2 Akorinto 6 – CCL & HHH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Akorinto 6:1-18

1Pogwira naye ntchito pamodzi, tikukudandaulirani kuti musangolandira chisomo cha Mulungu pachabe. 2Pakuti akunena kuti,

“Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera,

ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza.

Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”

Masautso a Paulo

3Ife sitikuyika chokhumudwitsa pa njira ya wina aliyense, kuti utumiki wathu usanyozeke. 4Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa. 5Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya; 6pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi 7ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo. 8Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza. 9Amatiyesa osadziwika komatu ndife odziwika kwambiri. Amatiyesa wooneka ngati tikufa, koma tikupitirirabe ndi moyo, okanthidwa, koma osaphedwa. 10Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.

11Tayankhula momasuka kwa inu, Akorinto, ndipo tanena zonse za kumtima kwathu. 12Ife sitikukubisirani chikondi chathu pa inu, koma inu mukubisa chikondi chanu pa ife. 13Pofuna kufanana zochita ndi kuyankhula monga kwa ana anga, nanunso muzinena za kukhosi kwanu.

Kukhala Pamodzi ndi Osakhulupirira

14Musamasenze goli pamodzi ndi osakhulupirira. Kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kulungama ndi kusalungama? Kapena kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kuwala ndi mdima? 15Pali mgwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira angayanjane bwanji ndi munthu wosakhulupirira? 16Pali mgwirizano wanji pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ya mafano? Popezatu ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo. Monga Mulungu wanena kuti,

“Ndidzakhala mwa iwo

ndipo ndidzayendayenda pakati pawo,

ndipo ndidzakhala Mulungu wawo,

ndipo adzakhala anthu anga.”

17Nʼchifukwa chake

“Tulukani pakati pawo

ndi kudzipatula,

akutero Ambuye.

Musakhudze chodetsedwa chilichonse,

ndipo ndidzakulandirani.”

18Ndipo

“Ndidzakhala Atate anu,

ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,

akutero Ambuye, Wamphamvuzonse.”

Habrit Hakhadasha/Haderekh

אגרת פולוס השנייה אל-הקורנתים 6:1-18

1כעוזרי אלוהים אנו מתחננים לפניכם לא להזניח את חסד אלוהים שקיבלתם; אל תבזבזו את טובו וחסדו של אלוהים! 2כי הוא אומר:6‏.2 ו 2 ישעיהו מט 8 ”בעת רצון עניתיך וביום ישועה עזרתיך“. עתה עת רצון והיום יום ישועה!

3אנו משתדלים לא להיות מכשול לאיש, כדי שלא יטילו דופי בעבודתנו. 4אדרבא, בכל מעשינו אנו משתדלים להראות שאנו משרתי אלוהים. בסבלנות רבה אנו נושאים סבל, צרות ומצוקות. 5הוכינו, הושלכנו לכלא, נמסרנו לידי המון זועם; עמלנו עד אפיסת כוחות, לא אכלנו ולא ישנו. 6הוכחנו שאנו משרתי אלוהים בחיינו הטהורים, בהבנתנו את הבשורה, בסבלנותנו, בנדיבות לבנו, באהבתנו הכנה, ברוח הקודש הממלא אותנו, 7בדבר האמת שבפינו ובגבורת אלוהים. אנו חמושים בנשק הצדקה להגנה ולהתקפה. 8אנו שומרים על נאמנותנו לאדון אם מכבדים אותנו ואם בזים לנו, אם מבקרים או משבחים אותנו. אנו כנים וישרים אך נחשבים לשקרנים. 9העולם מתעלם מאתנו, אך רבים מכירים אותנו; אנו קרובים למוות, ובכל זאת חיים. נפצענו אך לא מתנו. 10לבנו מלא צער, ובכל זאת אנו שמחים באדון. אנו אמנם עניים, אך מעשירים אנשים רבים במתנות רוחניות. אנו חסרי־כל אך נהנים מן הכול.

11הו, ידידי הקורינתיים, דיברתי אליכם בכנות ופתחתי לפניכם את לבי. 12לא סגרתי את לבי בפניכם; אתם סגרתם את לבכם בפני! 13אני פונה אליכם עתה כאל בני: אנא, פתחו לנו את לבכם והיענו לאהבתנו.

14אל תיכנסו לשותפות עם אלה שאינם אוהבים את האדון, שכן מה המשותף לאנשי אלוהים ולאנשי חטא? כיצד יכול האור לחיות עם החושך?

15איזו הסכמה יכולה להיות בין המשיח לבין השטן? כיצד יכול המאמין להיות שותף ללא־מאמין? 16איזה קשר יש להיכל אלוהים עם האלילים? הלא אתם היכל אלוהים, משכן אלוהים חיים, שכן הוא עצמו אמר:6‏.16 ו 16 ויקרא כו 11,12 ”ונתתי משכני בתוככם … והתהלכתי בתוככם והייתי לכם לאלוהים ואתם תהיו לי לעם“. 17על כן אמר ה׳:6‏.17 ו 17 ישעיה נב 11; יחזקאל כ 34,41 ”צאו מתוכם והברו, נאום ה׳, וטמא אל תיגעו ואני אקבץ אתכם. 18והייתי לכם לאב ואתם תהיו לי לבנים ולבנות, נאום ה׳ צבאות.“