列王纪下 10 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

列王纪下 10:1-36

耶户铲除亚哈家

1亚哈撒玛利亚有七十个子孙。耶户写信给那里的首领、长老以及亚哈子孙的监护人,说: 2“既然你们主人的子孙和你们在一起,你们也拥有车马、坚城和兵器,你们接到这封信后, 3就可以从你们主人的子孙中选立一个最好的继承王位,为你们主人家而战。” 4他们都十分害怕,彼此商议说:“两位王都不能抵挡他,我们怎能抵挡呢?” 5宫廷总管、总督、长老和众监护人便派人送信给耶户,说:“我们是你的仆人,你怎样吩咐,我们就怎样做。我们不会立任何人为王,你认为怎样好,就怎样办吧。”

6耶户又写了一封信,说:“如果你们归顺我,愿意听从我,明天这个时候,带着你们主人子孙的首级来耶斯列见我。”当时亚哈的七十个子孙都养在城中显贵的府中。 7这些显贵们接到信后,便杀了亚哈的七十个子孙,把他们的首级放在篮子里,送到耶斯列耶户那里。 8使者告诉耶户:“他们将王众子孙的首级送来了。”耶户下令:“把首级分成两堆,放在城门口,一直放到明天早上。” 9第二天早晨,耶户出去站在城门口,对众人说:“你们都没有罪,是我背叛我主人,把他杀了。可是,是谁杀了这些人呢? 10由此可知,耶和华对亚哈家的预言一句也没有落空。耶和华借祂仆人以利亚所说的一切都应验了。” 11耶户杀了亚哈家留在耶斯列的亲属、大臣、朋友和祭司,一个不留。

12耶户动身去撒玛利亚,经过牧人剪羊毛的地方时, 13遇见犹大亚哈谢的亲属,就问:“你们是谁?”他们答道:“我们是亚哈谢的亲属,现在去问候王和太后一家。” 14耶户下令活捉他们,他的手下便捉住他们,在剪羊毛处的井旁全部杀掉,共四十二人,一个不留。

15耶户继续前行,遇见前来迎接他的利甲的儿子约拿达耶户问候他,并说:“我对你忠诚,你对我也一样忠诚吗?”约拿达答道:“当然!”耶户说:“既然如此,把手伸给我。”他伸出手来,耶户把他拉上车, 16说:“跟我来,看我怎样热心为耶和华工作。”于是耶户让他坐在车上。 17到了撒玛利亚,他把亚哈家在撒玛利亚剩下的人全部杀光,一个不留,应验了耶和华对以利亚说的话。

耶户计杀拜巴力之人

18耶户召集了所有的人,对他们说:“亚哈供奉巴力还不够热心,我耶户要更热心地供奉他。 19我要向巴力献大祭,你们去把巴力的先知和祭司及所有拜巴力的人一个不漏地召来。凡不来的人休想活命。”耶户这样做,是想用计杀尽拜巴力的人。 20耶户下令召开祭拜巴力的庄严聚会,于是他们发出通告。 21耶户派人送信到以色列各地,凡拜巴力的人全都来了,没有一个缺席。他们把整个巴力庙塞得满满的。 22耶户吩咐掌管礼服的人拿出礼服给他们穿上, 23然后他和利甲的儿子约拿达进庙向他们宣布说:“你们仔细察看,这里不可有事奉耶和华的人,只允许拜巴力的人在这里。” 24耶户约拿达在庙里献上祭物和燔祭。此前,他预先派了八十人在庙外守着,并下令:“我把这些人交在你们手中,谁放走一个,谁就要以命抵偿。” 25耶户献完燔祭出来,便命令卫兵和将领说:“进去杀死他们,不要放走一人。”卫兵和将领进庙挥刀杀了他们,把尸首抛出去后,走入庙的内殿, 26巴力神柱搬出去烧了。 27他们摧毁了巴力的神柱和庙,把庙当作厕所,至今未变。

28这样,耶户以色列扫除了巴力29可是,他重蹈尼八的儿子耶罗波安的覆辙,拜伯特利两地的金牛犊,使以色列人陷入罪中。 30耶和华对耶户说:“你已经做了我视为正的事,照我的意思除掉了亚哈一家,因此你的子孙必做以色列王,直到第四代。” 31耶户没有全心全意地遵守以色列的上帝耶和华的律法,却重蹈耶罗波安的覆辙,使以色列人陷入罪中。

耶户去世

32那时,耶和华开始削减以色列的领土。哈薛攻打以色列各处, 33侵占了约旦河以东的土地,包括基列全境,即迦得人、吕便人和玛拿西人住的地方,从亚嫩谷附近的亚罗珥起,直到基列巴珊34耶户其他的事及其一切所作所为和成就都记在以色列的列王史上。 35他与祖先同眠后葬在撒玛利亚,他儿子约哈斯继位。 36耶户撒玛利亚统治以色列二十八年。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 10:1-36

Kuphedwa kwa Banja la Ahabu

1Tsono Ahabu anali ndi ana aamuna 70 a ku Samariya. Ndipo Yehu analemba makalata nawatumiza ku Samariya kwa atsogoleri a mu mzinda wa Yezireeli, kwa akuluakulu ndiponso kwa amene ankalera ana a Ahabu, nati, 2“Inu mukangolandira kalatayi, popeza ana a mbuye wanu ali ndi inu ndiponso muli ndi magaleta ndi akavalo, mzinda wotetezedwa ndi zida zankhondo, 3sankhani mwana wa mbuye wanu amene ndi wooneka bwino ndiponso woyenera, mulowetseni ufumu wa abambo ake. Kenaka muchite nkhondo kuteteza nyumba ya mbuye wanu.”

4Koma anthuwo anachita mantha kwambiri ndipo anati, “Taonani, mafumu awiri sanathe kulimbana naye, nanga ife tingathe bwanji?”

5Choncho woyangʼanira nyumba ya mfumu, bwanamkubwa wa mzinda, akuluakulu ena ndiponso olera anawo anatumiza uthenga uwu kwa Yehu: “Ife ndife atumiki anu ndipo tidzachita chilichonse chomwe mutiwuze. Sitidzasankha munthu wina aliyense kukhala mfumu ndipo chitani chimene mukuganiza kuti nʼchabwino kwa inu.”

6Ndipo Yehu anawalembera kalata yachiwiri yonena kuti, “Ngati inu muli mbali yanga ndi kuti mudzandimvera, mudule mitu ya ana a mbuye wanu ndipo mubwere nayo kwa ine ku Yezireeli mawa nthawi ngati yomwe ino.”

Tsono ana a mfumu onse 70 anali pamodzi ndi akuluakulu a mu mzindamo, amene ankawalera. 7Kalatayo itafika, anthuwo anatenga ana a mfumu 70 aja ndi kuwapha onse. Anayika mitu yawo mʼmadengu ndi kuyitumiza ku Yezireeli kwa Yehu. 8Mthenga uja atafika, anamuwuza Yehu kuti, “Abweretsa mitu ya ana a mfumu.”

Ndipo Yehu analamula kuti, “Unjikani mituyo mʼmilu iwiri pa chipata cha mzinda ndipo ikhale pamenepo mpaka mmawa.”

9Mmawa mwake Yehu anatuluka. Iye anayimirira pamaso pa anthu onse ndipo anati, “Inu ndinu osalakwa. Ndine amene ndinachita chiwembu mbuye wanu ndi kumupha, koma kodi wapha anthu onsewa ndani? 10Koma dziwani tsono, kuti mawu amene Yehova anayankhula kunena za banja la Ahabu sadzapita padera. Yehova wachita chimene analonjeza kudzera mwa mtumiki wake Eliya.” 11Choncho Yehu anapha onse amene anatsala a mʼbanja la Ahabu ku Yezireeli, pamodzinso ndi akuluakulu ake onse, abwenzi ake ndiponso ansembe ake, sanasiyeko ndi mmodzi yemwe wamoyo.

12Kenaka Yehu ananyamuka kupita ku Samariya. Atafika pa malo otchedwa Beti-Ekedi wa abusa, 13Yehu anakumana ndi abale ena a Ahaziya mfumu ya Yuda nawafunsa kuti, “Kodi ndinu yani?”

Iwo anayankha kuti, “Ndife abale ake a Ahaziya, ndipo tabwera kulonjera banja la mfumu ndi ana a mfumukazi.”

14Yehu analamula kuti, “Atengeni amoyo!” Choncho anawatenga amoyo ndipo anakawaphera ku chitsime cha ku malo otchedwa Beti-Ekedi wa abusa; anthu onse 42. Iye sanasiyepo ndi mmodzi yemwe wamoyo.

15Yehu atachoka kumeneko anakumana ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu, amene amabwera kudzakumana naye. Yehu anamulonjera nati kwa iye, “Kodi mtima wako uli bwino monga momwe mtima wanga ugwirizana nawo mtima wako?”

Yehonadabu anayankha kuti, “Inde ndikugwirizana nawe.”

Yehu anati, “Ngati ndi choncho, gwire dzanja.” Ndipo iye anaterodi, ndipo Yehu anamugwira dzanja namulowetsa mʼgaleta lake. 16Yehu anati, “Tiye kuno uwone mmene ndikudziperekera kwa Yehova.” Ndipo anayenda naye mʼgaleta mwake.

17Yehu atafika ku Samariya, anapha onse amene anatsala a mʼbanja la Ahabu ku Samariya; anawawonongeratu potsata mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Eliya.

Aneneri a Baala Aphedwa

18Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi nawawuza kuti, “Ahabu ankatumikira Baala pangʼono chabe; Yehu adzamutumikira kwambiri. 19Tsopano itanani aneneri a Baala onse, atumiki ake onse ndi ansembe ake onse. Pasapezeke ndi mmodzi yemwe wotsala chifukwa ine ndidzapereka nsembe yayikulu kwa Baala. Aliyense amene alephere kubwera adzaphedwa.” Koma Yehu anachita zimenezi mwachinyengo ndi cholinga choti awononge atumiki onse a Baala.

20Yehu anati, “Itanitsani msonkhano wodzalemekeza Baala.” Ndipo analengeza za msonkhanowo. 21Pamenepo Yehu anatumiza mawu ku dziko lonse la Israeli ndipo atumiki onse a Baala anabwera; palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala. Iwo anadzaza nyumba ya Baala. Nyumbayo inadzaziratu kuchokera ku khoma lina mpaka ku khoma lina. 22Ndipo Yehu anawuza munthu wosunga mikanjo kuti, “Bweretsa mikanjo yokwanira atumiki onse a Baala.” Ndipo iye anabweretsa mikanjoyo.

23Kenaka Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu analowa mʼnyumba ya Baala. Yehu anawawuza atumiki a Baala kuti, “Yangʼanitsitsani ndipo muone kuti muno musapezeke atumiki a Yehova, koma mukhale atumiki okhawo a Baala.” 24Choncho Yehu analowa kukapereka nsembe zina ndi nsembe zopsereza. Nthawi iyi nʼkuti Yehu atayika anthu 80 kunja kwa nyumbayo ndi chenjezo lakuti, “Ngati wina aliyense wa inu adzathawitsa wina aliyense wa anthu amene ndayika kuti muziwayangʼanira, munthu woteroyo adzaphedwa.”

25Yehu atangotsiriza kupereka nsembe yopsereza, analamula alonda ndi akulu a ankhondo kuti, “Lowani ndipo mukawaphe ndipo musalole kuti wina athawe.” Choncho iwo anawapha ndi lupanga. Alonda ndi akulu a ankhondo anaponya mitembo ya anthuwo panja ndipo anakalowa mʼkati mwenimweni mwa nyumba ya Baala. 26Iwo anakatulutsa mwala wopatulika umene unali mʼnyumba ya Baala ndipo anawutentha. 27Anawononga mwala wopatulika wa Baala ndi kugwetsa nyumba ya Baala, ndipo anthu anayisandutsa chimbudzi mpaka lero lino.

28Motero Yehu anawononga Baala mu Israeli. 29Koma Yehuyo sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli kupembedza mafano a golide a ana angʼombe ku Beteli ndi ku Dani.

30Yehova anati kwa Yehu, “Chifukwa wachita bwino pokwaniritsa kuchita zabwino pamaso panga ndipo wachitira banja la Ahabu zonse zimene zinali mʼmaganizo anga, zidzukulu zako zidzakhala pa mpando waufumu wa Israeli mpaka mʼbado wachinayi.” 31Komatu Yehu sanasamalire kusunga lamulo la Yehova Mulungu wa Israeli ndi mtima wake wonse. Iyeyo sanaleke machimo a Yeroboamu amene anachimwitsa nawo Israeli.

32Masiku amenewo Yehova anayamba kuchepetsa dziko la Israeli. Hazaeli anagonjetsa Aisraeli, 33kuyambira kummawa kwa Yorodani, dziko lonse la Giliyadi (chigawo cha Gadi, Rubeni ndi Manase), kuchokera ku Aroeri pafupi ndi chigwa cha Arinoni kudutsa Giliyadi mpaka ku Basani.

34Ntchito zina za Yehu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli?

35Yehu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ku Samariya. Ndipo Yehowahazi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 36Yehu analamulira Aisraeli ku Samariya zaka 28.