列王纪下 20 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

列王纪下 20:1-21

希西迦的病危与康复

1那些天,希西迦病危,亚摩斯的儿子以赛亚先知前来对他说:“耶和华说,‘你要交待后事,因为你要死了,你的病不能康复。’” 2希西迦把脸转向墙,向耶和华祷告,说: 3“耶和华啊,求你顾念我怎样全心、忠诚地事奉你,做你视为善的事。”希西迦痛哭起来。 4当时,以赛亚还没有走出中院,耶和华对他说: 5“回去告诉我子民的首领希西迦,‘你祖先大卫的上帝耶和华说,我已听见你的祷告,看见了你的眼泪。我要医治你,三天后你就可以上耶和华的殿。 6我要使你的寿命增加十五年,我要从亚述王手中拯救你和这城。为我自己和我仆人大卫的缘故,我要保护这城。’”

7以赛亚说:“拿一块无花果饼贴在王的疮上,他就会痊愈。”

8希西迦以赛亚:“有什么兆头证明耶和华要医治我,三天后我可以上耶和华的殿呢?” 9以赛亚说:“耶和华要给你一个兆头,证明祂言出必行。你要日影前进十度还是后退十度呢?” 10希西迦说:“日影前进十度容易,让日影后退十度吧。” 11以赛亚先知向耶和华祈求,耶和华就使亚哈斯日晷上的日影后退了十度。

巴比伦的使者来访

12那时,巴拉但的儿子巴比伦米罗达·巴拉但听说希西迦病了,便派人送去书信和礼物。 13希西迦接见使者,让他们观看国库里的金银、香料、珍贵膏油、所有兵器和一切宝物。希西迦把宫中及国内的一切都给他们看。

14以赛亚先知来见希西迦王,问他:“这些人说了些什么?他们从哪里来?”希西迦答道:“他们来自遥远的巴比伦。” 15以赛亚问:“他们在你宫里看到了什么?”希西迦答道:“他们看到了我宫中的一切。我把国库里的一切都给他们看了。”

16以赛亚希西迦说:“你听着,耶和华说, 17‘终有一天,你宫中的一切和你祖先积攒到现在的一切,必一件不留地被掳到巴比伦。这是耶和华说的。 18你的子孙当中必有人被掳去,在巴比伦王的宫中做太监。’” 19希西迦以赛亚说:“耶和华借你说的话很好。”因为他想:“至少我有生之年将平安稳妥。”

20希西迦其他的事迹和成就,包括怎样建造水池和挖沟引水入城,都记在犹大的列王史上。 21希西迦与祖先同眠后,他儿子玛拿西继位。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 20:1-21

Kudwala kwa Hezekiya

1Masiku amenewo Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti: Konza nyumba yako chifukwa umwalira ndipo suchira.”

2Hezekiya anatembenuka nayangʼana ku khoma ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, 3“Inu Yehova, kumbukirani ndithu mmene ndayendera mokhulupirika ndi mtima wonse ndipo ndachita zolungama pamaso panu.” Hezekiya analira kwambiri.

4Yesaya asanatuluke mʼbwalo lapakati, Yehova anayankhula kuti, 5“Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova. 6Ndidzawonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzinda umenewu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya. Ndidzateteza mzinda umenewu chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”

7Pamenepo Yesaya anati, “Konzani phala lankhuyu.” Iwo anakonza phalalo nalipaka pa chithupsacho ndipo Hezekiya anachira.

8Tsono Hezekiya anafunsa Yesaya kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Yehova adzandichiritsa ndi kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu kuchokera lero lino?”

9Yesaya anayankha kuti, “Chizindikiro cha Yehova chosonyeza kuti Iye adzachita chimene walonjeza ndi ichi: Kodi chithunzithunzi chipite patsogolo kapena chibwerere pambuyo makwerero khumi?”

10Hezekiya anati, “Nʼchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, kulekana nʼkuti chithunzithunzicho chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi.”

11Pamenepo mneneri Yesaya anapemphera kwa Yehova ndipo Yehova anachititsa kuti chithunzithunzi chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi pa makwerero amene mfumu Ahazi anamanga.

Akazembe Ochokera ku Babuloni

12Pa nthawi imeneyo Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babuloni anatumiza amithenga kwa Hezekiya kukapereka makalata ndi mphatso, chifukwa nʼkuti atamva za kudwala kwa Hezekiyayo. 13Hezekiya analandira amithengawo ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Anawaonetsa siliva, golide, zonunkhiritsa zakudya ndi mafuta abwino kwambiri, zida zake zankhondo ndiponso china chilichonse chimene chinali mosungiramo zinthu zake. Panalibe chinthu mʼnyumba yake yaufumu kapena mu ufumu wake wonse chimene Hezekiya sanawaonetse.

14Tsono mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani zotani ndipo anachokera kuti?”

Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”

15Mneneriyo anafunsa kuti, “Kodi anaona chiyani mʼnyumba yanu yaufumu?”

Hezekiya anayankha kuti, “Anaona china chilichonse mʼnyumba yanga yaufumu ndipo palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindinawaonetse mʼnyumba zanga zosungiramo chuma.”

16Pamenepo Yesaya anawuza Hezekiya kuti, “Imvani zimene Yehova akunena: 17Taonani, masiku akubwera ndithu pamene zonse za mʼnyumba yanu yaufumu, zonse zimene makolo anu anazisunga mpaka lero, zidzatengedwa kupita ku Babuloni. Palibe chimene chidzatsale, akutero Yehova. 18Ndipo ena mwa ana anu omwe, amene mudzabereke adzatengedwa ndipo adzawasandutsa anthu ofulidwa mʼnyumba yaufumu ya mfumu ya Babuloni.”

19Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhulawa ndi abwino. Pakuti iye ankaganiza kuti, ‘Kodi pa nthawi yanga sipadzakhala mtendere ndi bata?’ ”

20Ntchito zina za Hezekiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 21Hezekiya anamwalira nagona pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.