1 Mafumu 8 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 8:1-66

Abwera ndi Bokosi la Chipangano ku Nyumba ya Yehova

1Pamenepo Mfumu Solomoni inasonkhanitsa akuluakulu a Israeli, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli mu Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, Mzinda wa Davide. 2Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Mfumu Solomoni nthawi ya chikondwerero cha mwezi wa Etanimu, mwezi wachisanu ndi chiwiri.

3Akuluakulu onse a Israeli atafika, ansembe ananyamula Bokosi la Chipangano, 4ndipo anabwera nalo Bokosi la Yehova pamodzi ndi tenti ya msonkhano ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼmenemo. Ansembe ndi Alevi ndiye anazinyamula, 5ndipo Mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Aisraeli amene anasonkhana naye anali patsogolo pa Bokosi la Chipangano, akupereka nsembe nkhosa zambiri ndi ngʼombe zambiri zosawerengeka.

6Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a akerubi. 7Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira. 8Mitengoyi inali yayitali kwambiri ndipo inkaonekera kunja kwa chipinda chamʼkati cha Malo Opatulika koma osati kunja kwa Malo Opatulikawo; ndipo mitengoyi ilipo mpaka lero lino. 9Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.

10Ansembe atatuluka mʼMalo Opatulikawo, mtambo unadzaza Nyumba ya Yehova. 11Ndipo ansembewo sanathe kugwira ntchito yawo chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza mʼNyumba ya Yehova.

12Pamenepo Solomoni anati, “Yehova anati adzakhala mʼmitambo yakuda; 13taonani ndithu, ine ndakumangirani Nyumba yokongola kwambiri, malo woti muzikhalamo mpaka muyaya.”

14Aisraeli onse ali chiyimire pomwepo, mfumu inatembenuka ndi kuwadalitsa. 15Ndipo inati:

“Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, amene wachita ndi dzanja lake zimene analonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide abambo anga. Pakuti Iye anati, 16‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga Aisraeli ku Igupto, sindinasankhe mzinda wina uliwonse pa fuko lina lililonse la Aisraeli kuti kumeneko andimangire Nyumba, koma ndasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisraeli.’

17“Abambo anga Davide anali ndi maganizo mu mtima mwawo oti amangire nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli. 18Koma Yehova ananena kwa abambo anga, Davide, kuti, ‘Popeza zinali mu mtima mwako kumangira nyumba Dzina langa, unachita bwino kukhala ndi maganizo amenewa mu mtima mwakomo. 19Komatu, si iwe amene udzamanga Nyumba ya Mulungu, koma mwana wako, mwana amene iwe udzabereke. Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba.’

20“Yehova wasunga zimene analonjeza: ine ndalowa mʼmalo mwa abambo anga Davide ndipo tsopano ndili pa mpando waufumu wa Israeli, monga momwe Yehova analonjezera, ndipo ndamangira nyumba Dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli. 21Ndalikonzera malo Bokosi la Chipangano mmene muli pangano la Yehova limene anapangana ndi makolo athu pamene anawatulutsa mʼdziko la Igupto.”

Pemphero Lodzipereka la Solomoni

22Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba, 23nati:

“Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pansi pa dziko, inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse. 24Inu mwasunga lonjezo lanu kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu. Inde zimene munalonjeza ndi pakamwa panu, mwazikwaniritsa ndi manja anu, monga mmene tikuonera lero lino.

25“Ndipo tsopano, Inu Yehova Mulungu wa Israeli, sungani zimene munalonjeza kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu, pamene munati, ‘Sudzasowa munthu wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israeli, ngati ana ako adzasamalira mayendedwe awo mokhulupirika monga iwe wachitira.’ 26Ndipo tsopano, Inu Mulungu wa Israeli, lolani kuti mawu anu akwaniritsidwe amene munalonjeza mtumiki wanu Davide abambo anga.

27“Kodi Mulungu angakhaledi pa dziko lapansi? Mlengalenga ngakhale kumwamba kwenikweni, sikungakukwaneni. Nanga kuli bwanji ndi Nyumba iyi imene ndamanga! 28Koma Inu Yehova Mulungu wanga, imvani pemphero ndi pembedzero la mtumiki wanu. Imvani kulira ndi pemphero la mtumiki wanu limene ndikupempha pamaso panu lero lino. 29Maso anu azikhala otsekuka kuyangʼana Nyumba ino usiku ndi usana, malo ano amene Inu munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo,’ choncho imvani pemphero limene mtumiki wanu akupemphera akuyangʼana malo ano. 30Imvani pembedzero la mtumiki wanu ndi la anthu anu Aisraeli pamene akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani kumwambako, malo anu amene mumakhala; ndipo mukamva muzitikhululukira.

31“Munthu akalakwira mnzake, nawuzidwa kuti alumbire, akabwera kudzalumbira patsogolo pa guwa lansembe la Nyumba ino, 32imvani kumwambako ndi kuchitapo kanthu. Weruzani atumiki anuwo, wochimwa mugamule kuti ndi wolakwa ndipo alangidwe chifukwa cha zimene wachita. Wosachimwa mugamule kuti ndi wosalakwa, ndipo muonetse kusalakwa kwakeko.

33“Anthu anu Aisraeli akagonja kwa adani awo chifukwa akuchimwirani, ndipo akatembenukira kwa Inu ndi kuvomereza Dzina lanu, kupemphera ndi kupembedzera kwa Inu mʼNyumba ino, 34pamenepo imvani kumwambako ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraeli ndi kuwabweretsa ku dziko limene munawapatsa makolo awo.

35“Pamene kumwamba kwatsekeka ndipo mvula sikugwa chifukwa anthu anu akuchimwirani, ndipo pamene apemphera akuyangʼana malo ano ndi kuvomereza Dzina lanu, ndi kutembenuka kuchoka ku machimo awo chifukwa inu mwawalanga, 36pamenepo imvani kumwambako ndipo muwakhululukire atumiki anu, anthu anu Aisraeli. Aphunzitseni makhalidwe oyenera ndipo gwetsani mvula mʼdziko limene munapereka kwa anthu anu monga cholowa chawo.

37“Pamene mʼdziko mwagwa njala kapena mliri, chinoni kapena chiwawu, dzombe kapena kapuchi, kapena pamene mdani wazungulira mzinda wawo wina uliwonse, kaya mavuto kapena matenda abwera, 38ndipo wina aliyense mwa Aisraeli akapemphera kapena kukudandaulirani, aliyense wa iwo akadziwa masautso a mu mtima mwake ndi kukweza manja awo kuloza Nyumba ino, 39pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo chitanipo kanthu. Muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita, popeza inu mumadziwa mtima wake (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu onse), 40motero iwo adzakuopani masiku onse amene adzakhale mʼdziko limene munalipereka kwa makolo athu.

41“Ndipo kunena za mlendo amene si mmodzi wa anthu anu Aisraeli, koma wabwera kuchokera ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu, 42pakuti anthu adzamva za dzina lanu lotchukali ndiponso za dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu, kudzapemphera akuyangʼana Nyumba ino, 43pamenepo imvani kumwambako, malo anu okhalamo, ndipo muchite zonse zimene mlendoyo akukupemphani, kotero kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu ndi kukuopani monga amachitira anthu anu Aisraeli, ndipo adziwe kuti Nyumba ino imene ndakumangirani imadziwika ndi Dzina lanu.

44“Pamene anthu anu apita ku nkhondo kukamenyana ndi adani awo, kulikonse kumene mungawatume, ndipo pamene apemphera kwa Yehova moyangʼana mzinda umene mwausankha ndi Nyumba imene ine ndamangira Dzina lanu, 45imvani kumwambako pemphero lawo ndi kudandaula kwawo, ndipo apambanitseni.

46“Pamene akuchimwirani, popeza palibe munthu amene sachimwa, ndipo Inu nʼkuwakwiyira ndi kuwapereka kwa mdani, amene adzawatenga ukapolo kupita ku dziko lake, kutali kapena pafupi; 47ndipo ngati asintha maganizo ali ku dziko la ukapololo ndi kulapa ndi kukudandaulirani mʼdziko la owagonjetsa ndi kunena kuti, ‘Ife tachimwa, tachita zolakwa, tachita zinthu zoyipa,’ 48ndipo ngati abwerera kwa Inu ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse mʼdziko la adani awo amene anawatenga ukapolo, ndi kupemphera kwa Inu moyangʼana dziko limene munapereka kwa makolo awo, moyangʼana mzinda umene munawusankha ndiponso Nyumba imene ine ndamangira Dzina lanu, 49imvani kumwambako, malo anu wokhalamo, imvani pemphero lawo ndi kudandaula kwawo, ndipo muwachitire zabwino. 50Ndipo khululukirani anthu anu amene akuchimwirani. Khululukirani zolakwa zonse akuchitirani ndipo mufewetse mitima ya amene anawagonjetsawo kuti awachitire chifundo; 51popeza ndi anthu anu ndiponso cholowa chanu, anthu omwe munawatulutsa ku Igupto, kuwachotsa mʼngʼanjo yamoto yosungunula zitsulo.

52“Maso anu atsekuke kuti aone dandawulo la mtumiki wanu ndiponso madandawulo a anthu anu Aisraeli, ndipo mutchere khutu nthawi iliyonse pamene akulirirani. 53Pakuti Inu munawasiyanitsa ndi anthu a mitundu ina yonse ya dziko lonse kuti akhale cholowa chanu, monga momwe munanenera kudzera mwa mtumiki wanu Mose pamene Inu, Ambuye Yehova, munatulutsa makolo athu ku Igupto.”

54Solomoni atamaliza mapemphero ndi mapembedzero onsewa kwa Yehova, anayimirira pa guwa lansembe la Yehova, nagwada atakweza manja ake kumwamba. 55Anayimirira ndi kudalitsa gulu lonse la Aisraeli ndi mawu okweza, nati:

56“Atamandike Yehova, amene wapereka mpumulo kwa anthu ake Aisraeli monga momwe analonjezera. Palibe mawu ndi amodzi omwe amene anapita pachabe pa malonjezo ake onse abwino amene anawapereka kudzera mwa mtumiki wake Mose. 57Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga momwe anakhalira ndi makolo athu; asatisiye kapena kutitaya. 58Atembenuzire mitima yathu kwa Iye, kuti tiyende mʼnjira zake zonse ndi kusunga mawu ake, malamulo ake ndi malangizo ake amene anapereka kwa makolo athu. 59Ndipo mawu angawa, amene ndapemphera pamaso pa Yehova, asayiwalike pamaso pa Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, ndipo Iye alimbikitse mtumiki wake ndiponso athandize Aisraeli, anthu ake powapatsa zosowa zawo za tsiku ndi tsiku, 60kotero kuti anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi adziwe kuti Yehova ndi Mulungu ndipo kuti palibenso wina. 61Koma mitima yanu ikhale yodzipereka kwathunthu kwa Yehova Mulungu wanu, kutsatira malamulo ake ndi kumvera malangizo ake, monga lero lino.”

Mwambo Wopereka Nyumba ya Mulungu

62Ndipo mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova. 63Solomoni anapereka nsembe zachiyanjano kwa Yehova: ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapatula Nyumba ya Yehova.

64Tsiku lomwelo mfumu inapatulanso malo a pakati pa bwalo limene linali kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndiponso nthuli za mafuta za nsembe yachiyanjano, chifukwa guwa lansembe la mkuwa limene linali pamaso pa Yehova linali lochepa kwambiri ndipo nsembe zonse zopsereza, nsembe zachakudya, ndi nthuli za mafuta a nsembe zachiyanjano sizikanakwanirapo.

65Choncho nthawi imeneyi, Solomoni anachita chikondwerero pamodzi ndi Aisraeli onse. Unali msonkhano waukulu, kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha ku Igupto. Anachita chikondwerero chimenechi pamaso pa Yehova Mulungu wathu kwa masiku asanu ndi awiri, anawonjezerapo masiku ena asanu ndi awiri, onse pamodzi ngati masiku 14. 66Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Solomoni anawuza anthu kuti apite kwawo. Anthuwo anathokoza mfumu ndipo kenaka anapita kwawo mokondwa ndi mosangalala mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira mtumiki wake Davide ndi anthu ake Aisraeli.

Het Boek

1 Koningen 8:1-66

De ark in het Heilige der Heiligen

1Salomo riep alle leiders van Israël—de stamhoofden en familiehoofden—naar Jeruzalem om er getuige van te zijn hoe de ark van het verbond van de Here vanuit het heiligdom in Sion, de Stad van David, naar de tempel werd overgebracht. 2Deze feestelijke gebeurtenis had plaats in de tijd van het Loofhuttenfeest, in de zevende maand. 3-4 Toen alle leiders van het volk Israël aanwezig waren, droegen de priesters de ark van de Here naar de tempel, samen met alle heilige voorwerpen uit de tabernakel. 5Koning Salomo en alle andere mensen kwamen voor de ark bij elkaar en offerden een ontelbaar aantal schapen en runderen. 6Daarna droegen de priesters de ark het Heilige der Heiligen binnen en zetten hem neer onder de vleugels van de engelen. 7Die engelen waren zo gemaakt dat hun vleugels zich uitstrekten over de plaats waar de ark zou komen te staan, hun vleugels overschaduwden dus de ark en zijn draagstokken. 8Die stokken waren zo lang dat zij terzijde van de engelen uitstaken en vanuit de andere kamer te zien waren. Vanuit de buitenste voorhof kon men ze echter niet zien. Zij bleven daar liggen tot op de dag van vandaag. 9Er lag in die tijd niets in de ark dan de twee stenen plaquettes die Mozes erin had gelegd toen de Here bij de berg Horeb zijn verbond had gesloten met het volk Israël, na het vertrek uit Egypte.

10Terwijl de priesters terugkeerden uit het binnenste heiligdom, vulde een heldere wolk de tempel 11en daardoor konden de priesters niet meer de tempel in om er hun diensten te verrichten. De heerlijkheid en glorie van de Here vulde het hele gebouw.

12Toen riep koning Salomo de Here aan met de volgende woorden: ‘De Here heeft gezegd dat Hij in de dichte wolk zou wonen. 13Maar, Here, ik heb op aarde een prachtig huis voor U gebouwd. Een plaats waar U voor altijd kunt verblijven.’ 14De koning draaide zich om naar de mensen die om hem heen stonden en zegende hen. 15‘Gezegend zij de Here, de God van Israël,’ zei hij, ‘die vandaag heeft gedaan wat Hij mijn vader David had beloofd. 16Want Hij zei tegen hem: “Toen Ik mijn volk uit Egypte haalde, wees Ik geen plaats aan voor mijn tempel, maar Ik wees wel een man aan als leider van mijn volk.” 17Die man was mijn vader David. Hij had altijd al de wens een tempel te bouwen voor de Here, de God van Israël. 18Maar de Here zei tegen mijn vader David: “U hebt er goed aan gedaan dat u van plan was een tempel te bouwen voor mijn naam. 19Toch mag u die tempel niet bouwen, maar uw zoon zal dat doen.” 20Nu is de Here zijn belofte nagekomen, ik ben mijn vader opgevolgd als koning van Israël en nu is deze tempel gebouwd voor de Here, de God van Israël. 21En in die tempel heb ik een plaats bestemd voor de ark waarin het verbond rust dat de Here met onze voorouders sloot, toen Hij hen uit het land Egypte bevrijdde.’

Salomo draagt de tempel op aan God

22Terwijl de mensen toekeken, ging Salomo voor het altaar van de Here staan, spreidde zijn handen uit naar de hemel en zei: 23‘O Here, God van Israël, er is geen God zoals U in de hemel of op aarde, want U bent liefdevol en trouw en U houdt uw beloften aan uw volk als het uw wil doet. 24Vandaag bent U de belofte aan mijn vader David nagekomen, die uw dienaar was. Wat uw mond heeft gesproken, heeft uw hand in vervulling laten gaan. Dat hebben wij vandaag kunnen zien. 25En, Here, God van Israël, vervul nu ook uw verdere beloften aan David: dat van zijn nakomelingen altijd één op de troon van Israël zal zitten, zolang zij uw wegen volgen en hun best doen uw wil te doen. 26Ja, God van Israël, vervul ook deze belofte die U mijn vader David hebt gedaan. 27Is het echt wel mogelijk dat U op aarde zou willen wonen? Zelfs de hoogste hemelen kunnen U niet bevatten, laat staan deze tempel die ik heb gebouwd. 28Hoor nu mijn gebed en luister naar mijn smeken, Here, mijn God. Beantwoord mijn roepen en luister naar het gebed van uw dienaar. 29Waak alstublieft dag en nacht over deze tempel, deze plaats waarin U, zoals U hebt beloofd, zult wonen om naar mij te luisteren wanneer ik tot U bid. 30Luister naar elke smeekbede van het volk Israël wanneer de mensen naar deze plaats komen om te bidden. Ja, luister vanuit de hemel, waar U woont en als U het hoort, vergeeft U dan alstublieft. 31Als een man wordt beschuldigd van een misdaad en hier, staande voor uw altaar, zweert dat hij het niet heeft gedaan, 32luister dan vanuit de hemel naar hem en doe wat juist is: geef de schuldige zijn verdiende loon en beloon de oprechte naar zijn verdienste. 33-34 En als uw onderdanen zondigen en hun vijanden verslaan hen, luister dan vanuit de hemel naar hen en vergeef hen als zij zich willen bekeren en opnieuw belijden dat U hun God bent. Breng hen dan terug naar dit land dat U hun voorouders hebt gegeven.

35-36 Als de hemelen zijn gesloten en er geen regen valt wegens hun zonde, luister dan vanuit de hemel en vergeef hen als zij op deze plaats bidden en uw naam aanroepen. Help hen dan om—nadat U hen hebt gestraft—de goede wegen te bewandelen en stuur regen naar het land dat U uw volk hebt gegeven.

37Als in het land hongersnood heerst of het wordt getroffen door plantenziekten of schadelijke insecten, zoals sprinkhanen of kevers, of als Israëls vijanden haar steden belegeren of als de mensen lijden onder een epidemie of een plaag—of wat voor problemen ook maar— 38-39 luister dan als zij hun zonde beseffen en bij deze tempel bidden, luister vanuit de hemel, vergeef en antwoord hen die een eerlijke bekentenis hebben afgelegd. U kent immers ieders hart. 40Op die manier zullen zij leren ontzag voor U te hebben, terwijl zij wonen in dit land dat U hun voorouders gaf.

41-42 En als buitenlanders uw naam horen noemen en uit verre landen komen om U te aanbidden (want zij zullen horen vertellen over uw grote naam en machtige wonderen) en bij deze tempel te bidden, 43luister dan naar hen vanuit de hemel en geef antwoord op hun gebeden. Alle volken van de aarde zullen uw naam kennen en ontzag voor U hebben, net als uw volk Israël, en de hele wereld zal weten dat U in deze tempel in ons midden bent.

44Als U uw volk laat vechten tegen zijn vijanden en het bidt tot U, terwijl zijn blik gericht is naar uw uitverkoren stad Jeruzalem en naar deze tempel die ik voor uw naam heb gebouwd, 45luister dan naar zijn gebed en help het.

46Als zij tegen U zondigen (en wie doet dat niet?) en U boos op hen wordt en toelaat dat hun vijanden hen als gevangenen wegleiden naar een ander land, dichtbij of veraf, 47en als zij daar beseffen wat zij hebben gedaan en U roepen met de woorden: “Wij hebben gezondigd, wij hebben het helemaal verkeerd gedaan,” 48als zij eerlijk naar U terugkeren en bidden in de richting van de stad Jeruzalem die U hebt gekozen en in de richting van deze tempel die ik voor uw naam heb gebouwd, 49luister dan naar hun bidden en smeken vanuit de hemel waar U woont en kom hen te hulp. 50Vergeef uw onderdanen al hun slechte daden waarmee zij tegen U zondigen en laten hun overwinnaars goed voor hen zijn. 51Want zij zijn uw volk, uw erfdeel, dat U bevrijdde uit de Egyptische oven. 52Mogen uw ogen geopend zijn en uw oren luisteren naar hun smeekbeden. O Here, luister naar hen en geef antwoord als zij tot U roepen. 53Want, Here God, toen U onze voorouders uit Egypte bevrijdde, hebt U door uw dienaar Mozes gezegd dat U uit alle volken op aarde Israël had uitgekozen om uw eigen volk te zijn.’

54-55 Salomo zat geknield met zijn handen uitgestrekt naar de hemel. Na zijn gebed stond hij op uit zijn geknielde houding voor het altaar van de Here en sprak luid de volgende zegen uit over het volk van Israël: 56‘Gezegend zij de Here, die zijn belofte heeft gehouden en zijn volk Israël rust heeft gegeven. Elk woord van zijn beloften die zijn dienaar Mozes afkondigde, is waarheid geworden. 57Moge de Here, onze God, met ons zijn zoals Hij met onze voorouders was, moge Hij ons nooit verlaten. 58Moge Hij ons het verlangen geven in alles zijn wil te doen en alle geboden en aanwijzingen te gehoorzamen die Hij onze voorouders heeft gegeven. 59En mogen deze woorden van mijn gebed de Here dag en nacht voor ogen staan, zodat Hij mij en heel Israël helpt en geeft wat wij dagelijks nodig hebben. 60Mogen de volken over de hele aarde weten dat de Here God is en dat geen enkele andere God bestaat. 61O mijn volk, leid een goed en oprecht leven voor de Here, onze God. Gehoorzaam altijd zijn wetten en geboden, net zoals u momenteel doet.’

62-63 Daarna wijdden de koning en alle aanwezigen de tempel in door het brengen van vredeoffers aan de Here, in totaal tweeëntwintigduizend runderen en honderdtwintigduizend schapen! 64Als tijdelijke maatregel heiligde de koning de hof vóór de tempel voor het brengen van brandoffers, spijsoffers en het vet van de vredeoffers, want het koperen altaar was te klein om zoveel offers ineens te verwerken.

65Voor deze gelegenheid vierden Salomo en het hele volk Israël veertien dagen lang feest en uit het hele land kwamen grote groepen mensen naar Jeruzalem, vanaf de Hamatpas in het noorden tot de beek bij de grens met Egypte. 66Na afloop stuurde Salomo de mensen terug naar huis.

Zij waren blij met de goedheid die de Here had getoond aan zijn dienaar David en het volk Israël. En bij hun afscheid zegenden zij de koning.