使徒行传 6 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

使徒行传 6:1-15

选立执事

1那时,门徒的人数与日俱增。当中有些讲希腊话的犹太人埋怨讲希伯来话的犹太人,说对方在日常分配食物的事上怠慢了他们的寡妇。 2于是,十二使徒召集所有的门徒,对他们说:“我们不应该忽略传上帝的道,去管理膳食。 3弟兄姊妹,请从你们中间选出七位声誉良好、被圣灵充满、有智慧的人来负责膳食, 4而我们要专心祈祷和传道。”

5大家一致同意,便选出充满信心、被圣灵充满的司提凡,此外还有腓利伯罗哥罗尼迦挪提门巴米拿,以及曾信过犹太教、来自安提阿的外族人尼哥拉6大家将这七个人带到使徒面前。使徒把手按在他们身上,为他们祷告。

7上帝的道兴旺起来,耶路撒冷的门徒大大增多,连许多祭司也皈信了。

司提凡被捕

8司提凡得到极大的恩典和能力,在百姓中间行了惊人的神迹奇事。 9但有些来自古利奈亚历山大基利迦亚细亚、属于“自由人6:9 自由人”指的是原为奴隶,后来获得自由的人。会堂”的犹太人联合起来与司提凡辩论。 10他们无法驳倒司提凡,因为他靠着智慧和圣灵说话。

11于是,他们暗中唆使一些人诬告司提凡说:“我们听见他说亵渎摩西和上帝的话!” 12又煽动百姓、长老和律法教师抓住司提凡,把他押到公会。 13他们还派人作伪证说:“司提凡常常讲侮辱圣地6:13 圣地”指“圣殿”。和律法的话。 14我们听见他说那个拿撒勒人耶稣要毁坏圣殿,还要摒弃摩西传给我们的规矩。” 15在场的人都盯着司提凡,只见他的容貌好像天使一样。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 6:1-15

Asankha Atumiki Asanu ndi Awiri

1Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku. 2Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya. 3Choncho abale, sankhani pakati panu anthu asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi anzeru. Ife tidzawapatsa udindo oyangʼanira. 4Koma ife tidzadzipereka kuti tizipemphera ndi kulalikira mawu.”

5Mawu amenewa anakondweretsa gulu lonse la anthu. Iwo anasankha, Stefano, munthu wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndiponso Mzimu Woyera; anasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanora, Timo, Parmena ndi Nikolao amene anatembenuka mtima ndi kulowa Chiyuda kuchokera kwa Antiokeya. 6Iwo anapereka anthuwa kwa atumwi amene anawapempherera ndi kuwasanjika manja.

7Ndipo Mawu a Mulungu anapitirira kufalikira. Chiwerengero cha ophunzira mu Yerusalemu chinakula mofulumira ndipo ansembe ochuluka anakhulupirira.

Ayuda Agwira Stefano

8Stefano, munthu wodzazidwa ndi chisomo cha Mulungu ndi mphamvu anachita zodabwitsa ndiponso zizindikiro zazikulu pakati pa anthu. 9Panauka mtsutso kuchokera kwa anthu a ku Kurene ndi a ku Alekisandriya komanso a ku dera la Silisiya ndi Asiya, otchedwa a Sunagoge ya Mfulu. Anthu amenewa anayamba kutsutsana ndi Stefano. 10Koma iwo sanathe kumugonjetsa chifukwa iye ankayankhula ndi nzeru zimene Mzimu Woyera anamupatsa.

11Iwo ananyengerera anthu ena mwamseri kuti anene kuti, “Ife tinamva Stefano akuchitira chipongwe Mose ndiponso Mulungu.”

12Motero anawutsa mitima ya anthu, akulu ndi aphunzitsi amalamulo. Anamugwira Stefano ndi kumubweretsa ku Bwalo Lalikulu. 13Iwo anabweretsa mboni zonama zimene zinati, “Munthu uyu akupitirirabe kuyankhula mawu onyoza malo oyera ndi malamulo. 14Pakuti tinamumva akunena kuti Yesu uja wa ku Nazareti adzawononga malo ano ndiponso kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”

15Onse amene anakhala pansi Mʼbwalo Lalikulu anamuyangʼanitsitsa Stefano, ndipo anaona kuti nkhope yake ikuwala ngati ya mngelo.