希伯来书 5 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

希伯来书 5:1-14

1从人间选出来的大祭司,都是受委任代表人办理与上帝有关的事,为人的罪向上帝献上礼物和赎罪祭。 2他能体谅那些无知和迷失的人,因为他自己也有人性的软弱。 3所以,他不但要为众人的罪献祭,也要为自己的罪献祭。 4没有人能自取这大祭司的尊荣,只有像亚伦一样蒙上帝呼召的人才可以做大祭司。

5同样,基督也没有自取荣耀做大祭司,是上帝对祂说:

“你是我的儿子,

我今日成为你父亲。”

6在圣经的另一处,上帝又说:

“你照麦基洗德的模式永远做祭司。”

7基督在世为人的时候,曾经声泪俱下地祈求能救祂脱离死亡的上帝。祂因为敬虔而蒙了应允。 8基督虽然是上帝的儿子,仍然从所受的苦难中学习了顺服。 9祂既然达到了纯全的地步,就成了永恒救恩的源头,使所有顺服祂的人都得到拯救。 10上帝照着麦基洗德的模式立祂做大祭司。

信徒要长进

11关于这方面的事,我们还有很多话要说,但因为你们已经听不进去,很难向你们解释。 12按你们学习的时间来算,你们本该做别人的老师了,可惜你们还需要别人向你们传授上帝话语的基本道理,成了不能吃干粮、只能吃奶的人。 13因为只能吃奶的人还是婴孩,不熟习仁义的道理。 14干粮是给成年人吃的,他们的心思历经锻炼,能够分辨善恶。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ahebri 5:1-14

1Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ndipo amayikidwa kuti aziwayimirira pamaso pa Mulungu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo. 2Popeza kuti iye mwini ali ndi zofowoka zake, amatha kuwalezera mtima amene ali osadziwa ndi osochera. 3Chifukwa cha ichi, iye amadziperekera nsembe chifukwa cha machimo ake omwe ndiponso chifukwa cha machimo a anthu ena.

4Palibe amene amadzipatsa yekha ulemu wotere, koma amachita kuyitanidwa ndi Mulungu monga momwe anayitanidwira Aaroni. 5Nʼchifukwa chake Khristu sanadzipatse yekha ulemu wokhala Mkulu wa ansembe. Koma Mulungu anamuwuza kuti,

“Iwe ndiwe Mwana wanga;

Ine lero ndakhala Atate ako.”

6Ndipo penanso anati,

“Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya,

monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”

7Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka. 8Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa. 9Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye. 10Ndipo Mulungu anamuyika kukhala Mkulu wa ansembe, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.

Awachenjeza kuti Asataye Chikhulupiriro

11Tili ndi zambiri zoti tinganene pa zimenezi, koma ndi zovuta kukufotokozerani chifukwa ndinu ochedwa kuphunzira. 12Ngakhale kuti pa nthawi ino munayenera kukhala aphunzitsi, pakufunikabe munthu wina kuti abwerezenso kudzakuphunzitsani maphunziro oyambira a choonadi cha Mulungu. Ndinu ofunika mkaka osati chakudya cholimba! 13Aliyense amene amangodya mkaka okha, akanali mwana wakhanda, sakudziwa bwino chiphunzitso cha chilungamo. 14Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima msinkhu, amene pogwiritsa ntchito nzeru zawo, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choyipa.