1 Samueli 24 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 24:1-22

Davide Amusiya Sauli Wosamupha

1Sauli atabwera kuchokera kumene amathamangitsa Afilisti anamva kuti, “Davide ali mʼchipululu cha Eni Gedi.” 2Tsono Sauli anatenga asilikali 3,000 odziwa kumenya bwino nkhondo kuchokera pakati pa Aisraeli onse ndipo anapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale.

3Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo. 4Tsono anthu a Davide anamuwuza kuti, “Tsiku lija lafika limene Yehova anakuwuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wanu mʼmanja mwanu, ndi kumuchita chimene chidzakukomereni.’ ” Koma Davide anapita mwakachetechete ndi kukadula msonga ya mkanjo wa Sauli.

5Atachita izi, Davide anatsutsika mu mtima chifukwa anadula msonga ya mkanjo wa Sauli. 6Tsono anawuza anthu ake kuti, “Yehova asalole kuti ndimuchite choyipa mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Ndisamupweteke pakuti ndi wodzozedwa wa Yehova.” 7Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka.

8Kenaka Davide anatuluka mʼphanga muja ndipo anayitana Sauli, “Mbuye wanga!” Sauli atayangʼana mʼmbuyo, Davide anawerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi. 9Anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumamvera mawu a anthu kuti, ‘Davide wakukonzerani chiwembu?’ 10Lero lino inu mwadzionera nokha kuti Yehova anakuperekani mʼmanja mwanga mʼphanga muja. Ena anandiwuza kuti ndikupheni, koma ndakusiyani. Ndinati, ‘Sindidzapha mbuye wanga pakuti ndiye wodzozedwa wa Yehova.’ 11Tsono abambo anga, onanitu kansalu ka mkanjo wanu kali mʼdzanja langali! Popeza kuti ndinatha kudula msonga ya mkanjo wanu koma osakuphani, pamenepo mudziwe kuti ine ndilibe maganizo woti ndikuchiteni choyipa kapena kukuwukirani. Sindinakulakwireni ngakhale kuti inu mukufuna moyo wanga kuti mundiphe. 12Yehova aweruze pakati pa inu ndi ine, akulangeni chifukwa cha zoyipa zimene mukundichitazi, koma dzanja langa silidzakukhudzani. 13Paja anthu akale anati, ‘Munthu woyipa, ntchito zakenso ndi zoyipa.’ Kotero dzanja langa silidzakukhudzani.

14“Kodi mfumu ya Israeli yadzalondola yani. Inu mukuthamangitsa yani? Galu wakufa kodi? Nsabwe kodi? 15Nʼchifukwa chake Yehova agamule, inde aweruze pakati pa inu ndi ine ndi kupeza wolakwa. Yehova anditeteze ndi kundipulumutsa mʼdzanja lanu.”

16Davide atatsiriza kuyankhula mawu awa, Sauli anafunsa kuti, “Kodi mawu amenewa ndi akodi mwana wanga Davide?” Sauli anayamba kulira mokweza. 17Anawuza Davide kuti, “Ndiwe wolungama kuposa ine. Iwe wandikomera mtima pamene ine ndakuchitira zoyipa. 18Iweyo lero lino wandifotokozera zabwino zimene wandichitira. Yehova anandipereka mʼdzanja lako koma iwe sunandiphe. 19Kodi munthu atapeza mdani wake angamulole kuti apite wosamuvulaza? Motero Yehova akuchitire iwe zabwino chifukwa cha zimene wandichitira lerozi. 20Ona tsono, Ine ndikudziwa kuti udzakhala mfumu ndithu ndipo ufumu wa Israeli udzakhazikika mʼmanja mwako. 21Tsopano undilonjeze molumbira lero mʼdzina la Yehova kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira kapena kufuta dzina langa pa banja la makolo anga.”

22Choncho Davide analumbira pamaso pa Sauli. Pambuyo pake Sauli anabwerera kwawo, koma Davide ndi anthu ake anapitanso ku phanga kuja.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒母耳记上 24:1-22

大卫不杀扫罗

1扫罗追击非利士人回来,得知大卫隐·基底的旷野, 2就率领三千以色列精兵去野羊岩附近搜索大卫和他的部下。 3他们来到路旁的一处羊圈,那里有一个山洞,扫罗进去大解。大卫和他的部下就躲在洞的深处。 4大卫的部下对大卫说:“耶和华说过要把你的仇敌交在你手中,任你处置,今天机会来了。”大卫就爬过去,偷偷割了扫罗外袍的一角。 5事后,大卫心里不安, 6他对部下说:“我不该做这样的事,我主是耶和华所膏立的王,我绝不出手伤害他,因为他是耶和华所膏立的。” 7大卫用这些话拦住他的部下,不让他们杀扫罗

扫罗起来离开山洞走了, 8大卫随后也来到洞外,在后面喊扫罗:“我主我王啊!”扫罗回头一看,见大卫俯伏在地,向他下拜。 9大卫扫罗说:“你为什么听信谗言,认为我要谋害你呢? 10你现在亲眼看见了,刚才在山洞里,耶和华把你交在我手中,有人叫我杀你,我却不肯,因为你是耶和华所膏立的王,我不会动手伤害你。 11我父请看,你的这块袍子在我手中。我割下了你的袍角,没有杀你,现在你应该明白我并未图谋背叛你。我没有对不起你,你却要置我于死地。 12愿耶和华在你我之间判定是非,替我申冤,我却不会动手伤害你。 13俗语说,‘恶事出于恶人’,所以我不会动手伤害你。 14以色列王出来要捉拿谁呢?一条死狗吗?一只跳蚤吗? 15愿耶和华做我们的审判官,在你我之间判定是非。愿耶和华鉴察,为我申冤,从你手中拯救我。”

16大卫说完了,扫罗问道:“我儿大卫啊!是你吗?”便放声大哭起来。 17扫罗大卫说:“你比我公义,因为你善待我,我却恶待你。 18你今天使我明白你善待了我,耶和华把我交在你手中,你却没有下手杀我。 19有谁会让自己手中的仇敌平安离去呢?愿耶和华因你今日善待我而赐福你。 20我知道你必做王,以色列国必在你手中得到坚固。 21现在请你凭耶和华向我起誓,你不会杀害我的子孙,灭绝我的后代。” 22大卫便向扫罗起誓。之后,扫罗回家了,大卫和部下也回堡垒去了。