1 Mbiri 3 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 3:1-24

Ana a Davide

1Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa:

Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli;

wachiwiri anali Danieli, amayi ake anali Abigayeli wa ku Karimeli;

2wachitatu anali Abisalomu, mwana wa Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri;

wachinayi anali Adoniya amayi ake anali Hagiti;

3wachisanu anali Sefatiya, amayi ake anali Abitali;

wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila.

4Ana asanu ndi mmodzi awa a Davide anabadwira ku Hebroni kumene analamulirako zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi.

Davide analamuliranso mu Yerusalemu kwa zaka 33, 5ndipo ana amene anabadwira ku Yerusalemuko anali awa:

Samua, Sobabu, Natani ndi Solomoni. Ana anayi awa anali a Batisuwa mwana wa Amieli. 6Anaberekanso Ibihari, Elisua, Elipeleti, 7Noga, Nefegi, Yafiya, 8Elisama, Eliada ndi Elifeleti, onse analipo asanu ndi anayi. 9Onsewa anali ana a Davide, osawerengera ana a azikazi. Ndipo mlongo wawo anali Tamara.

Mafumu a Yuda

10Mwana wa Solomoni anali Rehabiamu,

Rehabiamu anabereka Abiya,

Abiya anabereka Asa,

Asa anabereka Yehosafati,

11Yehosafati anabereka Yehoramu,

Yehoramu anabereka Ahaziya,

Ahaziya anabereka Yowasi,

12Yowasi anabereka Amaziya,

Amaziya anabereka Azariya,

Azariya anabereka Yotamu,

13Yotamu anabereka Ahazi,

Ahazi anabereka Hezekiya,

Hezekiya anabereka Manase,

14Manase anabereka Amoni,

Amoni anabereka Yosiya.

15Ana a Yosiya anali awa:

Yohanani mwana wake woyamba,

Yehoyakimu mwana wake wachiwiri,

Zedekiya mwana wake wachitatu,

Salumu mwana wake wachinayi.

16Ana a Yehoyakimu:

Yekoniya

ndi Zedekiya mwana wake.

Mayina a Mafumu Utatha Ukapolo

17Zidzukulu za Yekoniya wa mʼndende zinali izi:

mwana wake Silatieli, 18Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama ndi Nedabiya.

19Ana a Pedaya anali awa:

Zerubabeli ndi Simei.

Ana a Zerubabeli anali awa:

Mesulamu ndi Hananiya.

Mlongo wawo anali Selomiti.

20Panalinso ana ena asanu awa:

Hasubu, Oheli, Berekiya, Hasabiya ndi Yusabu-Hesedi.

21Zidzukulu za Hananiya zinali izi:

Pelatiya ndi Yesaiya, ndiponso ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya ndi ana a Sekaniya.

22Zidzukulu za Sekaniya zinali izi:

Semaya ndi ana ake:

Hatusi, Igala, Bariya, Neariya ndi Safati. Onse anali asanu ndi mmodzi.

23Ana a Neariya anali awa:

Eliyoenai, Hezekiya ndi Azirikamu. Onse anali atatu.

24Ana a Eliyoenai: Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu,

Yohanani, Delaya ndi Anani, onse anali asanu ndi awiri.