以賽亞書 37 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以賽亞書 37:1-38

希西迦向以賽亞求助

1希西迦王聽後就撕裂衣服,披上麻衣,進入耶和華的殿。 2他派身披麻衣的宮廷總管以利亞敬、書記舍伯那和祭司中的長者去見亞摩斯的兒子以賽亞先知, 3對他說:「希西迦說,『今日是遭難、蒙羞、受辱的日子,就像嬰兒要出生,產婦卻無力生產一樣。 4亞述王派他的元帥來辱罵永活的上帝,也許你的上帝耶和華聽見那些話,就懲罰他。請你為我們這些剩下的人禱告。』」 5希西迦王的臣僕說完後, 6以賽亞對他們說:「告訴你們主人,耶和華這樣說,『你不要因亞述王的僕人那些褻瀆我的話而害怕。 7我必驚動37·7 驚動」希伯來文是「使靈進入」。亞述王的心,讓他聽見風聲後便返回本國,使他在那裡死於刀下。』」

8亞述的將軍聽說亞述王已經離開拉吉,便回去見王,發現王在攻打立拿9亞述王聽說古實特哈加要來攻打他,就派使者去對希西迦說: 10「不要讓你所倚靠的上帝愚弄你,說什麼耶路撒冷必不會落在亞述王手中。 11你肯定聽過亞述諸王掃滅列國的事,難道你能倖免嗎? 12我先祖毀滅了歌散哈蘭利色提·拉撒伊甸人,這些國家的神明救得了他們嗎? 13哈馬王、亞珥拔王、西法瓦音城的王、希拿王和以瓦王如今在哪裡呢?」

希西迦的禱告

14希西迦從使者手中接過信,讀完後走進耶和華的殿,在耶和華面前展開信, 15禱告說: 16「坐在二基路伯天使之上、以色列的上帝——萬軍之耶和華啊,唯有你是天下萬國的上帝,你創造了天地。 17耶和華啊,求你側耳垂聽!耶和華啊,求你睜眼察看!求你聽聽西拿基立派人來辱罵永活上帝的話。 18耶和華啊,亞述諸王確實掃滅列國,使其土地荒涼, 19把他們的神像丟進火中燒毀。因為那些神像只是人用木頭石頭製造的,根本不是神。 20我們的上帝耶和華啊,現在求你從亞述王手中拯救我們,讓天下萬國都知道唯有你是耶和華。」

預言亞述必敗

21亞摩斯的兒子以賽亞先知派人對希西迦說:「以色列的上帝耶和華說,『因為你就亞述西拿基立的事向我禱告, 22以下是耶和華對他的判語,

錫安的居民藐視你,嘲笑你;

耶路撒冷的居民朝你逃竄的背影搖頭。

23『你在侮辱、褻瀆誰呢?

你不放在眼裡、高聲罵的是誰呢?

以色列的聖者!

24你藉你的使者侮辱主。

你說你帶著許多戰車上到群山之巔,

上到黎巴嫩的巔峰,

砍下最高的香柏樹和上好的松樹,

征服最高的山和最美的樹林。

25你說你已在外邦之地挖井喝水,

已用腳掌踏乾埃及的河流。

26『難道你不知這是我在遠古所定的嗎?

如今我要實現我昔日所定的計劃,

就是藉著你使堅城淪為廢墟。

27城中的居民軟弱無力,

驚慌失措,羞愧難當,

脆弱如野草和菜蔬,

又像還未長大就被曬焦的房頂草。

28『你起你坐,你出你進,

你向我發怒,我都知道。

29因為你向我發怒,

你狂傲的話達到了我耳中,

我要用鉤子鉤住你的鼻子,

把嚼環放在你嘴裡,

使你原路返回。』

30希西迦啊,我要給你一個兆頭。你們今年明年要吃野生的,後年要撒種,收割,栽種葡萄園,吃園中的果子。 31猶大的倖存者要再次向下扎根,向上結果。 32因為將有餘民從耶路撒冷出來,有倖存者從錫安山出來。萬軍之耶和華必熱切地成就這事。 33至於亞述王,耶和華說,『他必不能進城或向這裡射一箭,必不能手持盾牌兵臨城下或修築攻城的高臺。 34他必原路返回,不得進入這城。這是耶和華說的。 35我必為自己和我僕人大衛而保護、拯救這城。』」

36於是,耶和華的天使到亞述營中殺了十八萬五千人。人們清早起來,發現到處是屍體。 37亞述西拿基立便拔營回國,住在尼尼微38有一天,他在廟中祭拜他的神明尼斯洛的時候,他兒子亞得米勒沙利色用刀殺了他,然後逃往亞拉臘。他兒子以撒哈頓繼位。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 37:1-38

Hezekiya Apempha Thandizo kwa Yehova

1Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. 2Iye anatuma Eliyakimu woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. 3Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.’ 4Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a kazembe amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.”

5Akuluakulu a mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, 6Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. 7Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”

8Kazembe wa ankhondo uja atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.

9Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi akubwera kudzachita naye nkhondo. Atamva zimenezi, anatumiza amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: 10“Kawuzeni Hezekiya mfumu ya ku Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ 11Ndithudi iwe unamva zimene mafumu a ku Asiriya akhala akuchitira mayiko onse. Iwo anawawononga kotheratu. Tsono iwe ndiye ndi kupulumuka? 12Makolo anga anawononga mizinda ya Gozani, Harani, Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu inayi ija anawapulumutsa anthu a mizindayi? 13Kodi mafumu a ku Hamati, Aripadi, Safaravaimu, Hena ndi Iva ali kuti?”

Pemphero la Hezekiya

14Hezekiya analandira kalata kwa amithenga nayiwerenga pomwepo. Hezekiya anapita ku Nyumba ya Yehova ndipo anayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova: 16“Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 17Inu Yehova tcherani khutu ndipo mumve. Inu Yehova, tsekulani maso anu ndipo muone. Imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza, kunyoza Mulungu wamoyo.

18“Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu yonse ya anthu ndi mayiko awo. 19Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu. 20Tsono Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼdzanja lake kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndiye Mulungu.”

Yehova Ayankha Pemphero la Hezekiya

21Tsono Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga wochokera kwa Yehova kwa Hezekiya poyankha pemphero lake lokhudza Senakeribu mfumu ya ku Asiriya. 22Mawu amene Yehova wayankhula motsutsana naye ndi awa:

“Mwana wamkazi wa Ziyoni

akukunyoza ndi kukuseka.

Mwana wamkazi wa Yerusalemu,

akupukusa mutu wake pamene iwe ukuthawa.

23Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira ndani?

Kodi iwe wafuwulira

ndi kumuyangʼana monyada ndani?

Watsutsana ndi Woyerayo wa Israeli!

24Kudzera mwa amithenga ako

iwe wanyoza Ambuye.

Ndipo wanena kuti,

‘Ndi magaleta anga ochuluka

ndafika pamwamba pa mapiri,

pamwamba penipeni pa mapiri a Lebanoni.

Ndagwetsa mitengo yamkungudza yayitali kwambiri,

ndi mitengo yabwino kwambiri ya payini.

Ndafika pa msonga pake penipeni,

nkhalango yake yowirira kwambiri.

25Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo

ndi kumva madzi akumeneko

ndi mapazi anga

ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’

26“Kodi sunamvepo

kuti zimenezi ndinazikonzeratu kalekale?

Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;

tsopano ndazichitadi,

kuti iwe kwako nʼkusandutsa mizinda yotetezedwa

kukhala milu ya miyala.

27Anthu amene ankakhala kumeneko analibenso mphamvu,

ankada nkhawa ndi kuchititsidwa manyazi.

Anali ngati mbewu za mʼmunda,

ngati udzu wanthete,

ali ngati udzu omera pa denga,

umene mphepo imawumitsa usanakule nʼkomwe.

28“Koma Ine ndimadziwa zonse za iwe;

ndimadziwa pamene ukuyima ndi pamene ukukhala; ndimadziwa pamene ukutuluka ndi pamene ukulowa,

ndiponso momwe umandikwiyira Ine.

29Chifukwa umandikwiyira Ine

ndi kuti mwano wako wamveka mʼmakutu anga,

ndidzakola mphuno yako ndi mbedza

ndikuyika chitsulo mʼkamwa mwako,

ndipo ndidzakubweza pokuyendetsa

njira yomwe unadzera pobwera.

30“Iwe Hezekiya, chizindikiro chako cha zimene zidzachitike ndi ichi:

“Chaka chino mudzadya zimene zamera zokha,

ndipo chaka chachiwiri zimene zaphukira pa zomera zokha,

koma chaka chachitatu mudzafesa ndi kukolola,

mudzawoka mitengo yamphesa ndi kudya zipatso zake.

31Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsalire

adzazika mizu yawo pansi ndipo adzabereka zipatso poyera.

32Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,

ndi ku phiri la Ziyoni gulu la anthu opulumuka.

Changu cha Yehova Wamphamvuzonse

chidzachita zimenezi.

33“Choncho Yehova akunena izi za mfumu ya ku Asiriya:

“Iye sadzalowa mu mzinda umenewu

kapena kuponyamo muvi uliwonse.

Sadzafika pafupi ndi mzindawu ndi ankhondo ake a zishango

kapena kuwuzinga ndi mitumbira yankhondo.

34Adzabwerera potsata njira yomwe anadzera pobwera;

sadzalowa mu mzinda umenewu,”

akutero Yehova.

35“Ine ndidzawuteteza ndi kuwupulumutsa mzindawu,

chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha pangano ndi mtumiki wanga Davide!”

36Tsopano mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya nkhondo ya ku Asiriya ndikukapha asilikali 185,000. Podzuka mmawa mwake anthu anangoona mitembo ponseponse! 37Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anasasula misasa nʼkuchoka kubwerera kukakhala ku Ninive.

38Tsiku lina, pamene ankapembedza mʼnyumba ya mulungu wake, Nisiroki, ana ake awiri, Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga, ndipo anathawira mʼdziko la Ararati. Ndipo mwana wake Esrahadoni analowa ufumu mʼmalo mwake.