe changa chilibe malire.

5Pakuti titafika ku Makedoniya, sitinapume nʼkomwe, koma tinavutitsidwa mbali zonse. Kunja kunali mikangano, ndipo mʼmitima mwathu munali mantha. 6Koma Mulungu, amene amatonthoza mtima wopsinjika, anatitonthoza mtima ndi kufika kwa Tito, 7sikubwera kwake kokhako, komanso mawu achilimbikitso amene analandira kuchokera kwa inu. Iye anatiwuza kuti mukufuna kundiona, zachisoni chanu chachikulu, ndi kudzipereka kwanu kwa ine, motero chimwemwe changa chinachuluka kuposa kale.

8Ngakhale kalata yanga ija inakupwetekani mtima, sindikudandaula kuti ndinalemberanji. Ngakhale zinandikhudza, ndikudziwa kuti kalata yanga inakupwetekani, koma kwa kanthawi kochepa. 9Koma tsopano ndine wokondwa, osati chifukwa chakuti kalatayo inakupwetekani, koma chifukwa chakuti chisoni chanu chinakuthandizani kutembenuka mtima. Pakuti munamva chisoni monga mmene Mulungu amafunira, choncho simunapwetekedwe mwanjira iliyonse. 10Chisoni chimene Mulungu amafuna chimabweretsa kutembenuka mtima komwe kumabweretsa chipulumutso, ndipo sichikhumudwitsa. Koma chisoni cha dziko lapansi chimabweretsa imfa. 11Taonani zimene chisoni chimene Mulungu amafuna chatulutsa mwa inu. Chatulutsa khama lalikulu, chakuthandizani kuti mudzikonze nokha, chakukwiyitsani kwambiri, komanso chakupatsani mantha aakulu. Chakuchititsani kuti mufune kundiona ine, mwakhudzidwa kwambiri ndipo mukufuna kuonetsetsa kuti chilungamo chachitikadi. Pa nkhani yonseyi, mwaonetsadi kuti ndinu osalakwa. 12Choncho ngakhale ndinakulemberani kalata ija, sindinayilembe ndi chifukwa cha amene analakwayo kapena wolakwiridwa, koma ndinayilemba kuti inuyo muone kudzipereka kwanu kwa ife pamaso a Mulungu. 13Zimenezi zatilimbikitsa kwambiri.

Kuwonjezera pa zotilimbikitsazo, tinakondwa kwambiri poona chisangalalo cha Tito, chifukwa nonsenu munamuthandiza kukhazikitsa mtima wake pansi. 14Ndinamuwuza kuti ndimakunyadirani, ndipo simunandichititse manyazi. Koma monga zonse zimene tinakuwuzani zinali zoona, tsono zomwe ndinawuza Tito zokunyadirani zinali zoona. 15Ndipo chikondi chake pa inu nʼchachikulu kwambiri akakumbukira kuti nonse munali omvera, munamulandira ndi mantha ndi kunjenjemera. 16Ndine wokondwa kuti ndingathe kukukhulupirirani pa zonse.

Nueva Versión Internacional (Castilian)

2 Corintios 7:1-16

1Como tenemos estas promesas, queridos hermanos, purifiquémonos de todo lo que contamina el cuerpo y el espíritu, para completar en el temor de Dios la obra de nuestra santificación.

La alegría de Pablo

2Hacednos un lugar en vuestro corazón. A nadie hemos agraviado, a nadie hemos corrompido, a nadie hemos explotado. 3No digo esto para condenaros; ya os he dicho que tenéis un lugar tan amplio en nuestro corazón que con vosotros viviríamos o moriríamos. 4Os tengo mucha confianza y me siento muy orgulloso de vosotros. Estoy muy animado; en medio de todas nuestras aflicciones se desborda mi alegría.

5Cuando llegamos a Macedonia, nuestro cuerpo no tuvo ningún descanso, sino que nos vimos acosados por todas partes; conflictos por fuera, temores por dentro. 6Pero Dios, que consuela a los abatidos, nos consoló con la llegada de Tito, 7y no solo con su llegada, sino también con el consuelo que él había recibido de vosotros. Él nos habló del anhelo, de la profunda tristeza y de la honda preocupación que vosotros tenéis por mí, lo cual me llenó de alegría.

8Si bien os entristecí con mi carta, no me pesa. Es verdad que antes me pesó, porque me di cuenta de que por un tiempo mi carta os había entristecido. 9Sin embargo, ahora me alegro, no porque os hayáis entristecido, sino porque vuestra tristeza os llevó al arrepentimiento. Vosotros os entristecisteis tal como Dios lo quiere, de modo que nosotros de ninguna manera os hemos perjudicado. 10La tristeza que proviene de Dios produce el arrepentimiento que lleva a la salvación, de la cual no hay que arrepentirse, mientras que la tristeza del mundo produce la muerte. 11Fijaos lo que ha producido en vosotros esta tristeza que proviene de Dios: ¡qué empeño, qué afán por disculparse, qué indignación, qué temor, qué anhelo, qué preocupación, qué disposición para ver que se haga justicia! En todo habéis demostrado vuestra inocencia en este asunto. 12Así que, a pesar de que os escribí, no fue por causa del ofensor ni del ofendido, sino más bien para que delante de Dios os dierais cuenta por vosotros mismos de cuánto interés tenéis en nosotros. 13Todo esto nos reanima.

Además del consuelo que hemos recibido, nos alegró muchísimo el ver lo feliz que estaba Tito debido a que todos vosotros fortalecisteis su espíritu. 14Ya le había dicho que me sentía orgulloso de vosotros, y no me habéis hecho quedar mal. Al contrario, así como todo lo que os dijimos es verdad, también resultaron ciertos los elogios que hice de vosotros delante de Tito. 15Y él os tiene aún más cariño al recordar que todos fuisteis obedientes y lo recibisteis con temor y temblor. 16Me alegro de que puedo confiar plenamente en vosotros.