1 Mafumu 20 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 20:1-43

Beni-Hadadi Athira Nkhondo Samariya

1Tsono Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu inasonkhanitsa magulu ake onse a ankhondo. Iye pamodzi ndi mafumu 32, akavalo awo ndi magaleta awo, anapita kukawuzungulira mzinda wa Samariya ndi kuwuthira nkhondo. 2Iye anatuma amithenga ake mu mzindamo kwa Ahabu mfumu ya Israeli, kukanena kuti, 3“Beni-Hadadi akuti, ‘Siliva wako ndi golide wako ndi wanga, ndipo akazi ako okongola ndi ana ako ndi anganso.’ ”

4Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Monga mmene mwanenera, mbuye wanga mfumu, ine pamodzi ndi zonse zomwe ndili nazo ndi zanu.”

5Amithenga aja anabwereranso kwa Ahabu ndipo anamuwuza kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Ine ndinakulamula kuti undipatse siliva wako ndi golide wako, akazi ako ndi ana ako. 6Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatuma atumiki anga kudzafufuza mʼnyumba yako yaufumu ndi nyumba za akuluakulu ako. Iwo adzatenga chilichonse chimene umachidalira ndi kupita nacho.’ ”

7Pamenepo mfumu ya Israeli inayitanitsa akuluakulu a mʼdzikomo niwawuza kuti, “Taonani momwe munthuyu akufunira kutibweretsera mavuto! Atatumiza mawu oti ndimupatse akazi anga ndi ana anga, siliva wanga ndi golide wanga, ine sindinamukanize.”

8Akuluakulu onse ndi anthu onse anayankha kuti, “Musamumvere kapena kuvomereza zofuna zake.”

9Tsono Ahabu anayankha amithenga a Beni-Hadadi kuti, “Kamuwuzeni mbuye wanga mfumu kuti, ‘Mtumiki wanu adzachita zonse zimene munazifuna nthawi yoyamba ija, koma izi mwazifunazi sindingazikwanitse.’ ” Iwo anachoka nakapereka yankho kwa Beni-Hadadi.

10Pamenepo Beni-Hadadi anatumizanso uthenga wina kwa Ahabu kuti, “Milungu indilange koopsa, ngati mu Samariya mudzakhale fumbi loti nʼkudzaza dzanja la aliyense wa anthu anga.”

11Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Kamuwuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako nʼpachulu, nʼkulinga utakwerapo.’ ”

12Beni-Hadadi anamva uthenga umenewu pamene iye ankamwa ndi mafumu anzake mʼmatenti awo, ndipo analamula anthu ake kuti, “Konzekerani kukathira nkhondo.” Choncho anakonzekera kukathira nkhondo mzindawo.

Ahabu Agonjetsa Beni-Hadadi

13Ndipo taonani, mneneri wina anabwera kwa Ahabu mfumu ya Israeli nadzalengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi ukuchiona chigulu chachikulu cha ankhondochi? Taona, ndikuchipereka chimenechi lero mʼdzanja lako, ndipo pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

14Ahabu anafunsa kuti, “Koma ndani adzachita zimenezi?”

Mneneri anayankha kuti, “Yehova akuti, ‘Adzachita zimenezi ndi asilikali a nduna za mʼzigawo.’ ”

Ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndani adzayambe nkhondoyi?”

Mneneriyo anayankha kuti, “Ndinu.”

15Choncho Ahabu anawerenga asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndipo onse analipo 232. Ndipo anawerenganso ankhondo a ku Israeli ndipo onse analipo 7,000. 16Iwo ananyamuka nthawi yamasana pamene Beni-Hadadi ndi mafumu 32 othandizana naye ankamwa mpaka kuledzera mʼmatenti awo. 17Asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndiwo amene anayamba kupita ku nkhondo.

Nthawi imeneyi Beni-Hadadi nʼkuti atatumiza anthu oti akazonde, amene anadzafotokoza kuti, “Anthu ankhondo akubwera kuchokera ku Samariya.”

18Iye anati, “Kaya akubwera mwamtendere kapena mwankhondo, muwagwire amoyo.”

19Choncho asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo anatuluka mu mzinda, gulu lankhondo lili pambuyo pawo. 20Ndipo aliyense wa iwo anapha munthu wake. Ataona izi, Aaramu anathawa Aisraeli ali pambuyo pawo kuwapirikitsa. Koma Beni-Hadadi mfumu ya ku Aaramu anathawa atakwera pa kavalo pamodzi ndi ankhondo ena okweranso pa akavalo. 21Mfumu ya Israeli inapita chitsogolo ndi kugwira akavalo ndi magaleta ndipo Aaramu ambiri anaphedwa.

22Zitachitika izi, mneneri wina anabwera kwa mfumu ya Israeli ndipo anati, “Mulimbike ndipo muganize bwino zoti mudzachite, chifukwa chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzakuthiraninso nkhondo.”

23Nthawi imeneyi, akuluakulu a mfumu ya Aramu anamulangiza kuti, “Milungu ya anthu a ku Israeli ndi milungu ya mʼmapiri. Nʼchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambana ife. Koma ngati tidzamenyana nawo ku chigwa, ndithudi ife tidzakhala ndi mphamvu kuposa iwo. 24Inu chitani izi: chotsani mafumu onse pa maudindo awo ndipo mʼmalo mwawo muyikemo atsogoleri a ankhondo. 25Musonkhanitsenso gulu lankhondo lofanana ndi lomwe linaphedwa lija, akavalo monga omwe anaphedwa aja, ndi magaleta monga omwe anawonongedwa aja, kuti tikamenyane ndi Israeli ku chigwa. Pamenepo, ife tidzapambana iwowo.” Beni-Hadadi anagwirizana nawo ndipo anachita momwemo.

26Chaka chinacho Beni-Hadadi anasonkhanitsa Aaramu, napita ku Afeki kukamenyana ndi Israeli. 27Aisraeli atasonkhananso, napatsidwa zakudya zawo anapita kukakumana nawo. Aisraeli anamanga misasa yawo moyangʼanana ndi Aaramu ndipo ankaoneka ngati timagulu tiwiri ta mbuzi, pomwe Aaramu anali atakuta dera lonselo.

28Munthu wa Mulungu anabwera, nawuza mfumu ya Israeli kuti, “Yehova akuti, ‘Popeza Aaramu akuganiza kuti Yehova ndi mulungu wa ku mapiri, osati wa ku zigwa, Ine ndidzapereka chigulu chonsechi kwa iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

29Kwa masiku asanu ndi awiri anakhala moyangʼanana mʼmisasa yawo, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri nkhondo inayambika. Aisraeli anapha Aaramu okwana 100,000 tsiku limodzi lokha. 30Ena onse otsala anathawira ku Afeki, kumene khoma linagwera anthu 27,000. Ndipo Beni-Hadadi anathawira mu mzinda, nakabisala mʼchipinda chamʼkati.

31Atumiki ake anamuwuza kuti, “Taonani, ife tamva kuti mafumu a fuko la Israeli ndi achifundo. Tiyeni tipite kwa mfumu ya ku Israeli titavala ziguduli mʼchiwuno mwathu ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwathu. Mwina iye sakakuphani.”

32Atavala ziguduli mʼchiwuno mwawo ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwawo, anapita kwa mfumu ya ku Israeli ndipo anayiwuza kuti, “Mtumiki wanu Beni-Hadadi akunena kuti, ‘Chonde loleni kuti ndikhale moyo.’ ”

Mfumu inayankha kuti, “Kodi iye akanali ndi moyo? Iye ujatu ndi mʼbale wanga.”

33Anthuwo ankaganiza kuti mawuwo anali abwino ndipo anavomereza mawuwa mofulumira. Iwo anati, “Inde, Beni-Hadadi ndi mʼbale wanu!”

Mfumu inati, “Pitani kamutengeni.” Beni-Hadadi atatuluka, Ahabu anamukweza mʼgaleta lake.

34Beni-Hadadi anawuza Ahabu kuti, “Ndidzabweza mizinda imene abambo anga analanda abambo anu. Ndipo mutha kumanga nyumba zanu zamalonda mu Damasiko, monga anachitira abambo anga ku Samariya.”

Ahabu anati, “Chifukwa cha mgwirizano umenewu, ine ndidzakumasula.” Choncho anachita naye mgwirizano, ndipo anamulola kuti apite.

Mneneri Adzudzula Ahabu

35Molamulidwa ndi Yehova, mmodzi mwa ana a aneneri anawuza mnzake kuti, “Chonde, menye ndi chida chako,” koma mnzakeyo anakana.

36Choncho mneneriyo anati, “Chifukwa sunamvere Yehova, ukangochoka pano, mkango ukupha.” Ndipo munthuyo atangochoka pamenepo, mkango unamupeza ndi kumupha.

37Mneneriyo anapeza munthu wina ndipo anamuwuza kuti, “Chonde, menye.” Choncho munthuyo anamumenya ndi kumuvulaza. 38Pamenepo mneneriyo anapita nakayima pa msewu kudikirira mfumu. Iye anadzibisa nakulunga nsalu nkhope yake. 39Mmene mfumu inkadutsa pamenepo, mneneriyo anafuwula kwa mfumuyo kuti, “Ine mtumiki wanu ndinalowa pakati pa nkhondo, ndipo munthu wina anabwera kwa ine atatenga mmodzi mwa anthu ogwidwa pa nkhondo, nandiwuza kuti, ‘Sunga munthu uyu. Ngati asowa, ndiye kuti ndidzakupha, kapena udzalipira ndalama 3,000 za siliva.’ 40Pamene ine mtumiki wanu ndinali wotanganidwa apa ndi apa, munthuyo anasowa.”

Mfumu ya Israeli inati, “Chimenechi ndiye chilango chako. Iwe wadziweruza wekha.”

41Pamenepo mneneriyo anachotsa msangamsanga nsalu yomwe anakulunga pa nkhope yake, ndipo mfumu ya Israeli inamuzindikira kuti ndi mmodzi mwa aneneri. 42Iye anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chakuti mwamasula munthu amene Ine ndinati ndi woyenera kuphedwa, inuyo ndi amene mudzaphedwe mʼmalo mwa iyeyo, anthu anu mʼmalo mwa anthu ake.’ ” 43Mwachisoni ndi mokwiya, mfumu ya Israeli inapita ku nyumba yake yaufumu ku Samariya.

New Serbian Translation

1. Књига о царевима 20:1-43

Рат с Арамејцима

1Вен-Адад, арамејски цар, је сабрао сву своју војску; с њим је било тридесет два цара, с коњима и бојним колима. Он је отишао, опколио Самарију и напао је. 2Потом је послао гласнике Ахаву, цару израиљском, у град. 3Рекао му је: „Овако поручује Вен-Адад: ’Твоје сребро и злато припада мени, и твоје предивне жене и деца припадају мени.’“

4Цар израиљски одговори: „Како ти кажеш, господару мој, царе. Твој сам и ја и све што имам.“

5Гласници су поново дошли и рекли: „Овако каже Вен-Адад: ’Поручио сам ти: предај ми своје сребро и злато, своје жене и децу. 6Зато ћу ти сутра у ово време послати своје слуге и они ће претражити твоју кућу и куће твојих слугу, па ће узети све што ти је вредно и однети.’“

7Тада цар израиљски позва све старешине земље и рече: „Примите к знању и погледајте како тражи невољу; јер је послао по моје жене и децу, и по моје сребро и злато, а ја му нисам одбио.“

8Све старешине и сав народ му рекоше: „Не слушај, нити пристај!“

9Он рече Вен-Ададовим гласницима: „Реците своме господару цару: ’Учинићу све што си први пут тражио од свога слуге, али ово не могу да учиним.’“ Гласници оду и врате се са поруком.

10Вен-Адад му посла поруку: „Нека ми богови тако учине и нека додају, ако од Самарије остане толико пепела да сваки човек који ме следи добије по шаку.“

11Израиљски цар му одговори: „Каже се: ’Нека се не хвали онај који се опасује, него онај који се распасује.’“

12Кад је Вен-Адад чуо ову поруку док је пио са царевима под шаторима, рекао је својим слугама: „Крените!“ Они кренуше у град.

Ахав побеђује Вен-Адада

13Уто један пророк приступи Ахаву, цару израиљском, и рече: „Говори Господ: ’Видиш ли све ово велико мноштво? Ево, данас ћу га предати у твоје руке, да знаш да сам ја Господ.’“

14Ахав рече: „Преко кога?“ Пророк рече: „Говори Господ: ’Преко момака обласних намесника.’“

Он упита: „Ко ће започети битку?“

Пророк рече: „Ти.“

15Ахав је пребројао момке обласних намесника, њих две стотине тридесет два, а затим је пребројио сав народ, све Израиљце, њих седам хиљада. 16Изашли су у подне, док се Вен-Адад напијао са тридесет два цара, који су му дошли у помоћ. 17Прво су изашли момци обласних намесника.

Вен-Адад је послао извидницу, која му је јавила: „Изашли су људи из Самарије.“

18Он рече: „Ако су изашли ради мира, похватајте их живе, а ако су изашли ради рата, свеједно их похватајте живе.“

19Тако момци обласних намесника изађу из града, а војска за њима. 20Сваки је убио свог противника, те су се Арамејци разбежали. Израиљци су их гонили, али је Вен-Адад, арамејски цар, побегао на коњу с коњаником. 21Тада је изашао и израиљски цар и навалио на коње и бојна кола, и нанео Арамејцима велики пораз.

22Затим пророк приступи израиљском цару и рече му: „Иди и појачај своје снаге; размисли и види шта ћеш да урадиш, јер ће те арамејски цар напасти на почетку наредне године.“

23А слуге арамејског цара рекоше му: „Њихови богови су планински богови, и зато су нас савладали. Али ако се сукобимо са њима у равници, свакако ћемо их савладати. 24Учини овако: уклони цареве с њихових положаја, а уместо њих постави војводе. 25Затим скупи онакву војску какву си изгубио, исто толико коња и бојних кола, па ћемо се сукобити с њима у равници, и свакако ћемо их савладати.“ Он их је послушао, па је учинио тако.

Победа код Афека

26На почетку године, Вен-Адад скупи Арамејце и крене на Афек да ратује против Израиљаца. 27И Израиљци су се скупили и понели храну, па су им кренули у сусрет. Кад су се Израиљци утаборили насупрот њима, били су као два стада коза. Арамејци су, пак, прекрили земљу.

28Тада приступи човек Божији и рече израиљском цару: „Говори Господ: ’Зато што су Арамејци рекли: Господ је бог планина, а не бог долина, предаћу све ово велико мноштво у твоје руке, да знате да сам ја Господ.’“

29Седам дана су били утаборени једни наспрам других. Седмога дана је почела битка. Израиљци су побили стотину хиљада арамејских пешака у једном дану. 30Остали су побегли у Афек, у град, али се градски зид срушио на преосталих двадесет седам хиљада људи. Вен-Адад је побегао у град и ушао у тајну одају.

31Његове слуге му рекоше: „Чули смо да су цареви дома Израиљевог милостиви. Стога, хајде да ставимо кострет око бокова и конопце око глава и изађимо пред израиљског цара; можда ће ти поштедети живот.“

32Тако су опасали кострет око бокова и ставили конопце око глава, па су дошли к израиљском цару и рекли: „Твој поданик, Вен-Адад, каже: ’Молим те, поштеди ми живот.’“ Ахав на то рече: „Зар је још увек жив? Он је мој брат.“

33Тражећи неки знак, људи су хитро дочекали његову реч и рекли: „Јесте, Вен-Адад је твој брат!“ Он им рече: „Идите и доведите га.“ Вен-Адад изађе пред њега, а он га узе у своја бојна кола.

34Вен-Адад му рече: „Вратићу ти градове које је мој отац узео од твог оца, а можеш за себе да поставиш и тржнице у Дамаску, као што је мој отац поставио у Самарији.“

Ахав одговори: „Пустићу те на основу овог договора.“ Затим је склопио савез с њим и пустио га.

Пророк осуђује Ахава

35Али дође један од пророчких синова и рече једном од својих другова по речи Господњој: „Удари ме!“ Но, овај је одбио да га удари.

36Зато му пророк рече: „Пошто ниси послушао глас Господњи, ево, чим изађеш од мене, убиће те лав.“ Тек што је мало одмакао од њега, наишао је на њега лав и убио га. 37Затим је нашао другог човека и рекао му: „Удари ме!“ Човек га удари и израњави га.

38Пророк оде и стаде на пут да сачека цара. На очи је ставио повез да се прикрије. 39Кад је цар пролазио, он довикну цару и рече: „Твој је слуга ступио у са̂мо средиште битке, кад је неки човек дошао к мени и довео ми једног човека, рекавши: ’Чувај овог човека! Ако буде нестао, својим ћеш животом платити за његов живот, или ћеш платити таланат20,39 Око 34 kg. сребра.’ 40Али док је твој слуга био заузет овим и оним, он је нестао.“

Израиљски цар му рече: „Онда је то твоја пресуда; сам си је изрекао.“

41Али он брже-боље скиде повез са очију. Тада је цар израиљски видео да је то један од пророка. 42Он рече цару: „Говори Господ: ’Зато што си пустио човека кога сам одредио за клето уништење, својим ћеш животом платити за његов живот, и твој народ за његов народ.’“

43Цар израиљски оде својој кући, смркнут и љутит.