1 Akorinto 13 – CCL & CRO

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akorinto 13:1-13

Kupambana kwa Chikondi

1Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera. 2Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu. 3Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.

4Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. 5Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. 6Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. 7Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.

8Chikondi ndi chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha. 9Pakuti timadziwa zinthu pangʼono chabe ndipo timanenera pangʼono chabe. 10Koma changwiro chikadzaoneka ndipo chopereweracho chidzatha. 11Pamene ndinali mwana ndinkayankhula ngati mwana, ndinkaganiza ngati mwana, ndinkalingalira ngati mwana. Koma nditakula, zonse zachibwana ndinazisiya. 12Pakuti tsopano tiona zinthu mosaoneka bwino ngati mʼgalasi loonera; kenaka tidzaziona maso ndi maso. Tsopano ndidziwa mosakwanira koma kenaka ndidzadziwa mokwanira, monga mmene Mulungu akundidziwira ine.

13Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.

Knijga O Kristu

1 Korinćanima 13:1-13

Hvalospjev ljubavi

1Kad bih sve ljudske i anđeoske jezike govorio, a ljubavi ne bih imao, bio bih poput mjedi što ječi ili cimbala što zveči. 2Kad bih imao dar prorokovanja, kad bih razumio sva otajstva i imao sve znanje te takvu vjeru da bih i gore premještao, a ljubavi ne bih imao, bio bih—ništa. 3Kad bih siromasima razdao sav svoj imetak, kad bih i tijelo svoje predao da se sažeže, a ljubavi ne bih imao—ništa mi koristilo ne bi.

4Ljubav je strpljiva, ljubav je dobrostiva; ona ne zavidi, ne hvasta se, ne oholi se. 5Nije nepristojna, ne traži svoje pravo, nije razdražljiva, ne pamti zlo; 6ne raduje se nepravdi, nego istini. 7Sve izdržava, nikad ne gubi vjeru, uvijek se nada, sve podnosi.

8Ljubav nikad neće uminuti. Prorokovanje? Iščeznut će. Jezici? Zamuknut će. Znanje? Nestat će. 9Jer nepotpuno je naše znanje, nepotpuno naše prorokovanje. 10A kada dođe ono što je savršeno, uminut će ovo što je nepotpuno.

11Kad sam bio dijete, govorio sam kao dijete, razmišljao sam kao dijete, rasuđivao sam kao dijete. Kad sam postao zrelim čovjekom, odbacio sam što je djetinje. 12Sad vidimo u zrcalu, nejasno, a tada ćemo gledati licem u lice. Sada spoznajem nepotpuno, a tada ću spoznati savršeno, kao što sam i sam spoznan.

13A sada ostaje troje: vjera, nada i ljubav, ali najveća je među njima ljubav.