罗马书 16 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

罗马书 16:1-27

介绍菲比

1现在我给你们推荐我们的姊妹菲比,她是坚革哩教会的女执事。 2请你们因为在主里的关系,照着做圣徒的本分接待她。无论她有什么需要,请你们帮助她,因为她帮助过许多人,也帮助过我。

问候圣徒

3请代我问候百基拉亚居拉夫妇,他们是我在基督耶稣里的同工, 4为了救我将生死置之度外。不但我感谢他们,就是外族人的教会也感谢他们。 5请问候在他们家中聚会的教会。请问候我所爱的以拜尼土,他在亚细亚最先信主。 6请问候玛丽亚。她为你们受尽了劳苦。 7请问候安多尼古犹尼亚,他们是我的亲人,曾与我一同坐牢,同受患难,在使徒中很有名望,比我先信基督。 8请问候我在主里所爱的暗伯利9请问候在基督里与我同工的耳巴奴和我所爱的士大古10请问候亚比利,他在基督里曾受过考验。请问候亚利多布全家。 11请问候我的亲戚希罗天。请问候拿其数家中的信徒。 12请问候土非娜土富撒,她们都为主劳苦。请问候我所爱的彼息,她为主多受劳苦。 13请问候主所拣选的鲁孚,也问候他的母亲,他的母亲就是我的母亲。 14请问候亚逊其土弗勒干黑米八罗巴黑马和他们当中的其他弟兄姊妹。 15请问候非罗罗古犹利亚尼利亚和他的妹妹、阿林巴和他们那里的众圣徒。 16你们要以圣洁的吻彼此问候。基督的众教会都问候你们。

提防悖逆者

17弟兄姊妹,我劝你们要留意那些制造分裂、设置障碍、背离你们所学之道的人,你们要避开他们。 18他们并不是在事奉我们的主基督,只是为了满足自己的欲望,用花言巧语欺骗单纯善良的人。 19你们对主的顺服已人人皆知,我为你们高兴,我希望你们在好事上聪明,在坏事上无知。 20赐平安的上帝快要把撒旦践踏在你们脚下了。愿我们主耶稣的恩典常与你们同在!

其他人的问候

21我的同工提摩太和我的亲属路求耶孙所西巴德问候你们。 22我这为保罗代笔写信的德特在主里问候你们。 23接待我也接待全教会的该犹问候你们。 24主管本城财政的以拉都问候你们,括土弟兄也问候你们。

25感谢上帝!祂能使你们刚强,正如我所传讲的福音和耶稣基督的教导。这福音是自古隐藏、从未显明的奥秘, 26如今按着永恒上帝的命令,借着先知们所写的经书公诸于世,让世人都信从耶稣基督。 27愿荣耀借着耶稣基督归于独一全智的上帝,直到永远。阿们!

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aroma 16:1-27

Mawu Olawirana

1Ine ndikupereka kwa inu mlongo wathu Febe, mtumiki wa mpingo wa ku Kenkreya. 2Ine ndikukupemphani kuti mumulandire mwa Ambuye mʼnjira yoyenera oyera mtima ndi kumupatsa thandizo lililonse limene akulifuna kuchokera kwa inu, pakuti iye wakhala thandizo lalikulu kwa anthu ambiri kuphatikiza ine.

3Perekani moni kwa Prisila ndi Akura, atumiki anzanga mwa Khristu Yesu. 4Iwo anapereka miyoyo yawo chifukwa cha ine. Osati ine ndekha komanso mipingo yonse ya a mitundu ina ikuyamika.

5Perekaninso moni kwa mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo.

Perekani moni kwa mʼbale wanga wokondedwa Epeneto, amene ndi woyamba kukhulupirira Khristu mʼchigawo cha Asiya.

6Perekani moni kwa Mariya, amene wakhala akukugwirirani ntchito kwambiri.

7Perekani moni kwa Androniko ndi Yuniya abale anga amene anali mʼndende pamodzi ndi ine. Iwo amadziwika ndi atumwi, ndipo iwo anali mwa Khristu ine ndisanakhale.

8Perekani moni kwa Ampliato, amene ine ndimamukonda mwa Ambuye.

9Perekani moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu mwa Khristu ndi wokondedwa wanga Staku.

10Perekani moni kwa Apele, woyesedwa ndi wovomerezeka mwa Khristu.

Perekani moni kwa a mʼbanja la Aristobulo.

11Perekani moni kwa Herodiona, mʼbale wanga.

Perekani moni kwa a mʼbanja la Narkiso amene ali mwa Ambuye.

12Perekani moni kwa Trufena ndi Trufosa, amayi aja amene amagwira ntchito ya Ambuye molimbika.

Perekani moni kwa mnzanga wokondedwa Persida, mayi winanso amene wagwira ntchito kwambiri mwa Ambuye.

13Perekani moni kwa Rufo, wosankhidwa mwa Ambuye, ndi amayi ake, amene akhala amayi anganso.

14Perekani moni kwa Asunkrito, Felego, Herima, Patroba, Herima ndi abale amene ali nawo pamodzi.

15Perekani moni kwa Filologo, Yuliya, Neriya ndi mlongo wake, ndi Olumpa ndi oyera mtima onse amene ali nawo pamodzi.

16Mupatsane moni wina ndi mnzake mwachikondi choona.

Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.

17Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo. 18Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa. 19Aliyense anamva za kumvera kwanu, choncho ndine odzaza ndi chimwemwe chifukwa cha inu. Koma ine ndikufuna kuti inu mukhale anzeru pa zabwino, ndi wopanda cholakwa pa zimene zili zoyipa.

20Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana msanga pansi pa mapazi anu.

Chisomo cha Ambuye athu Yesu chikhale ndi inu.

21Timoteyo, mtumiki mnzanga, akupereka moni. Nawonso, Lusio, Yasoni ndi Sosipatro, abale anga akutero.

22Ine Tertio, amene ndalemba kalatayi, ndi kupereka moni mwa Ambuye.

23Gayo, amene chifukwa cha chisamaliro chake, ine ndi mpingo wonse kuno tikusangalala, akupereka moni.

Erasto, amene ndi msungichuma wa mzinda wonse ndiponso mʼbale wathu Kwato, akupereka moni.

24Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.

25Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali, 26koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye, 27kwa Mulungu yekhayo wanzeru kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu! Ameni.