列王紀下 6 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

列王紀下 6:1-33

以利沙找回斧頭

1一群先知對以利沙說:「你看,我們住的地方實在太小了。 2請讓我們去約旦河吧,我們每人都可以從那裡砍一根木頭蓋房子居住。」以利沙說:「你們去吧。」 3其中一人請以利沙一起去,以利沙答應了, 4便和他們一起去約旦河砍伐樹木。 5有個人砍樹的時候,斧頭掉進了水裡。他大喊:「唉!師傅,這把斧頭是借來的。」 6上帝的僕人問:「斧頭掉在哪裡了?」他就指給以利沙看。以利沙砍了一根樹枝拋進水裡,斧頭便浮了上來。 7以利沙說:「你去拿上來吧!」他便伸手拿起了斧頭。

以利沙使亞蘭軍敗退

8亞蘭王與以色列人交戰,他和臣僕商議要在某處安營。 9上帝的僕人派人去稟告以色列王說:「你要小心,不要經過那個地方,因為亞蘭人埋伏在那裡。」 10以色列王派人到上帝的僕人所說的地方,警告那裡的人要小心防備。這樣的事情發生了好幾次。

11亞蘭王因此十分惱怒,召來臣僕質問他們:「你們當中誰向以色列王洩露了我們的計劃?」 12一位臣僕說:「我主我王啊,沒有人洩露。是以色列的先知以利沙將王在寢宮所談的事告訴了以色列王。」 13王說:「去找出他在哪裡,我派人去捉拿他。」王得知以利沙多坍後, 14便派出大隊人馬和戰車前往那裡,他們在夜間抵達多坍,把城圍住。 15上帝僕人的侍者清早起來,走到外面,看見城被軍隊、車馬包圍,就對上帝的僕人說:「唉!我主啊,怎麼辦呢?」 16上帝的僕人說:「不要害怕!我們的人比他們的還要多。」 17他隨後禱告:「耶和華啊,求你開他的眼睛,讓他看見。」於是,耶和華開那個僕人的眼睛,他就看見山上到處都是火車火馬圍繞著以利沙18亞蘭人向以利沙衝來,以利沙祈求耶和華說:「求你使他們瞎眼。」耶和華聽了以利沙的禱告,使他們瞎了眼。 19以利沙對他們說:「不是這條路,也不是這座城。跟我來,我帶你們到你們要找的人那裡。」以利沙把他們領到撒瑪利亞

20他們進城後,以利沙禱告:「耶和華啊,求你開他們的眼睛,讓他們看見。」耶和華開了他們的眼睛,他們就看見了,發現自己在撒瑪利亞城中。 21以色列王看見他們,問以利沙說:「我父啊,我可以殺他們嗎?」 22以利沙答道:「不可殺他們。豈可殺從戰場上抓來的俘虜呢?給他們吃的喝的,讓他們回自己主人那裡吧。」 23於是,以色列王為他們大擺宴席,等他們吃喝完畢,便放他們回自己主人那裡。之後,亞蘭人不再侵犯以色列

撒瑪利亞城被圍困

24後來,亞蘭便·哈達召集全軍圍困撒瑪利亞25撒瑪利亞被困後,城裡陷入嚴重饑荒,以致一個驢頭可賣九百克銀子,二百克鴿子糞可賣十一克銀子。 26一天,以色列王從城牆上走過,一個婦人向他哭喊道:「我主我王啊,求你幫幫我!」 27王說:「如果耶和華不幫助你,我怎能幫助你呢?我既無糧也無酒。 28你有什麼難處呢?」 29婦人說:「這個女人對我說,『我們今天吃你兒子,明天再吃我兒子。』於是我們把我兒子煮了吃。第二天我叫她把她兒子交出來,她卻把兒子藏了起來。」 30王聽了婦人的話,就撕裂衣服。王走在城牆上,人們都看見他貼身穿著麻衣。 31王說:「如果今天沙法的兒子以利沙的頭顱還留在他頸項上,願上帝重重地懲罰我!」

32王派使者去以利沙那裡。那時,以利沙正與長老們坐在他家中。使者到達之前,以利沙對長老說:「你們看,這兇手派人來斬我的頭。使者到達時,你們要把他關在門外。他後面不就是他主人的腳步聲嗎?」 33話音未落,使者已經到了,說:「既然這禍是從耶和華來的,我何必再仰望祂呢?」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 6:1-33

Nkhwangwa Iyandama pa madzi

1Ana a aneneri anati kwa Elisa, “Taonani malo amene timakhala ndi inu atichepera kwambiri. 2Tiloleni tipite ku Yorodani kumene aliyense wa ife akadule mtengo umodzi, kuti timange malo woti tizikhalamo.”

Ndipo Elisa anati, “Pitani.”

3Mmodzi wa iwo anati, “Chonde mulole kutsagana nawo atumiki anu.”

Elisa anayankha kuti, “Ndipita nanu.” 4Ndipo anapita nawo.

Anapita ku Yorodani nayamba kudula mitengo. 5Pamene wina ankadula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka nigwera mʼmadzi. Iye anafuwula kuti, “Mayo! Mbuye wanga! Popeza ndi yobwereka!”

6Ndipo munthu wa Mulungu uja anafunsa, “Yagwera pati?” Pamene anamuonetsa malowo, Elisa anadula kamtengo nakaponya pamenepo, ndipo nkhwangwayo inayandama. 7Elisa anati, “Itenge.” Ndipo munthuyo anatambalitsa dzanja lake nayitenga.

Elisa Achititsa Khungu Ankhondo a ku Aramu

8Tsono mfumu ya ku Aramu inali pa nkhondo ndi Israeli. Itakambirana ndi atsogoleri ake ankhondo inati, “Ndidzamanga misasa yanga pamalo akutiakuti.”

9Munthu wa Mulungu anatumiza mawu kwa mfumu ya ku Israeli kuti “Musamale podutsa malo akuti, chifukwa Aaramu akupita kumeneko.” 10Choncho mfumu ya ku Israeli inatuma anthu kumalo kumene munthu wa Mulunguyo ananena. Nthawi ndi nthawi Elisa ankachenjeza mfumu, kotero kuti ankakhala tcheru ku malo amenewo.

11Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri mfumu ya ku Aramu. Mfumuyo inayitanitsa atsogoleri ake ankhondo ndipo inawafunsa kuti, “Kodi simungandiwuze munthu amene pakati pathu pano ali mbali ya mfumu ya ku Israeli?”

12Mmodzi mwa atsogoleri a ankhondowo anati, “Palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu, inu mbuye wanga, koma Elisa mneneri amene ali ku Israeli amawuza mfumu ya ku Israeli mawu enieni amene inu mumayankhula ku chipinda kwanu.”

13Choncho mfumu inalamula kuti, “Pitani, kafufuzeni kumene akukhala kuti ine nditume anthu kukamugwira.” Anthuwo anabweretsa mawu oti, “Taonani, Elisa ali ku Dotani.” 14Ndipo mfumu inatumizako magaleta ndi akavalo ndiponso gulu lankhondo lamphamvu. Anapita usiku nakawuzungulira mzindawo.

15Mtumiki wa munthu wa Mulungu atadzuka mmamawa ndi kutuluka panja, gulu la ankhondo pamodzi ndi akavalo ndi magaleta anali atazungulira mzindawo. Mtumikiyo anafunsa kuti, “Kalanga mbuye wanga, tidzachita chiyani?”

16Mneneri anamuyankha kuti, “Usachite mantha. Amene ali mbali yathu ndi ambiri kupambana amene ali mbali yawo.”

17Ndipo Elisa anapemphera kuti, “Inu Yehova tsekulani maso ake kuti aone.” Pamenepo Yehova anatsekula maso a mtumikiyo, ndipo anayangʼana naona kuti phiri lonse linali lodzaza ndi akavalo ndi magaleta a moto atazungulira Elisa.

18Pamene adaniwo ankabwera kudzalimbana naye, Elisa anapemphera kwa Yehova kuti, “Achititseni khungu anthu awa.” Kotero Yehova anawachititsa khungu monga anapemphera Elisa.

19Elisa anawawuza ankhondowo kuti, “Njira si imeneyi ndipo mzinda sumenewunso. Tsateni, ndipo ndidzakutengerani kwa munthu amene mukumufunayo.” Ndipo anawatengera ku Samariya.

20Atalowa mu mzinda wa Samariya, Elisa anati, “Yehova tsekulani maso a anthu awa kuti aone.” Choncho Yehova anatsekula maso awo ndipo anangoona kuti ali mʼkati mwenimweni mwa Samariya.

21Mfumu ya ku Israeli itawaona, inafunsa Elisa kuti, “Abambo anga, kodi ndiwaphe? Kodi ndiwaphe?”

22Elisa anayankha kuti, “Musawaphe. Kodi mungaphe anthu amene munawagwira pogwiritsa ntchito lupanga ndi uta? Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa kenaka apite kwa mbuye wawo.” 23Choncho anawakonzera mphwando lalikulu, ndipo atatsiriza kudya ndi kumwa, anawatumiza kwawo ndipo anabwerera kwa mbuye wawo. Kotero magulu a ankhondo a ku Aramu analeka kuthira nkhondo dziko la Israeli.

Njala mu Mzinda wa Samariya

24Patapita nthawi, Beni-Hadadi mfumu ya Aramu anasonkhanitsa gulu lake lonse la ankhondo, napita kukazungulira mzinda wa Samariya. 25Mu mzinda wa Samariya munali njala yoopsa. Ndipo taonani, Aaramu anazungulira mzindawu kwa nthawi yayitali kotero kuti mutu wa bulu ankawugulitsa ndalama za siliva 80, ndipo magalamu 200 a zitosi za nkhunda ankawagulitsa pa mtengo wa masekeli asanu.

26Pamene mfumu inkayenda pa khoma la mzindawo, mayi wina anafuwulira mfumuyo kuti, “Thandizeni mbuye wanga mfumu!”

27Mfumu inayankha kuti, “Ngati Yehova sakuthandiza iwe, ine thandizo lako ndingalipeze kuti? Kuchokera ku malo opunthira tirigu kodi? Kuchokera kumalo opsinyira mphesa kodi?” 28Pamenepo mfumuyo inafunsa mayiyo kuti, “Kodi chakuvuta nʼchiyani?”

Iye anayankha kuti, “Mayi uyu anandiwuza kuti, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye lero, ndipo mawa tidzadya mwana wangayu.’ 29Choncho tinaphika mwana wanga ndi kumudya. Tsiku lotsatira lakelo ine ndinati, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye,’ koma iye anabisa mwana wakeyo.”

30Mfumu itamva mawu a mayiyo, inangʼamba mkanjo wake. Pamene inkayenda pa khoma, anthu anayangʼana, ndipo anaona zovala zamʼkati, pakuti anavala chiguduli. 31Mfumuyo inati, “Mulungu andilange, andilange kwambiri ndikapanda kudula mutu wa Elisa mwana wa Safati lero!”

32Tsono Elisa nʼkuti atakhala mʼnyumba mwake, ndipo akuluakulu anali naye limodzi. Mfumu inatuma munthu wina kuti imutsogolere, koma asanafike, Elisa anawuza akuluakuluwo kuti, “Kodi simukuona momwe wopha munthu uja watumizira munthu wina kuti adzadule mutu wanga? Taonani mthengayo akafika, mutseke chitseko ndipo muchigwiritsitse kuti asalowe. Kodi ndikumvawo pambuyo pake si mgugu wa mbuye wake?”

33Elisa akuyankhulabe ndi anthuwo, taonani, wamthengayo anafika kwa iye. Ndipo mfumu inati, “Mavuto amenewa ndi ochokera kwa Yehova. Kodi nʼchifukwa chiyani ine ndiyenera kudikira thandizo lochokera kwa Yehova?”