撒迦利亚书 4 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒迦利亚书 4:1-14

金灯台和橄榄树

1那位与我说话的天使又来唤醒我,像唤醒睡觉的人一样。 2他问我:“你看见了什么?”

我说:“我看见一个纯金的灯台,上面有一个油碗,灯台上有七盏灯,每盏灯有七个灯芯。 3灯台旁边有两棵橄榄树,左右各一棵。” 4我问与我说话的天使:“主啊,这是什么意思?” 5他说:“你不知道吗?”我说:“主啊,我不知道。”

6他对我说:“这是耶和华对所罗巴伯讲的话。万军之耶和华说,‘不靠权势,不靠才能,乃靠我的灵。 7大山啊,你算什么?你必在所罗巴伯面前化为平地。他必搬出那块封殿顶的石头,伴随着欢呼声——愿恩典、恩典归于这殿!’”

8耶和华的话又传给了我,说: 9所罗巴伯的手奠立这殿的根基,他的手也必完成这项工程。那时你便知道是万军之耶和华差遣我到你们这里来的。 10谁敢藐视这微不足道的日子?人们看见所罗巴伯手中拿着线锤时,就必欢喜。

“这七盏灯是耶和华遍察天下的眼睛。”

11我又问天使:“灯台左右的两棵橄榄树是什么意思?” 12然后我又问道:“流出橄榄油的两个金管旁边的两根橄榄枝是什么意思?” 13他说:“你不知道吗?”我说:“主啊,我不知道。” 14他说:“这是侍立在天下之主旁边的两位受膏者。”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 4:1-14

Choyikapo Nyale cha Golide ndi Mitengo Iwiri ya Olivi

1Kenaka mngelo amene amayankhula nane anabwerera nandidzutsa, ngati mmene amadzutsira munthu amene ali mʼtulo. 2Anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?”

Ndinayankha kuti, “Ine ndikuona choyikapo nyale, chonse chagolide ndi mbale pamwamba pake ndi nyale zoyaka zisanu ndi ziwiri, iliyonse ili ndi zibowo zisanu ndi ziwiri zolowetsera zingwe zoyatsira. 3Ndiponso pambali pake pali mitengo ya olivi iwiri, umodzi uli kumanja kwa mbaleyo ndipo winawo kumanzere.”

4Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi nʼchiyani mbuye wanga?”

5Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?”

Ndinayankha kuti, “Ayi mbuye wanga.”

6Choncho iye anandiwuza kuti, “Mawu a Yehova kwa Zerubabeli ndi awa: ‘Osati mwa nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi Mzimu wanga,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.

7“Kodi ndiwe yani, iwe phiri lamphamvu? Pamaso pa Zerubabeli udzasanduka dziko losalala. Pamenepo adzabweretsa mwala wotsiriza. Akamadzawuyika pamwamba anthu adzafuwula kuti, ‘Mulungu adalitse Nyumbayi! Mulungu adalitse Nyumbayi!’ ”

8Ndipo Yehova anayankhulanso nane kuti, 9“Manja a Zerubabeli ndiwo ayika maziko a Nyumbayi; adzatsiriza ndi manja ake omwewo. Pamenepo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse ndiye anakutuma.

10“Ndani wanyoza tsiku la zinthu zazingʼono? Anthu adzasangalala akadzaona chingwe choyezera mʼmanja mwa Zerubabeli.

(“Nyale zisanu ndi ziwirizi ndi maso a Yehova, amene amayangʼanayangʼana pa dziko lapansi.”)

11Kenaka ndinafunsa mngelo uja kuti, “Kodi mitengo ya olivi iwiri ili kumanja ndi kumanzere kwa choyikapo nyalechi ikutanthauza chiyani?”

12Ndinamufunsanso kuti, “Kodi nthambi ziwiri za mtengo wa olivi zomwe zili pambali pa mipopi yodzera mafuta iwiri yagolide zikutanthauza chiyani?”

13Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?”

Ine ndinati, “Ayi mbuye wanga.”

14Choncho iye anati, “Amenewa ndi anthu awiri amene adzozedwa kuti atumikire Ambuye pa dziko lonse lapansi.”