约书亚记 21 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

约书亚记 21:1-45

分给利未人的城邑

1-2利未人的众族长到迦南示罗见祭司以利亚撒的儿子约书亚以色列各支派的首领,说:“耶和华借着摩西曾吩咐你们把一些城邑分给我们住,让我们可以在城郊牧养牲畜。” 3以色列人便按照耶和华的吩咐,从他们的产业中把以下的城邑及城郊分给了利未人。

4利未哥辖宗族中大祭司亚伦的子孙从犹大西缅便雅悯支派的产业中抽签得了十三座城。 5哥辖宗族中其他的人也从以法莲玛拿西半个支派的产业中抽签得了十座城。 6革顺的子孙从以萨迦亚设拿弗他利和在巴珊玛拿西半个支派的产业中抽签得了十三座城。 7米拉利的子孙按宗族从吕便迦得西布伦支派的产业中抽签得了十二座城。

8以色列人照耶和华对摩西的吩咐,把这些城邑及其草场用抽签的方式分给利未人。

9-10利未支派哥辖宗族中亚伦的子孙得到第一签,以下是从犹大西缅两支派的产业中抽出来分给他们的土地: 11犹大山区的基列·亚巴及其草场,亚巴原是亚衲人的祖先,基列·亚巴就是希伯仑12而城周围的田地和乡村已经分给耶孚尼的儿子迦勒作产业。

13以色列人把避难城希伯仑分给祭司亚伦的子孙,并把立拿14雅提珥以实提莫15何仑底璧16亚因淤他伯·示麦共九座城及其草场分给了他们。这都是从犹大西缅两支派分出来的。 17便雅悯支派的产业中分给他们的城有:基遍迦巴18亚拿突亚勒们四座城及其草场。 19亚伦的子孙中做祭司的共分到十三座城邑及其草场。

20利未哥辖宗族其他的子孙从以法莲支派的产业中分到的城邑有: 21以法莲山区的避难城示剑基色22基伯先伯·和仑共四座城及其草场。 23支派的产业中分给他们的城邑有:伊利提基基比顿24亚雅仑迦特·临门四座城及其草场。 25他们从玛拿西半个支派的产业中分到他纳迦特·临门两座城及其草场。 26以上是哥辖其他的子孙所分到的十座城及其草场。

27以色列人分给利未支派中革顺子孙的城邑有:玛拿西半个支派中巴珊哥兰避难城和比·施提拉及其草场,共两座城; 28以萨迦支派的基善大比拉29耶末隐·干宁四座城及其草场; 30亚设支派的米沙勒押顿31黑甲利合四座城及其草场; 32拿弗他利支派的哈末·多珥加珥坦加利利的避难城基低斯三座城及其草场。 33革顺人按宗族共分到十三座城邑及其草场。 34其余的利未人,就是米拉利的子孙所分到的城邑有:西布伦支派的约念加珥他35丁拿拿哈拉四座城及其草场; 36吕便支派的比悉雅杂37基底莫米法押四座城及其草场; 38迦得支派的玛哈念基列的避难城拉末39希实本雅谢四座城及其草场。 40利未人中米拉利的子孙按宗族所分到的城邑共有十二座。

41利未人从以色列各支派共分到四十八座城及其草场, 42这些城周围都有草场,城城如此。

43这样,耶和华把从前起誓赐给以色列人祖先的整个地区都赐给了以色列人,以色列人都分到土地,住了下来。 44耶和华照着给他们祖先的应许,使他们四境安宁,没有仇敌能抵挡他们。耶和华将所有仇敌都交在了他们手中。 45耶和华给以色列人的美好应许没有一句落空,全部实现了。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 21:1-45

Mizinda ya Alevi

1Tsono atsogoleri a mabanja a fuko la Levi anabwera kwa wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraeli, 2ku Silo mʼdziko la Kanaani ndipo anati, “Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti atipatse mizinda kuti tikhalemo, pamodzi ndi malo odyetseramo ziweto zathu.” 3Choncho, Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizinda iyi pamodzi ndi malo owetera ziweto zawo kuchokera ku madera awo, monga Yehova analamulira:

4Maere oyamba anagwera mabanja a Kohati, Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aaroni anapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini. 5Ndipo mabanja otsala a Kohati anapatsidwa mizinda khumi kuchokera ku mafuko a Efereimu, Dani ndi theka la fuko la Manase.

6Zidzukulu za Geresoni zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mabanja a mafuko a Isakara, Aseri, Nafutali ndi theka la fuko la Manase ku Basani.

7Mabanja a Merari anapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.

8Choncho Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizindayi pamodzi ndi malo odyetserako ziweto pogwiritsa ntchito maere, monga Yehova analamula kudzera mwa Mose.

9Awa ndi mayina a mizinda ya mafuko a Yuda ndi Simeoni imene inaperekedwa kwa zidzukulu za Aaroni, 10ku banja la Kohati amene anali Alevi. Paja maere oyamba anagwera mabanja a Kohati kuti alandira mizinda.

11Anapatsidwa mzinda wa Kiriati Ariba. (Paja Ariba ndiye kholo la Anaaki). Dzina lina la mzindawu ndi Hebroni, ndipo unali mʼdziko la mapiri la Yuda. Pamodzi ndi mzindawu anapatsidwanso mabusa ake onse ozungulira. 12Komabe minda ndi midzi yozungulira mizindayi inali itaperekedwa kale kwa Kalebe, mwana wa Yefune kuti ikhale cholowa chake.

13Choncho zidzukulu za Aaroni wansembe, zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu), Libina, 14Yatiri, Esitemowa, 15Holoni, Debri, 16Aini, Yuta, ndi Beti-Semesi pamodzi ndi mabusa odyetseramo ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda isanu ndi inayi yochokera ku mafuko awiriwa.

17Fuko la Benjamini linapereka Gibiyoni, Geba, 18Anatoti ndi Alimoni, pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.

19Choncho mizinda 13 pamodzi ndi malo odyetsera ziweto anapatsidwa kwa ansembe, zidzukulu za Aaroni.

20Mabanja ena otsalira a Kohati a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iyi kuchokera ku fuko la Efereimu:

21Mizinda ya Sekemu ndi Gezeri ndiye inali mizinda wopulumukirako munthu aliyense wopha mnzake mwangozi. Mizindayi inali ku mapiri a Efereimu. 22Analandiranso mizinda ya Gezeri, Kibuzaimu, Beti-Horoni pamodzi ndi malo odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.

23Fuko la Dani linapereka mizinda ya Eliteke, Gibetoni, 24Ayaloni, Gati-Rimoni pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.

25Kuchokera ku theka la fuko la Manase analandira Taanaki ndi Gati-Rimoni pamodzi ndi malo awo owetera ziweto, mizinda iwiri.

26Mizinda khumi yonseyi pamodzi ndi malo odyetsera ziweto, zinapatsidwa ku mabanja ena onse a Akohati.

27Mabanja a Ageresoni a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iwiri

kuchokera ku theka la Manase wa kummawa,

Golani ku Basani (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu mwangozi) ndi Beesitera, pamodzi ndi malo awo odyetserako ziweto.

28Fuko la Isakara linapereka mizinda ya

Kisoni, Daberati, 29Yarimuti ndi Eni Ganimu, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.

30Fuko la Aseri linapereka mizinda ya

Misali, Abidoni, 31Helikati ndi Rehobu pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.

32Fuko la Nafutali linapereka mizinda ya

Kedesi wa ku Galileya, mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi. Analandiranso mizinda ya Hamoti-Dori ndi Karitani. Kuphatikizira apa, analandira malo odyetsera ziweto a mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.

33Mabanja onse a Ageresoni analandira mizinda 13 pamodzi ndi malo awo odyetsera a ziweto.

34Mabanja a Merari amene anali otsala a fuko la Levi, anapatsidwa

mizinda iyi kuchokera ku fuko la Zebuloni:

Yokineamu, Karita, 35Dimuna ndi Nahalali, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.

36Kuchokera ku fuko la Rubeni analandira

Bezeri, Yahaza, 37Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi.

38Kuchokera ku fuko la Gadi

analandira mzinda wa Ramoti ku Giliyadi. Mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi. 39Analandiranso mizinda ya Mahanaimu, Hesiboni, Yazeri pamodzi ndi malo odyetserako ziweto ozungulira mizinda yonseyi. Yonse pamodzi inali mizindayi anayi.

40Choncho mabanja onse a Merari, amene anali otsala a fuko la Levi analandira mizinda khumi ndi iwiri pogwiritsa ntchito maere.

41Motero mizinda 48 ya mʼdziko limene Aisraeli analanda inapatsidwa kwa Alevi, kuphatikizapo malo ake odyetsera ziweto. 42Iliyonse mwa mizindayi inali ndi malo owetera ziweto oyizungulira.

43Motero Yehova anapereka kwa Israeli dziko limene analumbira kulipereka kwa makolo awo. Atalilandira anadzakhalamo. 44Yehova anawapatsa mtendere mʼdziko lonse monga momwe analonjezera makolo awo. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa adani awo amene anatha kuwagonjetsa chifukwa Yehova anapereka adani awo onse mʼmanja mwawo. 45Yehova anakwaniritsa zonse zimene analonjeza kwa Aisraeli.