以賽亞書 23 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以賽亞書 23:1-18

關於泰爾的預言

1以下是關於泰爾的預言:

他施的船隻哀號吧!

因為從基提23·1 基提」就是現在的塞浦路斯。傳來消息,

泰爾已被毀滅,

房屋和港口都蕩然無存。

2海邊的居民,西頓23·2 先知在本預言中提到西頓,是因為泰爾和西頓都在同一地區,都屬於腓尼基人。的商賈啊,

要靜默無言。

你們的商人飄洋過海,

3西曷的糧食、尼羅河流域的農產都運到泰爾

泰爾成為列國的商埠。

4西頓啊,你要羞愧!

你這海上的堡壘啊,

大海否認你,說:

「我沒有經歷過產痛,

沒有生過孩子,

也未曾養育過兒女。」

5埃及人聽見泰爾的消息,

都感到傷痛。

6海邊的居民啊,你們要去他施

你們要哀號!

7這就是你們那歷史悠久、

充滿歡樂的城嗎?

她曾經派人到遠方居住。

8泰爾曾是封王之地,

她的商賈是王侯,

她的商人名聞天下。

但她如今的遭遇是誰定的?

9是萬軍之耶和華定的,

為要摧毀因榮耀而生的驕傲,

羞辱世上的尊貴者。

10他施的人民啊,

要像尼羅河一樣穿行在自己的土地上,

因為再沒有人壓制你們。

11耶和華已經在大海之上伸出懲罰之手,

使列國震動。

祂已下令毀滅迦南的堡壘。

12祂說:「受欺壓的西頓人啊,

你們再也不能歡樂了!

你們就是逃到基提

也得不到安寧。」

13看看迦勒底人的土地,那裡已杳無人煙!亞述人使它成為野獸出沒之地,他們築起圍城的高臺,摧毀它的宮殿,使它淪為廢墟。

14他施的船隻都哀號吧!

因為你們的堡壘已被摧毀。

15到那日,泰爾必被遺忘七十年,正好一個王的壽數。七十年之後,泰爾必如歌中所描述的妓女:

16「被遺忘的妓女啊,

拿起琴,走遍全城。

要彈得美妙,要多唱幾首歌,

好使人再記起你。」

17那時,耶和華必眷顧泰爾。她必重操舊業,與天下萬國交易。 18但她得到的利潤和收入不會被積攢或儲存起來,而是要被獻給耶和華,用來供應那些事奉耶和華的人,使他們吃得飽足,穿得精美。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 23:1-18

Za Chilango cha Turo

1Uthenga wonena za Turo:

Lirani mofuwula, inu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi:

pakuti mzinda wa Turo wawonongedwa

ndipo mulibe nyumba kapena dooko.

Zimenezi anazimva

pochokera ku Kitimu.

2Khalani chete inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja,

inu amalonda a ku Sidoni,

iwe amene unalemera ndi anthu oyenda pa nyanja.

3Pa nyanja zazikulu

panabwera tirigu wa ku Sihori;

zokolola za ku Nailo, ndipo munachita malonda

ndi anthu a mitundu ina.

4Chita manyazi, iwe Sidimu

pakuti nyanja yayankhula, linga la ku nyanja (Turo) layankhula kuti,

“Sindinamvepo zowawa za kubereka kapena kuberekapo mwana;

sindinalerepo ana aamuna kapena kulera ana aakazi.”

5Mawuwa akadzamveka ku Igupto,

iwo adzachita mantha akadzamva kuti Turo wawonongeka.

6Wolokerani ku Tarisisi,

lirani mofuwula, inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja.

7Kodi uwu si mzinda wachisangalalo uja,

mzinda wakalekale,

umene anthu ake ankapita

kukakhala ku mayiko akutali?

8Kodi ndani anakonza zimenezi kuti zigwere Turo, mzinda umene unakhazikitsa mizinda ina,

mzinda umene amalonda ake ndi akalonga

ndi otchuka

pa dziko lapansi?

9Yehova Wamphamvuzonse anakonza zimenezi

kuti athetse kunyada kwawo

ndi kutsitsa anthu otchuka a pa dziko lapansi.

10Mubalalike mʼdziko mwanu ngati mtsinje wa Nailo

inu anthu a ku Tarisisi,

pakuti mulibenso chokutetezani.

11Yehova watambasula dzanja lake kuloza ku nyanja

ndipo wagwedeza maufumu ake.

Iye walamula kuti Kanaani

agwetse malinga ake.

12Iye anati, “Simudzakondwanso konse,

inu anthu opanikizidwa a ku Sidoni, tsopano wamphwanyidwa!

“Ngakhale muwolokere ku Kitimu,

kumeneko simukapezako mpumulo.”

13Onani dziko la Ababuloni,

anthu amenewa tsopano atheratu!

Asiriya asandutsa Turo kukhala

malo a zirombo za ku chipululu;

anamanga nsanja zawo za nkhondo,

anagumula malinga ake

ndipo anawasandutsa bwinja.

14Lirani mofuwula, inu anthu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi;

chifukwa malinga ako agwetsedwa!

15Pa nthawi imeneyo Turo adzayiwalika pa zaka 70, amene ndi masiku a moyo wa mfumu. Koma potsiriza pa zaka 70 zimenezi, Turo adzakhala ngati mkazi wachiwerewere woyimbidwa mu nyimbo:

16“Tenga zeze wako uzungulire mzinda,

iwe mkazi wachiwerewere woyiwalika;

imba zeze mokometsera, imba nyimbo zambiri,

kuti anthu akukumbukire.”

17Pakutha pa zaka 70, Yehova adzachitapo kanthu pa Turo. Iye adzabwerera ku ntchito yake yakale monga mkazi wachiwerewere ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu onse a dziko lapansi. 18Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Yehova; sadzazikundika kapena kuzisunga. Phindu lake lidzapita kwa mtumiki wa Yehova kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.