1 Akorinto 11 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akorinto 11:1-34

1Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu.

Makhalidwe Oyenera pa Mapemphero

2Ndikukuyamikani chifukwa chondikumbukira pa zonse ndiponso posunga ziphunzitso monga ndinakuphunzitsirani. 3Tsopano ndikufuna muzindikire kuti Khristu ndiye mutu wa munthu aliyense, ndipo mwamuna ndiye mutu wamkazi, ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu. 4Mwamuna aliyense wopemphera kapena kunenera ataphimba mutu wake akunyoza mutu wakewo. 5Ndipo mkazi aliyense wopemphera kapena kunenera asanaphimbe mutu wake sakulemekeza mutu wakewo. Kuli chimodzimodzi kumeta mutu wake. 6Ngati mkazi saphimba kumutu kwake, ndiye kuti amete tsitsi lake. Ngati nʼchamanyazi kwa mkazi kungoyepula kapena kumeta mpala, ndiye kuti aphimbe kumutu kwake.

7Mwamuna sayenera kuphimba kumutu popeza ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu; pamene mkazi ndi ulemerero wa mwamuna. 8Pakuti mwamuna sachokera kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna. 9Ndipo mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna. 10Pa chifukwa ichi, ndiponso pa chifukwa cha angelo, mkazi akuyenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro wake. 11Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi. 12Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa mwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu.

13Dziweruzeni. Kodi nʼchabwino kuti mkazi apemphere kwa Mulungu wopanda chophimba kumutu? 14Kodi chikhalidwe chathu sichitiphunzitsa kuti nʼchamanyazi kuti mwamuna akhale ndi tsitsi lalitali, 15koma mkazi akakhala ndi tsitsi lalitali ndi ulemerero wake? Pakuti mkazi anapatsidwa tsitsi lalitali monga chophimba kumutu. 16Ngati wina akufuna kutsutsapo pa zimenezi, ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe machitidwe ena apadera koma ndi omwewa.

Mgonero wa Ambuye

17Koma popereka malangizo awa sindikufuna kukuyamikirani popeza mʼmisonkhano yanu mumachita zoyipa kuposa zabwino. 18Choyamba, ndikumva kuti mukasonkhana mu mpingo mumasankhana ndipo ndikukhulupirira kuti zimenezi kwinaku nʼzoona. 19Nʼzosakayikitsa kuti pali kugawikana pakati panu kuti adziwike amene ndi ovomerezeka ndi Mulungu. 20Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye. 21Pakuti mukamadya, aliyense amangodzidyera zomwe anakonza. Wina amakhala ndi njala pamene wina amaledzera. 22Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni.

23Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye ndi zomwe ndinakupatsani. Ambuye Yesu, usiku umene anaperekedwa uja, anatenga buledi. 24Atayamika ndi kumunyema ananena kuti, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.” 25Chimodzimodzi, atatha kudya, anatenga chikho, nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga; imwani nthawi zonse pokumbukira Ine.” 26Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.

27Chifukwa chake, aliyense amene adya buledi kapena kumwa chikho cha Ambuye mʼnjira yosayenera adzachimwira thupi ndi magazi a Ambuye. 28Munthu adzisanthule yekha asanadye buledi kapena kumwa chikhochi. 29Popeza aliyense amene adya kapena kumwa mosazindikira thupi la Ambuye, amadya ndi kumwa chiweruzo chake chomwe. 30Nʼchifukwa chake pakati panu ambiri mwa inu ndi ofowoka ndi odwala, ndipo ambirinso agona tulo. 31Koma tikanadziyesa tokha sitikaweruzidwanso. 32Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

33Ndiye tsono abale anga, pamene musonkhana pa chakudya, mudikirirane. 34Ngati wina ali ndi njala, adye ku nyumba kwake kuti pamene musonkhana pamodzi zisafike poti muweruzidwe nazo.

Ndipo ndikabwera ndidzakupatsani malangizo ena owonjezera.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

哥林多前書 11:1-34

1你們要效法我,正如我效法基督一樣。

敬拜的禮儀

2我讚賞你們,因為你們凡事都想到我,並堅守我傳給你們的各種教導。

3我希望你們知道,基督是男人的頭,丈夫是妻子的頭,上帝是基督的頭。 4男人在禱告和講道時,若蒙著頭,就是羞辱自己的頭。 5但婦女在禱告和講道時,若不蒙著頭,就是羞辱自己的頭,因為她就像剃光了頭髮一樣。 6因此,如果婦女不願意把頭蒙起來,就該把頭髮剪掉。如果她覺得剪髮或剃頭是羞恥的,就應該蒙頭。 7然而,男人不該蒙頭,因為男人是上帝的形像和榮耀,而女人是男人的榮耀。 8因為男人並非出自女人,而女人卻是出自男人。 9並且男人不是為女人而造的,女人卻是為男人而造的。

10因此為了天使的緣故,女人在頭上應該有服權柄的記號。 11不過在主裡面,女人不可沒有男人,男人不可沒有女人。 12因為女人是從男人而來,男人又是女人生的,但萬物都是來自上帝。

13你們自行斟酌吧,女人向上帝禱告時不蒙頭合適嗎? 14按著人的天性,難道你們不知道男人留長髮是他的羞辱, 15女人留長髮是她的榮耀嗎?因為頭髮是用來給女人蓋頭的。 16如果有誰想反駁這些話,我只能說,這是我們和上帝的眾教會向來遵守的規矩。

守聖餐的規矩

17現在我有話要吩咐你們,不是稱讚你們,因為你們聚會不但無益,反而有害。 18首先,我聽說你們在聚會的時候拉幫結派,我相信這些話有幾分真實。 19你們中間必然會有分裂的事,好顯出誰是經得起考驗的。

20你們聚會的時候,不是在吃主的晚餐。 21因為你們進餐的時候,各人只顧吃自己的,結果有些人挨餓,有些人醉酒。 22難道你們不可以在家裡吃喝嗎?還是你們輕看上帝的教會,存心羞辱那些貧窮的弟兄姊妹呢?我該說什麼呢?稱讚你們嗎?不可能!

23我把從主領受的傳給了你們,就是:主耶穌被出賣的那天晚上,祂拿起一個餅來, 24向上帝祝謝後掰開,說,「這是我的身體,是為你們掰開的,你們要這樣做,為的是紀念我。」 25晚餐後,祂又照樣拿起杯來,說,「這杯是用我的血立的新約。你們每逢喝的時候,要這樣做,為的是紀念我。」 26所以,每當你們吃這餅、喝這杯的時候,就是宣告主的死,一直到主再來。

27因此,無論是誰,若以不正確的心態吃主的餅、喝主的杯,就是得罪主的身體和主的血。 28所以,人要先自我省察,才可以吃這餅喝這杯。 29因為守聖餐的時候,若有人隨便吃喝,忘記了這是主的身體,他就是自招審判。 30正因如此,你們當中有許多人身體軟弱,疾病纏身,死亡的也不少。 31如果我們先自我省察,就不會遭受審判了。 32主審判我們,是對我們的管教,免得我們和世人一同被定罪。

33因此,我的弟兄姊妹,當你們吃聖餐時,要彼此等候。 34如果有人饑餓,可以在家中先吃,免得你們聚會的時候自招審判。至於其餘的事,等我到了以後再安排。